< Hosea 6 >
1 “Come on! Let's go back to the Lord. He has torn us to pieces, but now he will heal us. He has struck us down, but now he will bind up our wounds.
“Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova. Iye watikhadzula, koma adzatichiritsa. Iye wativulaza, koma adzamanga mabala athu.
2 In two days he will heal us; after three days he will raise us up so we can live in his presence.
Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa; pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3 Let's get to know the Lord, really strive to know him, and he will appear to us as surely as the sun will rise; he will come to us as certainly as the spring rains fall on the earth.”
Tiyeni timudziwe Yehova, tiyeni tilimbike kumudziwa Iye. Adzabwera kwa ife mosakayikira konse ngati kutuluka kwa dzuwa; adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe, ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
4 Ephraim, what shall I do with you? Judah, what shall I do with you? Your love disappears like mist at dawn; it vanishes like dew in the morning.
Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani? Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda? Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa, ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
5 So I cut you down through the prophets; I killed you with my words. My judgment shines out like a light.
Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga, ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga; chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
6 I want your true love, not your sacrifices; I want you to know me, not your burnt offerings.
Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe, ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
7 But you, just like Adam, broke our agreement, there you were unfaithful to me.
Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa, iwo sanakhulupirike kwa Ine.
8 Gilead is a city of evil people where footprints are tracked in blood.
Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa, okhala ndi zizindikiro za kuphana.
9 Priests are like a gang of bandits, lying in wait to ambush travelers on the road. They commit murder in Shechem, carrying out wicked crimes.
Monga momwe mbala zimadikirira anthu, magulu a ansembe amachitanso motero; iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu, kupalamula milandu yochititsa manyazi.
10 I have seen in the house of Israel something totally disgusting: Ephraim engages in prostitution and Israel is sexually corrupt.
Ndaona chinthu choopsa kwambiri mʼnyumba ya Israeli. Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere, ndipo Israeli wadzidetsa.
11 And as for you, Judah, your harvest-time has been set! When I restore the fortunes of my people,
“Kunenanso za iwe Yuda, udzakolola chilango. “Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”