< Titus 2 >
1 Bvt speake thou the thinges which become wholesome doctrine,
Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona.
2 That the elder men be watchful, graue, teperate, sounde in the faith, in loue, and in patience:
Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.
3 The elder women likewise, that they be in such behauiour as becommeth holinesse, not false accusers, not subiect to much wine, but teachers of honest things,
Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino.
4 That they may instruct the yong women to be sober minded, that they loue their husbands, that they loue their children,
Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo.
5 That they be temperate, chaste, keeping at home, good and subiect vnto their husbands, that the word of God be not euill spoken of.
Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.
6 Exhort yong men likewise, that they bee sober minded.
Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa.
7 In all things shewe thy selfe an ensample of good woorkes with vncorrupt doctrine, with grauitie, integritie,
Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako.
8 And with the wholesome woorde, which can not be condemned, that hee which withstandeth, may be ashamed, hauing nothing concerning you to speake euill of.
Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.
9 Let seruants be subiect to their masters, and please them in al things, not answering again,
Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo
10 Neither pickers, but that they shew al good faithfulnesse, that they may adorne the doctrine of God our Sauiour in all things.
kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu.
11 For that grace of God, that bringeth saluation vnto all men, hath appeared,
Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse.
12 And teacheth vs that we should denie vngodlinesse and worldly lusts, and that we should liue soberly and righteously, and godly in this present world, (aiōn )
Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, (aiōn )
13 Looking for that blessed hope, and appearing of that glorie of that mightie God, and of our Sauiour Iesus Christ,
pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu,
14 Who gaue him selfe for vs, that hee might redeeme vs from all iniquitie, and purge vs to bee a peculiar people vnto himselfe, zealous of good woorkes.
amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
15 These things speake, and exhort, and conuince with all authoritie. See that no man despise thee.
Tsono zimenezi ndi zinthu zomwe uyenera kuphunzitsa. Uziwalimbikitsa anthu ndi kuwatsutsa komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ayi.