< 1 Samuel 31 >
1 Meanwhile the Philistines had attacked Israel, and the Israelite army ran away from them, and many were killed on Mount Gilboa.
Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa.
2 The Philistines chased down Saul and his sons, killing Saul's sons Jonathan, Abinadab, and Malchishua.
Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa.
3 The fighting became very intense around Saul, and the arrows of the Philistine archers found their target, wounding Saul very badly.
Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza kwambiri.
4 Saul said to his armor-bearer, “Take your sword and kill me, or these heathen men will come and kill and torture me!” But the armor-bearer didn't want to do it because he was too afraid. So Saul took his own sword and fell on it.
Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere kudzandizunza ine.” Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo.
5 When his armor-bearer saw that Saul was dead, he also fell on his own sword and died with him.
Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa naye limodzi.
6 Saul, his three sons, his armor-bearer, and all the men with him, died the same day.
Motero Sauli ndi ana ake atatu, wonyamula zida zake pamodzi ndi anthu ake onse anafera limodzi pa tsikulo.
7 When the Israelites who lived along the valley and those on the other side of the Jordan realized that the Israelite army had run away, and that Saul and his sons had died, they abandoned their cities and they also ran away. So the Philistines came and took them over.
Pamene Aisraeli amene anali tsidya lina la chigwa ndi amene anali tsidya la chigwa cha Yorodani anaona kuti gulu la ankhondo la Aisraeli lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.
8 The next day, when the Philistines went to strip the dead, they found Saul and his three sons lying on Mount Gilboa.
Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa pa phiri la Gilibowa.
9 They cut off Saul's head, stripped him of his armor, and sent messengers throughout the country of the Philistines to announce the news in the temples of their idols and to their people.
Iwo anadula mutu wake ndi kumuvula zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo.
10 They placed his armor in the temple of the Ashtoreths, and nailed his body to the town wall of Beth-shan.
Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba yopembedzera Asitoreti, ndipo thupi lake analikhomera pa khoma la mzinda wa Beti-Sani.
11 However, when the people of Jabesh-gilead heard what the Philistines had done to Saul,
Pamene anthu a ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli,
12 all their strong warriors set out, traveled all night, and took down the bodies of Saul and his sons from the wall of Beth-shan. When they got back to Jabesh, they burned the bodies there.
anthu awo onse olimba mtima anayenda usiku wonse kupita ku Beti-Sani. Anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pa khoma la mzinda wa Beti-Sani, ndipo anabwera nayo ku Yabesi kumene anayitentha ndi moto.
13 Then they took their bones and buried them under the tamarisk tree in Jabesh, and fasted for seven days.
Pambuyo pake anatenga mafupa awo ndi kuwakwirira pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.