< Proverbs 5 >

1 My son, attend unto my wisdom, and bow thine ear to my understanding:
Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi, tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,
2 That thou mayest regard discretion, and that thy lips may keep knowledge.
kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.
3 For the lips of a strange woman drop as an honeycomb, and her mouth is smoother than oil:
Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi. Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,
4 But her end is bitter as wormwood, sharp as a twoedged sword.
koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu; ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
5 Her feet go down to death; her steps take hold on hell. (Sheol h7585)
Mapazi ake amatsikira ku imfa; akamayenda ndiye kuti akupita ku manda. (Sheol h7585)
6 Lest thou shouldest ponder the path of life, her ways are moveable, that thou canst not know them.
Iye saganizirapo za njira ya moyo; njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.
7 Hear me now therefore, O ye children, and depart not from the words of my mouth.
Tsopano ana inu, mundimvere; musawasiye mawu anga.
8 Remove thy way far from her, and come not nigh the door of her house:
Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo, usayandikire khomo la nyumba yake,
9 Lest thou give thine honour unto others, and thy years unto the cruel:
kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena; ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,
10 Lest strangers be filled with thy wealth; and thy labours be in the house of a stranger;
kapenanso alendo angadyerere chuma chako ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.
11 And thou mourn at the last, when thy flesh and thy body are consumed,
Potsiriza pa moyo wako udzabuwula, thupi lako lonse litatheratu.
12 And say, How have I hated instruction, and my heart despised reproof;
Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo! Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!
13 And have not obeyed the voice of my teachers, nor inclined mine ear to them that instructed me!
Sindinamvere aphunzitsi anga kapena alangizi anga.
14 I was almost in all evil in the midst of the congregation and assembly.
Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke pakati pa msonkhano wonse.”
15 Drink waters out of thine own cistern, and running waters out of thine own well.
Imwa madzi a mʼchitsime chakochako, madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.
16 Let thy fountains be dispersed abroad, and rivers of waters in the streets.
Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu? Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?
17 Let them be only thine own, and not strangers' with thee.
Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha, osati uyigawireko alendo.
18 Let thy fountain be blessed: and rejoice with the wife of thy youth.
Yehova adalitse kasupe wako, ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.
19 Let her be as the loving hind and pleasant roe; let her breasts satisfy thee at all times; and be thou ravished always with her love.
Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino. Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse, ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
20 And why wilt thou, my son, be ravished with a strange woman, and embrace the bosom of a stranger?
Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo? Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?
21 For the ways of man are before the eyes of YHWH, and he pondereth all his goings.
Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona, ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.
22 His own iniquities shall take the wicked himself, and he shall be holden with the cords of his sins.
Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha; zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha.
23 He shall die without instruction; and in the greatness of his folly he shall go astray.
Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo, adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.

< Proverbs 5 >