< 2 Samuel 20 >
1 A rabble-rouser called Sheba, son of Bichri, from the tribe of Benjamin, happened to be there. He blew the ram's horn and shouted: “We have no interest in David, no commitment to Jesse's son. Israelites, let's all go home!”
Ndipo munthu wina wokonda kuyambitsa chisokonezo, dzina lake Seba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini, anali komweko. Iye analiza lipenga ndipo anafuwula kuti, “Ife tilibe chathu mu mfumu wa Davide, tilibe gawo mwa mwana wa Yese! Inu Aisraeli aliyense apite ku nyumba kwake!”
2 So all the men of Israel abandoned David to follow Sheba, son of Bichri. But the men of Judah accompanied their king all the way from the Jordan to Jerusalem.
Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu.
3 When David returned to his palace in Jerusalem, he took the ten concubines he had left to look after the palace and put them in a house under guard. He took care of their needs but he didn't sleep with them. They were imprisoned until they died, living like widows.
Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye.
4 Then the king ordered Amasa, “Call up the army of Judah. Have them come to me within three days, and you come too.”
Kenaka mfumu inati kwa Amasa, “Itanitsa ankhondo a Yuda kuti abwere kwa ine pasanathe masiku atatu, ndipo iwe udzakhale nawo.”
5 Amasa called up the army of Judah, but he took longer than the time he was given.
Motero Amasa anakayitana Ayuda, koma anachedwa, napitirira pa nthawi imene mfumu inamuyikira.
6 David then spoke to Abishai, saying, “Now Sheba the son of Bichri is going to cause us more trouble than Absalom did. Take the king's men and chase him down, or he will take over fortified towns and get away from us.”
Davide anati kwa Abisai, “Tsono Seba mwana wa Bikiri adzatipweteka kuposa momwe Abisalomu anatichitira. Tenga asilikali a mbuye wako ndipo umuthamangitse, mwina adzapeza mizinda yotetezedwa ndi kutithawa ife.”
7 So Joab's men, along with the Cherethites, the Pelethites, and all the experienced fighters, marched out of Jerusalem to chase down Sheba, son of Bichri.
Kotero anthu a Yowabu, Akereti ndi Apeleti ndiponso asilikali onse amphamvu anapita motsogozedwa ndi Abisai. Iwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri.
8 While they were at the large rock in Gibeon, Amasa caught up with them. Joab was dressed for battle. Over his clothes was a belt around his waist with a dagger in its sheath. As he moved forward, it fell out.
Ali pa mwala waukulu wa ku Gibiyoni, Amasa anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala chovala chausilikali ndipo pamwamba pa malayawo, mʼchiwuno mwake anavala lamba womangirirapo lupanga lili moyikamo mwakemo. Akuyenda linasololoka kuchoka moyikamo mwake.
9 “How are you doing, my brother?” Joab asked Amasa. Joab held Amasa by the beard with his right hand to kiss him.
Yowabu anati kwa Amasa, “Kodi uli bwanji mʼbale wanga?” Kenaka Yowabu anamugwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja ndi kupsompsona.
10 Amasa wasn't prepared for the dagger in Joab's left hand. Joab stabbed him in the belly and his intestines poured out onto the ground. Joab didn't need to stab him twice, because Amasa was already dead. Then Joab and his brother Abishai set off in pursuit of Sheba.
Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri.
11 One of Joab's men stood beside Amasa and called out, “If you're on Joab's side, and if you are on David's side, then follow Joab!”
Mmodzi mwa ankhondo a Yowabu anakayimirira pafupi ndi mtembo wa Amasa ndipo anati, “Aliyense amene amakonda Yowabu ndi aliyense amene ali wa Davide, atsatire Yowabu!”
12 But Amasa was there, lying in his blood in the middle of the main road. When the man saw that everybody was stopping to look, he pulled the body off the road into a field and threw a cloth over it.
Amasa anagona pakati pa msewu atasamba magazi ake, ndipo munthuyo anaona kuti asilikali onse amayima pamenepo. Atazindikira kuti aliyense amene ankafika pamene panali Amasa amayima, iye anamuchotsa mu msewu ndi kumukokera mʼmunda ndipo anamuphimba ndi nsalu.
13 Once Amasa's body was off the road, all the men followed Joab in pursuit of Sheba.
Amasa atachotsedwa pa msewu anthu onse anapita ndi Yowabu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri.
14 In the meantime Sheba had gone around all the tribes of Israel and eventually ended up the town of Abel-beth-maacah. All the Bichrites gathered for battle and followed him into the town.
Seba anadutsa mafuko onse a Israeli mpaka ku Abeli ndi Beti-Maaka ndiponso chigawo chonse cha Abeli, amene anasonkhana pamodzi ndi kumutsata iye.
15 Joab's army came and besieged Sheba in Abel-Beth-Maacah. They built a siege ramp against the town's outer wall. While all of Joab's army was battering the wall to knock it down,
Ankhondo onse pamodzi ndi Yowabu anafika ndi kumuzungulira Seba mu Abeli-Beti-Maaka. Iwo anapanga mzere wa nkhondo mpaka ku mzinda, ndipo unayangʼanana ndi malo otetezera a kunja. Pamene amalimbana ndi khoma kuti aligwetse,
16 a wise woman from the town called out, “Listen! Please listen! Tell Joab, ‘Come over here so I can speak to you.’”
mayi wina wanzeru anafuwula kuchokera mu mzindawo, “Tamverani! Tamverani! Muwuzeni Yowabu abwere pano kuti ndiyankhule naye.”
17 He went over to her, and the woman asked, “Are you Joab?” “Yes, that's me,” he replied. “Please listen to what I, your servant, have to say,” she said. “I'm listening,” he replied.
Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?” Iye anayankha kuti, “Ndine.” Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.” Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.”
18 Then the woman said, “In times gone by people used to say, ‘If you want advice, go to Abel,’ and that's how arguments were settled.
Iye anapitiriza kunena kuti, “Kalekale ankanena kuti, ‘Kapeze yankho lako ku Abeli,’ ndipo nkhani imathera pamenepo.
19 I am one of the peaceful and faithful people of Israel. You're trying to destroy a town that's like a mother in Israel. Why do you want to tear down the Lord's possession?”
Ife ndife anthu a mtendere ndi okhulupirika mu Israeli. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene ndi mayi mu Israeli. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufafaniza cholowa cha Yehova?”
20 “Certainly not!” Joab answered. “It's not what I want—to destroy or tear down this town!
Yowabu anayankha kuti, “Ayi ndisatero. Ine sindikufuna kuwufafaniza kapena kuwuwononga.
21 That's not the intention. But a man called Sheba, son of Bichri, from the hill country of Ephraim, has rebelled against the king, against David. Just hand over this one man and I will withdraw from the town.” “Fine,” the woman replied, “his head will be thrown over the wall to you.”
Nkhani simeneyo ayi. Koma munthu wina wa ku dziko lamapiri la Efereimu, dzina lake Seba mwana wa Bikiri, wawukira mfumu Davide. Muperekeni munthuyo ndipo ine ndidzachoka pa mzinda uno.” Mayiyo anati kwa Yowabu, “Mutu wake tikuponyerani pa khoma pano.”
22 The woman went and talked with everyone about her wise plan. So they cut off the head of Sheba and threw it to Joab. Then Joab blew the ram's horn to sound the retreat, and all his men left the town and went home. Joab returned to the king in Jerusalem.
Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu.
23 Joab commanded the whole army of Israel. Benaiah, son of Jehoiada, was in charge of the Cherethites and Pelethites.
Yowabu ndiye amalamulira gulu lonse la ankhondo. Benaya mwana wa Yehoyada amalamulira Akereti ndi Apeleti.
24 Adoniram was in charge of the labor force. Jehoshaphat, son of Ahilud, kept the official records.
Adoramu amayangʼanira anthu ogwira ntchito ya thangata, Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika,
25 Sheva was the secretary. Zadok and Abiathar were the priests,
Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiatara anali ansembe
26 and Ira the Jairite was David's priest.
ndipo Ira wa ku Yairi anali wansembe wa Davide.