< Psalms 84 >

1 How amiable are thy tabernacles, O YHWH of hosts!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora. Malo anu okhalamo ndi okomadi, Inu Yehova Wamphamvuzonse!
2 My soul longeth, yea, even fainteth for the courts of YHWH: my heart and my flesh crieth out for the living El.
Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufuna mabwalo a Yehova; Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira Mulungu wamoyo.
3 Yea, the sparrow hath found an house, and the swallow a nest for herself, where she may lay her young, even thine altars, O YHWH of hosts, my King, and my Elohim.
Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo, ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa, kumene amagonekako ana ake pafupi ndi guwa lanu la nsembe, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
4 Blessed are they that dwell in thy house: they will be still praising thee. (Selah)
Odala amene amakhala mʼNyumba yanu; nthawi zonse amakutamandani. (Sela)
5 Blessed is the man whose strength is in thee; in whose heart are the ways of them.
Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu, mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
6 Who passing through the valley of Baca make it a well; the rain also filleth the pools.
Pamene akudutsa chigwa cha Baka, amachisandutsa malo a akasupe; mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
7 They go from strength to strength, every one of them in Zion appeareth before Elohim.
Iwo amanka nakulirakulira mphamvu mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.
8 O YHWH Elohim of hosts, hear my prayer: give ear, O Elohim of Jacob. (Selah)
Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse; mvereni Inu Mulungu wa Yakobo. (Sela)
9 Behold, O Elohim our shield, and look upon the face of thine anointed.
Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu; yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.
10 For a day in thy courts is better than a thousand. I had rather be a doorkeeper in the house of my Elohim, than to dwell in the tents of wickedness.
Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
11 For YHWH Elohim is a sun and shield: YHWH will give favour and glory: no good thing will he withhold from them that walk uprightly.
Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.
12 O YHWH of hosts, blessed is the man that trusteth in thee.
Inu Yehova Wamphamvuzonse, wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.

< Psalms 84 >