< Exodus 24 >

1 Now hee had said vnto Moses, Come vp to the Lord, thou, and Aaron, Nadab, and Abihu, and seuentie of the Elders of Israel, and yee shall worship a farre off.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Bwera ku phiri kuno kwa Yehova, iwe pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu a Israeli makumi asanu ndi awiri. Enanu mundipembedze muli chapatali.
2 And Moses himselfe alone shall come neere to the Lord, but they shall not come neere, neither shall the people goe vp with him.
Koma Mose yekha ayandikire Yehova, ndipo enawo asayandikire. Komanso anthu ena onse asakwere nawe ku phiri kuno.”
3 Afterwarde Moses came and told the people all the wordes of the Lord, and all the lawes: and all the people answered with one voyce, and said, All the things which the Lord hath said, will we doe.
Tsono Mose anapita kukawuza anthu mawu onse a Yehova ndi malamulo onse, ndipo anthu onse anayankha mogwirizana kuti, “Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.”
4 And Moses wrote all the wordes of the Lord, and rose vp early, and set vp an altar vnder the mountaine, and twelue pillars according to the twelue tribes of Israel.
Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena. Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli.
5 And he sent young men of the children of Israel, which offered burnt offrings of bieues, and sacrificed peace offrings vnto the Lord.
Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano.
6 Then Moses tooke halfe of the blood, and put it in basens, and halfe of the blood he sprinckled on the altar.
Mose anatenga theka la magazi ndi kuyika mʼmbale, ndipo theka linalo analiwaza pa guwa lansembe.
7 After he tooke the booke of the couenant, and read it in the audience of the people: who said, All that the Lord hath said, we will do, and be obedient.
Anatenganso Buku la Chipangano ndi kuwerengera anthu. Anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tamva, ndipo tidzazichita.”
8 Then Moses tooke the blood, and sprinkled it on the people, and said, Behold, the blood of the couenant, which the Lord hath made with you concerning all these things.
Kenaka Mose anatenga magazi, nawaza anthuwo ndipo anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapanga ndi inu molingana ndi mawu ake onsewa.”
9 Then went vp Moses and Aaron, Nadab, and Abihu, and seuentie of the Elders of Israel.
Kenaka Mose pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Israeli aja anakwera ku phiri,
10 And they saw the God of Israel, and vnder his feete was as it were a worke of a Saphir stone, and as the very heauen when it is cleare.
ndipo anaona Mulungu wa Israeli. Pansi pa mapazi ake panali njira yoyendamo yopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino wa maonekedwe owala ngati thambo.
11 And vpon the nobles of the children of Israel he laide not his hande: also they sawe God, and did eate and drinke.
Ngakhale anaona Yehova koma sanafe, mʼmalo mwake anadya ndi kumwa.
12 And the Lord said vnto Moses, Come vp to me into the mountaine, and be there, and I will giue thee tables of stone, and the law and the commandement, which I haue written, for to teach them.
Yehova anati kwa Mose, “Bwera kwa ine ku phiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malemba kuti ndiwaphunzitse.”
13 Then Moses rose vp, and his minister Ioshua, and Moses went vp into the mountaine of God,
Ndipo anayamba ulendo wopita ku phiri la Mulungu pamodzi ndi womuthandiza wake Yoswa.
14 And said vnto the Elders, Tary vs here, vntill we come againe vnto you: and beholde, Aaron, and Hur are with you: whosoeuer hath any matters, let him come to them.
Apa nʼkuti Mose atawawuza akuluakulu aja kuti, “Mudikire pano mpaka titabweranso. Aaroni ndi Huri ali nanu, aliyense amene ali ndi milandu apite kwa iwo.”
15 Then Moses went vp to the mount, and the cloude couered the mountaine,
Mose atakwera ku phiri kuja mtambo unaphimba phirilo.
16 And the glorie of the Lord abode vpon mount Sinai, and the cloude couered it sixe dayes: and the seuenth day he called vnto Moses out of the middes of the cloude.
Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo.
17 And the sight of the glorie of the Lord was like consuming fire on the top of the moutaine, in the eyes of the children of Israel.
Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo.
18 And Moses entred into the middes of the cloude, and went vp to the mountaine: and Moses was in the mount fourtie dayes and fourty nightes.
Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku.

< Exodus 24 >