< Leviticus 22 >

1 And the LORD spake unto Moses, saying,
Yehova anawuza Mose kuti,
2 Speak unto Aaron and to his sons, that they separate themselves from the holy things of the children of Israel, and that they profane not my holy name [in those things] which they hallow unto me: I [am] the LORD.
“Uza Aaroni ndi ana ake kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraeli azipereka kwa Ine, kuti asayipitse dzina langa loyera. Ine ndine Yehova.
3 Say unto them, Whosoever [he be] of all your seed among your generations, that goeth unto the holy things, which the children of Israel hallow unto the LORD, having his uncleanness upon him, that soul shall be cut off from my presence: I [am] the LORD.
“Uwawuze kuti ngati wina aliyense mwa zidzukulu zawo mʼmibado yonse imene ikubwera adzayandikira zinthu zopatulika zimene ana a Israeli apereka kwa Yehova, ali wodetsedwa, ameneyo achotsedwe pamaso pa Yehova. Ine ndine Yehova.
4 What man soever of the seed of Aaron [is] a leper, or hath a running issue; he shall not eat of the holy things, until he be clean. And whoso toucheth any thing [that is] unclean [by] the dead, or a man whose seed goeth from him;
“Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aaroni amene ali ndi khate kapena amatulutsa zoyipa mʼthupi mwake, asadye zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Wansembe angakhale wodetsedwa atakhudzana ndi chinthu chimene chadetsedwa ndi chinthu chakufa kapena kukhudza munthu amene wataya umuna,
5 Or whosoever toucheth any creeping thing, whereby he may be made unclean, or a man of whom he may take uncleanness, whatsoever uncleanness he hath;
kapena kukhudza chilichonse chokwawa chomwe chimadetsa munthu, kapena kukhudza munthu amene angamudetse, kapenanso kukhudza kanthu kena kalikonse kodetsedwa.
6 The soul which hath touched any such shall be unclean until even, and shall not eat of the holy things, unless he wash his flesh with water.
Tsono ngati wansembe angakhudze chilichonse mwa zimenezi ndiye kuti adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Asadye chopereka chilichonse chopatulika mpaka atasamba thupi lake lonse.
7 And when the sun is down, he shall be clean, and shall afterward eat of the holy things; because it [is] his food.
Munthuyo adzakhala woyeretsedwa pamene dzuwa lalowa, ndipo angathe kudya chopereka chopatulikacho popeza ndi chakudya chake.
8 That which dieth of itself, or is torn [with beasts], he shall not eat to defile himself therewith: I [am] the LORD.
Wansembe sayenera kudya chinthu chofa chokha kapena chojiwa ndi chirombo kuopa kuti angadzidetse ndi chakudyacho. Ine ndine Yehova.
9 They shall therefore keep mine ordinance, lest they bear sin for it, and die therefore, if they profane it: I the LORD do sanctify them.
“‘Choncho ansembe azisunga malamulo angawa kuti asapezeke wolakwa ndi kufa chifukwa chopeputsa malamulowa. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.
10 There shall no stranger eat [of] the holy thing: a sojourner of the priest, or an hired servant, shall not eat [of] the holy thing.
“‘Aliyense amene si wabanja la wansembe, kaya ndi mlendo wa wansembe, kapena wantchito wake, asadye chopereka chopatulika.
11 But if the priest buy [any] soul with his money, he shall eat of it, and he that is born in his house: they shall eat of his meat.
Koma kapolo amene wagulidwa ndi ndalama kapena kubadwira mʼbanja la wansembe angathe kudya chakudya cha wansembeyo.
12 If the priest’s daughter also be [married] unto a stranger, she may not eat of an offering of the holy things.
Mwana wamkazi wa wansembe amene wakwatiwa ndi munthu amene si wansembe, asadyeko nsembe zopatulikazo.
13 But if the priest’s daughter be a widow, or divorced, and have no child, and is returned unto her father’s house, as in her youth, she shall eat of her father’s meat: but there shall no stranger eat thereof.
Koma mwana wamkazi wa wansembe amene ali wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, komanso anabwerera ku nyumba ya abambo ake monga pa nthawi ya utsikana wake, angathe kudya chakudya cha abambo ake. Mlendo asadye chakudya chopatulika.
14 And if a man eat [of] the holy thing unwittingly, then he shall put the fifth [part] thereof unto it, and shall give [it] unto the priest with the holy thing.
“‘Ngati munthu wina aliyense adya chopereka chopatulika mosadziwa, munthuyo amubwezere wansembe chinthu chopatulikacho ndipo awonjezerepo limodzi la magawo asanu a chinthucho.
15 And they shall not profane the holy things of the children of Israel, which they offer unto the LORD;
Choncho ansembe asayipitse zopereka zopatulika za Aisraeli zimene apereka kwa Yehova
16 Or suffer them to bear the iniquity of trespass, when they eat their holy things: for I the LORD do sanctify them.
ndipo asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraeli powalola kudya zakudya zawo zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndimawayeretsa.’”
17 And the LORD spake unto Moses, saying,
Yehova anawuza Mose kuti,
18 Speak unto Aaron, and to his sons, and unto all the children of Israel, and say unto them, Whatsoever [he be] of the house of Israel, or of the strangers in Israel, that will offer his oblation for all his vows, and for all his freewill offerings, which they will offer unto the LORD for a burnt offering;
“Yankhula ndi Aaroni, ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse, ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati wina aliyense wa inu, Mwisraeli kapena mlendo amene akukhala mu Israeli abwera ndi mphatso ya nsembe yopsereza kwa Yehova, kupereka chimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu,
19 [Ye shall offer] at your own will a male without blemish, of the beeves, of the sheep, or of the goats.
ndiye kuti abwere ndi ngʼombe yayimuna, nkhosa yayimuna kapena mbuzi yayimuna. Izi zikhale zopanda chilema kuti zilandiridwe.
20 [But] whatsoever hath a blemish, [that] shall ye not offer: for it shall not be acceptable for you.
Musapereke nyama iliyonse yokhala ndi chilema chifukwa sidzalandiridwa mʼmalo mwanu.
21 And whosoever offereth a sacrifice of peace offerings unto the LORD to accomplish [his] vow, or a freewill offering in beeves or sheep, it shall be perfect to be accepted; there shall be no blemish therein.
Pamene wina aliyense abweretsa ngʼombe kapena nkhosa kuti ikhale nsembe yachiyanjano kwa Yehova, kukwaniritsa zimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, nyamayo iyenera kukhala yangwiro ndi yopanda chilema kuti ilandiridwe.
22 Blind, or broken, or maimed, or having a wen, or scurvy, or scabbed, ye shall not offer these unto the LORD, nor make an offering by fire of them upon the altar unto the LORD.
Musapereke kwa Yehova nyama zakhungu, zovulala kapena zolumala, kapena nyama zimene zikutulutsa mafinya mʼthupi mwake, kapena zimene zili ndi nthenda yonyerenyetsa, kapena zimene zili ndi mphere. Nyama zotere musaziyike pa guwa kuti zikhale nsembe yopsereza kwa Yehova.
23 Either a bullock or a lamb that hath any thing superfluous or lacking in his parts, that mayest thou offer [for] a freewill offering; but for a vow it shall not be accepted.
Koma mungathe kupereka ngʼombe yayimuna kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi kukhala nsembe yaufulu. Koma simungayipereke ngati nsembe yoperekera zimene munalumbirira chifukwa sidzalandiridwa.
24 Ye shall not offer unto the LORD that which is bruised, or crushed, or broken, or cut; neither shall ye make [any offering thereof] in your land.
Nyama iliyonse imene mavalo ake ndi onyuka kapena ophwanyika, ongʼambika kapena oduka, musamayipereke kwa Yehova mʼdziko lanu.
25 Neither from a stranger’s hand shall ye offer the bread of your God of any of these; because their corruption [is] in them, [and] blemishes [be] in them: they shall not be accepted for you.
Ndipo musalandire nyama zotere kuchokera kwa mlendo ndi kuzipereka kukhala zakudya za Mulungu wanu. Zimenezi sizidzalandiridwa mʼmalo mwanu chifukwa zili ndi chilema ndipo ndi zolumala.’”
26 And the LORD spake unto Moses, saying,
Yehova anawuza Mose kuti,
27 When a bullock, or a sheep, or a goat, is brought forth, then it shall be seven days under the dam; and from the eighth day and thenceforth it shall be accepted for an offering made by fire unto the LORD.
“Pamene mwana wangʼombe, mwana wankhosa kapena mwana wambuzi wabadwa, akhale ndi make kwa masiku asanu ndi awiri. Kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka mʼtsogolo mwake, angathe kulandiridwa kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova.
28 And [whether it be] cow or ewe, ye shall not kill it and her young both in one day.
Musaphe ngʼombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzi. Muyidye pa tsiku lomwelo; musasiyeko ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova.
29 And when ye will offer a sacrifice of thanksgiving unto the LORD, offer [it] at your own will.
“Pamene mupereka nsembe yoyamika kwa Yehova, muyipereke mwakufuna kwanu mu njira yoti ilandiridwe mʼmalo mwanu.
30 On the same day it shall be eaten up; ye shall leave none of it until the morrow: I [am] the LORD.
Muyidye pa tsiku lomwelo, wosasiyako ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova.
31 Therefore shall ye keep my commandments, and do them: I [am] the LORD.
“Choncho sungani malamulo anga ndi kuwatsatira. Ine ndine Yehova.
32 Neither shall ye profane my holy name; but I will be hallowed among the children of Israel: I [am] the LORD which hallow you,
Musanyoze dzina langa loyera. Koma lilemekezedwe pakati pa Aisraeli. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani
33 That brought you out of the land of Egypt, to be your God: I [am] the LORD.
ndipo ndine amene ndinakutulutsani mu Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.”

< Leviticus 22 >