< Isaiah 15 >

1 The burden of Moab. Because in a night Ar of Moab was destroyed—It has been cut off, Because in a night Kir of Moab was destroyed—It has been cut off.
Uthenga wonena za Mowabu: Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha. Mzinda wa Kiri wawonongedwa, wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
2 He has gone up to Bajith and Dibon, The high places—to weep, Moab howls on Nebo and on Medeba, Baldness [is] on all its heads, every beard cut off.
Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo, akupita ku malo awo achipembedzo kukalira; anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. Mutu uliwonse wametedwa mpala, ndipo ndevu zonse zametedwa.
3 In its out-places they girded on sackcloth, On its pinnacles, and in its broad places, Everyone howls—going down with weeping.
Mʼmisewu akuvala ziguduli; pa madenga ndi mʼmabwalo aliyense akulira mofuwula, misozi ili pupupu.
4 And Heshbon and Elealeh cry, Their voice has been heard to Jahaz, Therefore the armed ones of Moab shout, His life has been grievous to him.
Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula, mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi. Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula, ndipo ataya mtima.
5 My heart [is] toward Moab, Her fugitives cry to Zoar, a heifer of the third [year], For—the ascent of Luhith—He goes up in it with weeping, For in the way of Horonaim, They wake up a cry of destruction.
Inenso ndikulirira Mowabu; chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari ndi Egilati-Selisiya akupita akulira ku chikweza cha Luhiti, Akulira mosweka mtima pa njira yopita ku Horonaimu; akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.
6 For the waters of Nimrim are desolations, For the hay has been withered, The tender grass has been finished, There has not been a green thing.
Madzi a ku Nimurimu aphwa ndipo udzu wauma; zomera zawonongeka ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala.
7 Therefore the abundance he made, and their store, They carry to the Brook of the Willows.
Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga, achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.
8 For the cry has gone around the border of Moab, Its howling [is] to Eglaim, And its howling [is] to Beer-Elim.
Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu; kulira kwawo kosweka mtima kukumveka mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.
9 For the waters of Dimon have been full of blood, For I set additions on Dimon, A lion for the escaped of Moab, And for the remnant of Adamah!
Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi, komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni, mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.

< Isaiah 15 >