< Job 26 >
1 But Job answered and said,
Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 How hast thou helped him that is without power? how savest thou the arm that hath no strength?
“Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu! Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka!
3 How hast thou counselled him that hath no wisdom? and how hast thou plentifully declared the thing as it is?
Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru! Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!
4 To whom hast thou uttered words? and whose spirit came from thee?
Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa? Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako?
5 Dead things are formed from under the waters, and the inhabitants thereof.
“Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi, ndi zonse zokhala mʼmadzimo.
6 Hell is naked before him, and destruction hath no covering. (Sheol )
Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu; chiwonongeko ndi chosaphimbidwa. (Sheol )
7 He stretcheth out the north over the empty place, and hangeth the earth upon nothing.
Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho; Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe.
8 He bindeth up the waters in his thick clouds; and the cloud is not rent under them.
Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake, koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
9 He holdeth back the face of his throne, and spreadeth his cloud upon it.
Iye amaphimba mwezi wowala, amawuphimba ndi mitambo yake.
10 He hath compassed the waters with bounds, until the day and night come to an end.
Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta, kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima.
11 The pillars of heaven tremble and are astonished at his reproof.
Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera, ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
12 He divideth the sea with his power, and by his understanding he smiteth through the proud.
Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja; ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe.
13 By his spirit he hath garnished the heavens; his hand hath formed the crooked serpent.
Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga, dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija.
14 Lo, these are parts of his ways: but how little a portion is heard of him? but the thunder of his power who can understand?
Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake; tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona! Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”