< Psalms 102 >
1 A prayer from someone who is suffering and is tired out, pouring out their troubles to the Lord. Lord please hear my prayer, my cry for help!
Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko. Yehova imvani pemphero langa; kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
2 Don't hide your face from me in my time of trouble! Turn and listen to me, and answer me quickly when I call.
Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pa msautso. Munditcherere khutu; pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.
3 My life is disappearing like smoke; my body feels like it's on fire!
Pakuti masiku anga akupita ngati utsi; mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
4 I'm like grass that's dried up, withered away—I even forget to eat!
Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu; ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
5 All my groaning has worn me out; my bones show through my skin.
Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
6 I'm like a desert owl, like a little owl among the ruins.
Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu, monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
7 I can't sleep. I'm like a lonely bird on a rooftop.
Ndimagona osapeza tulo; ndakhala ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
8 My enemies taunt me all day long. They mock me and swear at me.
Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe; iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
9 Ashes are the food I eat; my tears drip into my drink,
Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
10 because of your anger and hostility, for you have picked me up and tossed me away.
chifukwa cha ukali wanu waukulu, popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
11 My life is fading away like a shadow that lengthens—I'm withering away like grass.
Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo; Ine ndikufota ngati udzu.
12 But you, Lord, reign forever, your fame will last for all generations.
Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya; kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
13 You will take action and have pity on Jerusalem, for it's time to be kind to the city, the time has come.
Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo; nthawi yoyikika yafika.
14 For the people who follow you love its stones; they value even its dust!
Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu; fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
15 Then the nations will be in awe of who you are, Lord; all the kings of the earth will be in awe of your glory.
Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova, mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
16 For the Lord will rebuild Jerusalem; he will appear in glory.
Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni ndi kuonekera mu ulemerero wake.
17 He will pay attention to the prayers of the homeless; he will not disregard their requests.
Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo.
18 Let this be recorded for generations to come, so that people yet to be born may praise the Lord:
Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo, kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:
19 The Lord looked down from above, from the heights of his holy place; he looked down from heaven to the earth,
“Yehova anayangʼana pansi kuchokera ku malo ake opatulika mmwamba, kuchokera kumwamba anayangʼana dziko lapansi,
20 to respond to the groans of prisoners, to set free the children of death.
kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende, kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.”
21 As a result the wonderful nature of the Lord will be celebrated with praise in Jerusalem,
Kotero dzina la Yehova lidzalengezedwa mu Ziyoni ndi matamando ake mu Yerusalemu,
22 when the people of many kingdoms gather together to worship the Lord.
pamene mitundu ya anthu ndi maufumu adzasonkhana kuti alambire Yehova.
23 But as for me, he broke my health while I was still young, cutting my life short.
Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga; Iyeyo anafupikitsa masiku anga.
24 I cried out, “My God, don't take my life while I'm young! You are the one who lives forever.
Choncho Ine ndinati: “Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga; zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.
25 Long ago you created the earth; you made the heavens.
Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu.
26 They will come to an end, but you will not. They will all wear out, like clothes—you will change them, and throw them away.
Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo; zidzatha ngati chovala. Mudzazisintha ngati chovala ndipo zidzatayidwa.
27 But you are the one who always is; your years never come to an end.
Koma Inu simusintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.
28 Our children will live with you, and our children's children will grow in your presence.”
Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu; zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”