< Isaiah 25 >
1 O LORD, Thou art my God, I will exalt Thee, I will praise Thy name, for Thou hast done wonderful things; even counsels of old, in faithfulness and truth.
Yehova ndinu Mulungu wanga; ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu, pakuti mwachita zodabwitsa zimene munakonzekeratu kalekale mokhulupirika kwambiri.
2 For Thou hast made of a city a heap, of a fortified city a ruin; a castle of strangers to be no city, it shall never be built.
Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala. Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja, linga la anthu achilendo lero si mzindanso ndipo sidzamangidwanso.
3 Therefore shall the strong people glorify Thee, the city of the terrible nations shall fear Thee.
Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani; mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.
4 For Thou hast been a stronghold to the poor, a stronghold to the needy in his distress, a refuge from the storm, a shadow from the heat; for the blast of the terrible ones was as a storm against the wall.
Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka, mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake. Mwakhala ngati pobisalirapo pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa. Pakuti anthu ankhanza ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,
5 As the heat in a dry place, Thou didst subdue the noise of strangers; as the heat by the shadow of a cloud, the song of the terrible ones was brought low.
ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma. Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo. Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha, inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.
6 And in this mountain will the LORD of hosts make unto all peoples a feast of fat things, a feast of wines on the lees, of fat things full of marrow, of wines on the lees well refined.
Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino. Phwando la nyama yonona ndi vinyo wabwino kwambiri.
7 And He will destroy in this mountain the face of the covering that is cast over all peoples, and the veil that is spread over all nations.
Iye adzachotsa kulira kumene kwaphimba anthu ngati nsalu. Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.
8 He will swallow up death for ever; and the Lord GOD will wipe away tears from off all faces; and the reproach of His people will He take away from off all the earth; for the LORD hath spoken it.
Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula.
9 And it shall be said in that day: 'Lo, this is our God, for whom we waited, that He might save us; this is the LORD, for whom we waited, we will be glad and rejoice in His salvation.'
Tsiku limenelo iwo adzati, “Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu; ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa. Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira; tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”
10 For in this mountain will the hand of the LORD rest, and Moab shall be trodden down in his place, even as straw is trodden down in the dunghill.
Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake; ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo, ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.
11 And when he shall spread forth his hands in the midst thereof, as he that swimmeth spreadeth forth his hands to swim, his pride shall be brought down together with the cunning of his hands.
Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo, ngati mmene amachitira munthu wosambira. Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo ngakhale luso la manja awo.
12 And the high fortress of thy walls will He bring down, lay low, and bring to the ground, even to the dust.
Iye adzagumula malinga awo ataliatali ndipo adzawagwetsa ndi kuwaponya pansi, pa fumbi penipeni.