< Hebrews 9 >
1 Then the first Testament had also ordinances of religion, and a worldly Sanctuarie.
Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu.
2 For the first Tabernacle was made, wherein was the candlesticke, and the table, and the shewebread, which Tabernacle is called the Holy places.
Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika.
3 And after the seconde vaile was the Tabernacle, which is called the Holiest of all,
Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri.
4 Which had the golden censer, and the Arke of the Testament ouerlayde rounde about with golde, wherein the golden pot, which had Manna, was, and Aarons rod that had budded, and the tables of the Testament.
Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano.
5 And ouer the Arke were the glorious Cherubims, shadowing the mercie seat: of which things we will not nowe speake particularly.
Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.
6 Nowe when these things were thus ordeined, the Priestes went alwayes into the first Tabernacle, and accomplished the seruice.
Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo.
7 But into the second went the hie Priest alone, once euery yere, not without blood which hee offered for himselfe, and for the ignorances of the people.
Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira.
8 Whereby the holy Ghost this signified, that the way into ye Holiest of all was not yet opened, while as yet the first tabernacle was standing,
Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo.
9 Which was a figure for that present time, wherein were offred gifts and sacrifices that could not make holy, concerning the conscience, him that did the seruice,
Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo.
10 Which only stood in meates and drinkes, and diuers washings, and carnal rites, which were inioyned, vntill the time of reformation.
Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.
11 But Christ being come an high Priest of good things to come, by a greater and a more perfect Tabernacle, not made with handes, that is, not of this building,
Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano.
12 Neither by the blood of goates and calues: but by his owne blood entred he in once vnto the holy place, and obteined eternall redemption for vs. (aiōnios )
Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. (aiōnios )
13 For if the blood of bulles and of goates, and the ashes of an heifer, sprinkling them that are vncleane, sanctifieth as touching the purifying of the flesh,
Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi,
14 How much more shall the blood of Christ which through the eternall Spirit offered himselfe without fault to God, purge your conscience from dead workes, to serue the liuing God? (aiōnios )
nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo. (aiōnios )
15 And for this cause is he the Mediatour of the newe Testament, that through death which was for the redemption of the transgressions that were in the former Testament, they which were called, might receiue the promise of eternall inheritance. (aiōnios )
Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija. (aiōnios )
16 For where a Testament is, there must be the death of him that made the Testament.
Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi,
17 For the Testament is confirmed when men are dead: for it is yet of no force as long as he that made it, is aliue.
chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo.
18 Wherefore neither was the first ordeined without blood.
Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi.
19 For when Moses had spoken euery precept to the people, according to the Law, he tooke the blood of calues and of goates, with water and purple wooll and hyssope, and sprinckled both the booke, and all the people,
Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse.
20 Saying, This is the blood of the Testament, which God hath appointed vnto you.
Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.”
21 Moreouer, he sprinkled likewise the Tabernacle with blood also, and all the ministring vessels.
Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo.
22 And almost all things are by the Law purged with blood, and without sheading of blood is no remission.
Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.
23 It was then necessary, that the similitudes of heauenly things should be purified with such things: but the heauenly things them selues are purified with better sacrifices then are these.
Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo.
24 For Christ is not entred into ye holy places that are made with hands, which are similitudes of ye true Sanctuarie: but is entred into very heauen, to appeare now in ye sight of God for vs,
Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.
25 Not that he should offer himselfe often, as the hie Priest entred into the Holy place euery yeere with other blood,
Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake.
26 (For then must he haue often suffred since the foundation of the world) but now in the end of the world hath he bene made manifest, once to put away sinne by the sacrifice of him selfe. (aiōn )
Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. (aiōn )
27 And as it is appointed vnto men that they shall once die, and after that commeth the iudgement:
Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,
28 So Christ was once offered to take away the sinnes of many, and vnto them that looke for him, shall he appeare the second time without sinne vnto saluation.
momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.