< Deuteronomy 24 >

1 When a man hath taken a wife, and married her, and it come to pass, that if she find no favor in his eyes, because he hath found some scandalous thing in her, he may write her a bill of divorcement, and give it in her hand, and send her away out of his house;
Ngati mwamuna wakwatira mkazi amene sakukondwera naye chifukwa wapeza vuto pa mkaziyo, namulembera mkaziyo kalata ya chisudzulo, namupatsa ndi kumutulutsa mʼnyumba mwake,
2 And she shall depart out of his house; and if she go and become another man's wife;
mkaziyo ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina,
3 And the latter husband hate her, and write her a bill of divorcement, and give it in her hand, and send her away out of his house; or if the latter husband, who took her as his wife, should die:
ndipo mwamuna wachiwiriyo nʼkuyipidwa nayenso ndi kumulemberanso kalata ya chisudzulo nʼkumutulutsa mʼnyumba mwake, kapena ngati mwamunayo amwalira,
4 Then shall her former husband, who had sent her away, not be at liberty to take her again to be his wife, after she hath been defiled; for it is abomination before the Lord; and thou shalt not bring sin upon the land, which the Lord thy God giveth thee for an inheritance.
mwamuna wake woyamba uja, amene anamuleka saloledwanso kumukwatira kachiwiri popeza mkaziyo wadetsedwa. Chimenechi ndi chonyansa pamaso pa Yehova. Musalowetse tchimo mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu.
5 When a man hath taken a new wife, he shall not go out to war, neither shall he be charged with any public business: he shall be free for his house one year, and shall cheer up his wife whom he hath taken.
Mwamuna akangokwatira kumene asamatumizidwe ku nkhondo kapena kupatsidwa ntchito ina iliyonse. Kwa chaka chathunthu akhale ndi ufulu wokhala pa khomo pake kumasangalatsa mkazi wakeyo.
6 No man shall take to pledge the nether or the upper millstone; for he taketh a man's life to pledge.
Munthu akakhala nanu ndi ngongole musamutengere mwala wake wa mphero ngati chikole, chifukwa kutero nʼkumutengera moyo kukhala chikole cha ngongole.
7 If a man be found stealing any one of his brethren of the children of Israel, and he treateth him as a slave, and selleth him: then shall that thief die; and thou shalt put the evil away from the midst of thee.
Ngati munthu agwidwa akuba mʼbale wake wa Chiisraeli namamuzunza ngati kapolo kapena kumugulitsa, wogulitsa mnzakeyo ayenera kuphedwa. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
8 Take heed of the plague of leprosy, to observe diligently, and to do according to all that the priests, the Levites, may instruct you; as I have commanded them, so shall ye observe to do.
Pakagwa matenda a khate, samalitsani kuchita zonse zimene ansembe, amene ndi Alevi, anakulangizani. Mutsatire mosamalitsa zimene ndinawalamula.
9 Remember what the Lord thy God did unto Miriam on the journey, at your coming forth out of Egypt.
Kumbukirani zimene Yehova Mulungu wanu anachita kwa Miriamu muli paulendo mutatuluka mu Igupto.
10 When thou dost lend thy brother any thing as a loan, thou shalt not go into his house to take his pledge.
Ukabwereketsa mnzako kanthu kena kalikonse, usalowe mʼnyumba mwake kukatenga chimene wachipereka ngati chikole.
11 In the street shalt thou stand, and the man to whom thou dost lend shall bring out unto thee the pledge into the street.
Uziyima kunja kwa nyumba kuti munthu amene wamubwereketsa kanthuyo akubweretsere kunja komweko.
12 And if he be a poor man, thou shalt not lie down with his pledge:
Ngati munthuyo ndi wosauka, usamutengere chikolecho mpaka kukagona nacho kwanu.
13 Thou shalt punctually deliver him the pledge again when the sun goeth down, that he may lie under his own cover, and bless thee; and unto thee shall it be as righteousness before the Lord thy God.
Pomalowa dzuwa ukhale utamubwezera mkanjo wakewo kuti akafunde. Pamenepo adzakuthokoza, ndipo amenewa adzawerengedwa ngati machitidwe olungama kwa iweyo pamaso pa Yehova Mulungu wako.
14 Thou shalt not withhold the wages of a hired man, of the poor and needy, [whether he be] of thy brethren, or of the strangers that are in thy land within thy gates.
Osamapezera mwayi pa anthu aganyu osauka ndi aumphawi, kaya ndi Mwisraeli kapena mlendo wokhala mu umodzi mwa mizinda yanu.
15 On the same day shalt thou give him his wages, that the sun may not go down upon it; for he is poor, and his soul longeth for it; so that he may not cry against thee unto the Lord, and it be sin in thee.
Mumulipire malipiro ake a tsiku dzuwa lisanalowe chifukwa ndi wosauka ndipo akudalira malipirowo. Kupanda kutero adzakudandaulirani kwa Yehova ndipo mudzapezeka ochimwa.
16 Fathers shall not be put to death for the children, neither shall children be put to death for the fathers: for his own sin shall every man be put to death.
Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.
17 Thou shalt not pervert the cause of the stranger, or of the fatherless; and thou shalt not take in pledge the raiment of a widow;
Musachitire mlendo kapena mwana wamasiye zoyipa, kapena kulanda mkazi wamasiye chovala ngati chikole cha ngongole.
18 But thou shalt remember that thou waste a bond-man in Egypt, and that the Lord thy God redeemed thee thence; therefore do I command thee to do this thing.
Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani kumeneko. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.
19 When thou cuttest down thy harvest in thy field, and forgettest a sheaf in the field, thou shalt not go back to fetch it; for the stranger, for the fatherless, and for the widow shall it be; in order that the Lord thy God may bless thee in all the work of thy hands.
Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse.
20 When thou beatest thy olive-tree, thou shalt not go over the boughs again; for the stranger, for the fatherless, and for the widow shall it be.
Mukathyola zipatso mu mtengo wa olivi, musamabwererenso kachiwiri ku mtengo womwewo. Zotsalazo zilekereni alendo, ana ndi akazi amasiye.
21 When thou gatherest the grapes of thy vineyard, thou shalt not glean the small fruit afterward; for the stranger, for the fatherless, and for the widow shall it be.
Mukakolola mphesa mʼmunda mwanu musamabwereremonso kachiwiri. Zotsalazo muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye.
22 And thou shalt remember that thou wast a bond-man in the land of Egypt; therefore do I command thee to do this thing:
Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.

< Deuteronomy 24 >