< Exodus 37 >
1 Bezalel made the Ark of acacia wood measuring two and a half cubits long by a cubit and a half wide by one and a half cubits high.
Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69.
2 He covered it with pure gold on the inside and the outside, and made a gold trim to go around it.
Iye analikuta bokosilo ndi golide wabwino kwambiri mʼkati mwake ndi kunja komwe. Anapanganso mkombero wagolide kuzungulira bokosilo.
3 He cast four gold rings and attached them to its four feet, two on one side and two on the other.
Iye anapanga mphete zinayi zagolide ndi kuzimangirira ku miyendo yake inayi ija, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri.
4 He made poles of acacia wood and covered them with gold.
Kenaka anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide.
5 He placed the poles into the rings on the sides of the Ark, so it could be carried.
Ndipo analowetsa nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira.
6 He made the atonement cover of pure gold, two and a half cubits long by a cubit and a half wide.
Iye anapanga chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69.
7 He made two cherubim of hammered gold for the ends of the atonement cover,
Ndipo anapanga Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo ndi kuwayika mbali ziwiri za chivundikirocho.
8 and put one cherub on each end. All of this was made from one piece of gold.
Iye anapanga kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa anawapangira limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo.
9 The cherubim were designed with spread wings pointing upward, covering the atonement cover. The cherubim were placed facing each another, looking down towards the atonement cover.
Mapiko a Akerubiwo anatambasukira pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo anakhala choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho.
10 Then he made the table of acacia wood two cubits long by a cubit wide by a cubit and a half high.
Iwo anapanga tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69.
11 He covered it with pure gold and made a gold trim to go around it.
Kenaka analikuta ndi golide wabwino kwambiri, ndipo anapanga mkombero wagolide mʼmbali mwake.
12 He made a border around it the width of a hand and put a gold trim on the border.
Iwo anapanga feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo anayika mkombero wagolide kuzungulira feremuyo.
13 He cast four gold rings for the table and attached them to the four corners of the table by the legs.
Iwo anapanga mphete zinayi zagolide ndipo anazilumikiza ku ngodya zake zinayi, kumene kunali miyendo yake inayi.
14 The rings were close to the border to hold the poles used to carry the table.
Mphetezo anaziyika kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo.
15 He made the poles of acacia wood for carrying the table and covered them with gold.
Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo.
16 He made utensils for the table from pure gold: plates and dishes, bowls and pitchers for pouring out drink offerings.
Ndipo anapanga ziwiya za pa tebulolo zagolide wabwino, mbale ndi zipande, mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe za chakumwa.
17 He made the lampstand of pure, hammered gold. The whole of it was made of one piece—its base, shaft, cups, buds, and flowers.
Iwo anapanga choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zinasulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zinapangidwa kumodzi.
18 It had six branches coming out of the sides of the lampstand, three on each side. It had three cups shaped like almond flowers on the first branch, each with buds and petals, three on the next branch.
Mʼmbali mwake munali mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse.
19 Each of six branches that came out had three cups shaped like almond flowers, all complete with buds and petals.
Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zinali pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri panalinso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zinali chimodzimodzi ndipo zinatuluka mʼchoyikapo nyalecho.
20 On the main shaft of the lampstand he made four cups shaped like almond flowers, complete with buds and petals.
Pa choyikapo nyalecho panali zikho zinayi zokhala ngati maluwa amtowo, mphukira ndi maluwa ake.
21 On the six branches that came out of it, he placed a bud under the first pair of branches, a bud under the second pair, and a bud under the third pair.
Mphukira yoyamba inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Mphukira yachitatu inali mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zinali nthambi zisanu ndi imodzi
22 The buds and branches are to be made with the lampstand as one piece, hammered out of pure gold.
Mphukira ndi nthambi zonse zinasulidwa kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.
23 He made seven lamps, as well as wick tongs and their trays of pure gold.
Iwo anapanga nyale zisanu ndi ziwiri, mbaniro ndi zowolera phulusa, zonse zinali zagolide wabwino kwambiri.
24 The lampstand and all these utensils required a talent of pure gold.
Iwo anapanga choyikapo nyale ndi zipangizo zake zonse zagolide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34.
25 He made the altar for burning incense from acacia wood. It was square, measuring a cubit by a cubit, by two cubits high, with horns on its corners that were all one piece with the altar.
Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo.
26 He covered its top, its side, and its horns with pure gold, and made a gold trim to go all around it.
Iwo anakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse ndi nyanga zake, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwalo.
27 He made two gold rings for the altar and attached them below the trim, two on both sides, to hold the poles to carry it.
Anapanga mphete ziwiri pansi pa mkomberowo ndi kulumikiza ku mbali zonse ziwiri kuti apisemo nsichi zonyamulira.
28 He made the poles of acacia wood and covered them with gold.
Anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndipo anayikuta ndi golide.
29 He made the holy anointing oil and the pure, aromatic incense like the product of an expert perfumer.
Iwo anapanganso mafuta opatulika odzozera ndi zofukiza za fungo lokoma kwambiri. Iyi inali ntchito ya mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa.