< Deuteronomy 3 >

1 Then we turned, and went vp by the way of Bashan: and Og King of Bashan came out against vs, he, and all his people to fight at Edrei.
Kenaka tinakhota ndi kumayenda mokwera mtunda ndi njira yolowera ku Basani. Ndipo Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anakumana nafe ndipo anamenyana nafe ku Ederi.
2 And the Lord sayde vnto me, Feare him not, for I will deliuer him, and all his people, and his land into thine hand, and thou shalt doe vnto him as thou diddest vnto Sihon King of the Amorites, which dwelt at Heshbon.
Yehova anati kwa ine, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.”
3 So the Lord our God deliuered also vnto our hand, Og the King of Bashan, and all his people: and we smote him, vntill none was left him aliue,
Choncho Yehova Mulungu wathu anapereka mʼmanja mwathu Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo. Tinawakantha onsewo osasiya ndi mmodzi yemwe.
4 And we tooke all his cities the same time, neither was there a citie which we tooke not from them, euen three score cities, and all ye countrey of Argob, the kingdome of Og in Bashan.
Pa nthawi imeneyo tinatenga mizinda yake yonse. Pa mizinda 60, panalibe ndi umodzi womwe umene sitinawalande, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basani chimene ndi chigawo cha Arigobu.
5 All these cities were fenced with hie walles, gates and barres, beside vnwalled townes a great many.
Mizinda yonseyi inali yotetezedwa ndi malinga ataliatali wokhala ndi zitseko ndi zitsulo, komabe panali midzi ina yambiri imene inalibe malinga.
6 And we ouerthrewe them, as we did vnto Sihon King of Heshbon, destroying euery citie, with men, women, and children.
Tinawawonongeratu monga momwe tinachitira Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Tinawononga mzinda uliwonse, amayi, amuna ndi ana omwe.
7 But all the cattell and the spoyle of the cities we tooke for our selues.
Koma tinafunkha ziweto ndi katundu wawo yense.
8 Thus we tooke at that time out of the hand of two Kings of the Amorites, the land that was on this side Iorden from the riuer of Arnon vnto mount Hermon:
Choncho pa nthawi imeneyi tinalanda kwa mafumu awiri Aamori, dera la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku khwawa la Arinoni mpaka ku Phiri la Herimoni.
9 (Which Hermon the Sidonians call Shirion, but the Amorites call it Shenir)
(Asidoni amatcha Herimoni kuti Siriyoni, pamene Aamori amalitcha Seniri).
10 All the cities of the plaine, and all Gilead, and all Bashan vnto Salchah, and Edrei, cities of the kingdome of Og in Bashan.
Tinalanda mizinda yonse ya ku mapiri, ku Giliyadi, Basani mpaka ku Saleka ndi Ederi, mizinda ya mu ufumu wa Ogi wa ku Basani.
11 For onely Og King of Bashan remained of the remnant of the gyants, whose bed was a bed of yron: is it not at Rabbath among the children of Ammon? the length thereof is nine cubites, and foure cubites the breadth of it, after the cubite of a man.
(Ogi, mfumu ya ku Basani, anali yekhayo amene anatsala mwa mtundu wa anthu ataliatali a Chirefai. Bedi lake linali lachitsulo ndipo lalitali kuposa mamita anayi. Mulifupi mwake munali mamita awiri. Bedilo likanalipo ku Raba kwa Aamori).
12 And this land which we possessed at that time, from Aroer, which is by the riuer of Arnon, and halfe mount Gilead, and the cities thereof, gaue I vnto the Reubenites and Gadites.
Dziko limene tinalanda nthawi imeneyo, ndinapatsa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi dera la kumpoto kwa Aroeri cha mʼmphepete mwa khwawa la Arinoni kuphatikizapo theka la dziko lamapiri la Giliyadi ndi mizinda yake.
13 And the rest of Gilead, and all Bashan, the kingdome of Og, gaue I vnto the halfe tribe of Manasseh: euen all the countrey of Argob with all Bashan, which is called, The land of gyants.
Theka la fuko la Manase ndinalipatsa dziko lonse lotsala la Giliyadi ndi Basani yense yemwe ndi dera la ufumu wa Ogi. (Chigawo chonse cha Arigobu mu Basani chinkadziwika kuti ndi dziko la Arefai.
14 Iair the sonne of Manasseh tooke all the countrey of Argob, vnto the coastes of Geshuri, and of Maachathi: and called them after his owne name, Bashan, Hauoth Iair vnto this day.
Yairi, mdzukulu wa Manase, anatenga chigawo chonse cha Arigobu mpaka ku malire a Agesuri ndi Amaakati. Anatcha chigawochi dzina lake, moti mpaka lero Basani amatchedwa Havoti Yairi).
15 And I gaue part of Gilead vnto Machir.
Ndipo ndinapereka Giliyadi kwa Makiri.
16 And vnto the Reubenites and Gadites I gaue the rest of Gilead, and vnto the riuer of Arnon, halfe the riuer and the borders, euen vnto the riuer Iabbok, which is the border of the children of Ammon:
Koma kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi ndinapereka chigawo chochokera ku Giliyadi kutsetsereka mpaka ku khwawa la Arinoni (pakati pa khwawalo ndiye panali malire) ndi kupitirira mpaka ku mtsinje wa Yaboki umene ndi malire Aamoni.
17 The plaine also and Iorden, and the borders from Chinneereth euen vnto the Sea of the plaine, to wit, the salt Sea vnder the springs of Pisgah Eastwarde.
Malire ake a chakumadzulo anali Yorodani ku Araba, kuchokera ku Kinereti mpaka ku Nyanja ya Araba (Nyanja ya Mchere), mʼmunsi mwa matsitso a Pisiga.
18 And I commanded you the same time, saying, The Lord your God hath giuen you this lande to possesse it: ye shall goe ouer armed before your brethren the children of Israel, all men of warre.
Ndinakulamulirani nthawi imene ija kuti, “Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili kuti likhale lanu. Koma amuna amphamvu onse ali ndi zida zankhondo, awoloke kutsogolera abale anu Aisraeli.
19 Your wiues onely, and your children, and your cattel (for I know that ye haue much cattel) shall abide in your cities, which I haue giuen you,
Koma akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri) zikhoza kumakhalabe mʼmizinda imene ndakupatsani,
20 Vntill the Lord haue giuen rest vnto your brethren as vnto you, and that they also possesse the lande, which the Lord your God hath giuen them beyond Iorden: then shall ye returne euery man vnto his possession, which I haue giuen you.
mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, nawonso atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa patsidya pa Yorodani, monga wachitira ndi inu. Kenaka, aliyense wa inu akhoza kudzabwerera ku dziko limene ndinakupatsani.”
21 And I charged Ioshua the same time, saying, Thine eyes haue seene all that the Lord your God hath done vnto these two Kings: so shall the Lord doe vnto all the kingdomes whither thou goest.
Nthawi imeneyo ndinamulamula Yoswa kuti, “Waona wekha ndi maso ako zonse zimene Yehova Mulungu wako anachitira mafumu awiriwa. Yehova adzachita zomwezo ndi mafumu ena onse kumene mukupitako.
22 Ye shall not feare them: for the Lord your God, he shall fight for you.
Musawaope chifukwa Yehova Mulungu mwini adzakumenyerani nkhondo.”
23 And I besought the Lord the same time, saying,
Nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti,
24 O Lord God, thou hast begunne to shewe thy seruant thy greatnesse and thy mightie hande: for where is there a God in heauen or in earth, that can do like thy workes, and like thy power?
“Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita?
25 I pray thee let me go ouer and see the good land that is beyond Iorden, that goodly mountaine, and Lebanon.
Mundilole ndipite ndi kukaona dziko labwinolo kutsidya kwa Yorodani dziko la mapiri abwinowo ndi Lebanoni.”
26 But the Lord was angrie with me for your sakes, and would not heare me: and the Lord said vnto me, Let it suffice thee, speake no more vnto me of this matter.
Koma chifukwa cha inu, Yehova anakwiya nane osandimvera. Yehova anati, “Basi pakwana, usayankhulenso ndi ine zimenezi.
27 Get thee vp into the top of Pisgah, and lift vp thine eyes Westward, and Northwarde, and Southward, and Eastward, and behold it with thine eyes, for thou shalt not goe ouer this Iorden:
Pita pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo uyangʼane kumadzulo, kumpoto, kummwera ndi kummawa. Ulione dzikolo ndi maso ako pakuti suwoloka Yorodaniyu.
28 But charge Ioshua, and incourage him, and bolden him: for hee shall goe before this people, and he shall deuide for inheritance vnto them, the land which thou shalt see.
Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.”
29 So wee abode in the valley ouer against Beth-Peor.
Ndipo tinakhala mʼchigwa pafupi ndi Beti-Peori.

< Deuteronomy 3 >