< Hosea 8 >
1 Set the trumpet to thy mouth: he shall come as an eagle against the House of the Lord, because they haue transgressed my couenant, and trespassed against my Lawe.
“Ika lipenga pakamwa pako. Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova chifukwa anthu aphwanya pangano langa ndiponso agalukira lamulo langa.
2 Israel shall crie vnto me, My God, we know thee.
Israeli akulirira kwa Ine kuti, ‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’
3 Israel hath cast off ye thing that is good: the enemie shall pursue him.
Koma Israeli wakana zabwino; mdani adzamuthamangitsa.
4 They haue set vp a King, but not by me: they haue made princes, and I knew it not: of their siluer and their gold haue they made them idoles: therefore shall they be destroyed.
Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amasankha akalonga popanda chilolezo changa. Amadzipangira mafano asiliva ndi agolide koma adzawonongeka nawo.
5 Thy calfe, O Samaria, hath cast thee off: mine anger is kindled against them: howe long will they be without innocencie!
Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe! Mkwiyo wanga wayakira anthuwo. Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
6 For it came euen from Israel: the workeman made it, therefore it is not God: but the calfe of Samaria shall be broken in pieces.
Mafanowa ndi ochokera ku Israeli! Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso; si Mulungu amene anamupanga. Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa, mwana wangʼombe wa ku Samariya.
7 For they haue sowne the winde, and they shall reape the whirlewind: it hath no stalke: the budde shall bring foorth no meale: if so be it bring forth, the strangers shall deuoure it.
“Aisraeli amadzala mphepo ndipo amakolola kamvuluvulu. Tirigu alibe ngala; sadzabala chakudya. Akanabala chakudya alendo akanadya chakudyacho.
8 Israel is deuoured, now shall they be among the Gentiles as a vessell wherein is no pleasure.
Israeli wamezedwa, tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina ngati chinthu cha chabechabe.
9 For they are gone vp to Asshur: they are as a wilde asse alone by himselfe: Ephraim hath hired louers.
Pakuti iwo anapita ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha. Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.
10 Yet though they haue hired among the nations, nowe will I gather them, and they shall sorowe a litle, for the burden of the King and the princes.
Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu, Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi. Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.
11 Because Ephraim hath made many altars to sinne, his altars shalbe to sinne.
“Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo, maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.
12 I haue written to them the great things of my Lawe: but they were counted as a strange thing.
Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga, koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.
13 They sacrifice flesh for ye sacrifices of mine offerings, and eate it: but the Lord accepteth them not: now will he remember their iniquitie, and visite their sinnes: they shall returne to Egypt.
Amapereka nsembe za nyama kwa Ine ndipo iwo amadya nyamayo, koma Yehova sakondwera nazo. Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo: iwowo adzabwerera ku Igupto.
14 For Israel hath forgotten his maker, and buildeth Temples, and Iudah hath increased strong cities: but I will sende a fire vpon his cities, and it shall deuoure the palaces thereof.
Israeli wayiwala Mlengi wake ndipo wamanga nyumba zaufumu; Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo, moto umene udzatenthe malinga awo.”