< Genesis 36 >

1 Now these are the generations of Esau — the same is Edom.
Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu:
2 Esau took his wives of the daughters of Canaan; Adah the daughter of Elon the Hittite, and Oholibamah the daughter of Anah, the daughter of Zibeon the Hivite,
Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi
3 and Basemath Ishmael's daughter, sister of Nebaioth.
ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti.
4 And Adah bore to Esau Eliphaz; and Basemath bore Reuel;
Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli;
5 and Oholibamah bore Jeush, and Jalam, and Korah. These are the sons of Esau, that were born unto him in the land of Canaan.
ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani.
6 And Esau took his wives, and his sons, and his daughters, and all the souls of his house, and his cattle, and all his beasts, and all his possessions, which he had gathered in the land of Canaan; and went into a land away from his brother Jacob.
Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo.
7 For their substance was too great for them to dwell together; and the land of their sojournings could not bear them because of their cattle.
Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi.
8 And Esau dwelt in the mountain-land of Seir — Esau is Edom.
Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.
9 And these are the generations of Esau the father of a the Edomites in the mountain-land of Seir.
Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.
10 These are the names of Esau's sons: Eliphaz the son of Adah the wife of Esau, Reuel the son of Basemath the wife of Esau.
Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau: Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau.
11 And the sons of Eliphaz were Teman, Omar, Zepho, and Gatam, and Kenaz.
Awa ndi mayina a ana a Elifazi: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.
12 And Timna was concubine to Eliphaz Esau's son; and she bore to Eliphaz Amalek. These are the sons of Adah Esau's wife.
Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.
13 And these are the sons of Reuel: Nahath, and Zerah, Shammah, and Mizzah. These were the sons of Basemath Esau's wife.
Awa ndi ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau.
14 And these were the sons of Oholibamah the daughter of Anah, the daughter of Zibeon, Esau's wife; and she bore to Esau Jeush, and Jalam, and Korah.
Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa: Yeusi, Yolamu ndi Kora.
15 These are the chiefs of the sons of Esau: the sons of Eliphaz the first-born of Esau: the chief of Teman, the chief of Omar, the chief of Zepho, the chief of Kenaz,
Nawa mafumu a zidzukulu za Esau: Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa: Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi,
16 the chief of Korah, the chief of Gatam, the chief of Amalek. These are the chiefs that came of Eliphaz in the land of Edom. These are the sons of Adah.
Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada.
17 And these are the sons of Reuel Esau's son: the chief of Nahath, the chief of Zerah, the chief of Shammah, the chief of Mizzah. These are the chiefs that came of Reuel in the land of Edom. These are the sons of Basemath Esau's wife.
Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau.
18 And these are the sons of Oholibamah Esau's wife: the chief of Jeush, the chief of Jalam, the chief of Korah. These are the chiefs that came of Oholibamah the daughter of Anah, Esau's wife.
Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa: Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.
19 These are the sons of Esau, and these are their chiefs; the same is Edom.
Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo.
20 These are the sons of Seir the Horite, the inhabitants of the land: Lotan and Shobal and Zibeon and Anah,
Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,
21 and Dishon and Ezer and Dishan. These are the chiefs that came of the Horites, the children of Seir in the land of Edom.
Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori.
22 And the children of Lotan were Hori and Hemam; and Lotan's sister was Timna.
Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
23 And these are the children of Shobal: Alvan and Manahath and Ebal, Shepho and Onam.
Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
24 And these are the children of Zibeon: Aiah and Anah — this is Anah who found the hot springs in the wilderness, as he fed the asses of Zibeon his father.
Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.
25 And these are the children of Anah: Dishon and Oholibamah the daughter of Anah.
Ana a Ana anali: Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi.
26 And these are the children of Dishon: Hemdan and Eshban and Ithran and Cheran.
Ana aamuna a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.
27 These are the children of Ezer: Bilhan and Zaavan and Akan.
Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Akani.
28 These are the children of Dishan: Uz and Aran.
Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani.
29 These are the chiefs that came of the Horites: the chief of Lotan, the chief of Shobal, the chief of Zibeon, the chief of Anah,
Mafumu a Ahori anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,
30 the chief of Dishon, the chief of Ezer, the chief of Dishan. These are the chiefs that came of the Horites, according to their chiefs in the land of Seir.
Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri.
31 And these are the kings that reigned in the land of Edom, before there reigned any king over the children of Israel.
Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:
32 And Bela the son of Beor reigned in Edom; and the name of his city was Dinhabah.
Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
33 And Bela died, and Jobab the son of Zerah of Bozrah reigned in his stead.
Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
34 And Jobab died, and Husham of the land of the Temanites reigned in his stead.
Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu.
35 And Husham died, and Hadad the son of Bedad, who smote Midian in the field of Moab, reigned in his stead; and the name of his city was Avith.
Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
36 And Hadad died, and Samlah of Masrekah reigned in his stead.
Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake.
37 And Samlah died, and Shaul of Rehoboth by the River reigned in his stead.
Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake.
38 And Shaul died, and Baal-hanan the son of Achbor reigned in his stead.
Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
39 And Baal-hanan the son of Achbor died, and Hadar reigned in his stead; and the name of the city was Pau; and his wife's name was Mehetabel, the daughter of Matred, the daughter of Me-zahab.
Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
40 And these are the names of the chiefs that came of Esau, according to their families, after their places, by their names: the chief of Timna, the chief of Alvah, the chief of Jetheth;
Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa: Timna, Aliva, Yeteti,
41 the chief of Oholibamah, the chief of Elah, the chief of Pinon;
Oholibama, Ela, Pinoni,
42 the chief of Kenaz, the chief of Teman, the chief of Mibzar;
Kenazi, Temani, Mibezari,
43 the chief of Magdiel, the chief of Iram. These are the chiefs of Edom, according to their habitations in the land of their possession. This is Esau the father of the Edomites.
Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo. Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.

< Genesis 36 >