< Psalms 61 >
1 Hear my cry, O God; attend to my prayer.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe. Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu; mvetserani pemphero langa.
2 From the end of the earth will I cry to you, when my heart is overwhelmed: lead me to the rock that is higher than I.
Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka; tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
3 For you have been a shelter for me, and a strong tower from the enemy.
Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga, nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.
4 I will abide in your tabernacle for ever: I will trust in the covert of your wings. (Selah)
Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.
5 For you, O God, have heard my vows: you have given me the heritage of those that fear your name.
Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga; mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.
6 You will prolong the king’s life: and his years as many generations.
Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu, zaka zake kwa mibado yochuluka.
7 He shall abide before God for ever: O prepare mercy and truth, which may preserve him.
Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya; ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.
8 So will I sing praise to your name for ever, that I may daily perform my vows.
Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.