< 1 Kings 5 >
1 When Hiram king of Tyre heard that Solomon had been anointed king to succeed his father, he sent ambassadors to Solomon because Hiram had always been David's friend.
Hiramu mfumu ya ku Turo atamva kuti Solomoni wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo ake Davide, anatumiza akazembe ake kwa Solomoni, chifukwa mfumu Hiramu inali pa ubale wabwino ndi Davide nthawi zonse.
2 So Solomon sent this message back to Hiram,
Solomoni anabweza mawu awa kwa Hiramu:
3 “As you know, my father David was not able to build a Temple to honor the Lord his God because of the wars fought against him from every direction, until the Lord had conquered his enemies.
“Inu mukudziwa kuti chifukwa cha nkhondo zimene zinkachokera ku mbali zonse kulimbana ndi abambo anga, iwo sanathe kumangira Nyumba Yehova Mulungu wawo, mpaka Yehova atawayika adani awo pansi pa ulamuliro wawo.
4 But now the Lord my God has given me peace all around—no enemies, no bad things happening.
Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko ndipo ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse.
5 So I plan to build a Temple to honor the Lord my God, as the Lord told my father David. He said to him, ‘Your son whom I will place on your throne to succeed you will build the Temple to honor me.’
Choncho ine ndikufuna kumangira nyumba Yehova Mulungu wanga, monga momwe Iye anawuzira abambo anga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando waufumu mʼmalo mwako ndiye adzandimangire Nyumba.’
6 So please order some cedars of Lebanon to be cut down for me. My workers will assist your workers, and I will pay your workers at the rate that you decide, for you know that we don't have anyone who knows how to cut timber like the Sidonians.”
“Choncho lamulani kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Anthu anga adzagwira ntchito imeneyo pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzalipira anthu anuwo malipiro amene inu mungakhazikitse. Inu mukudziwa kuti ife tilibe anthu aluso locheka matabwa monga Asidoni.”
7 When Hiram heard Solomon's message, he was very happy and said, “Praise the Lord today, for he has given David a wise son to lead this great nation!”
Hiramu anakondwa kwambiri atamva uthenga wa Solomoni ndipo anati, “Lero Yehova atamandike chifukwa wapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu waukuluwu.”
8 Hiram sent this reply to Solomon: “Thank you for your message. As for the cedar and cypress timber, I will do everything you want.
Tsono Hiramu anabweza mawu awa kwa Solomoni: “Ndalandira uthenga umene mwanditumizira ndipo ine ndidzachita zonse zimene mukufuna pokupatsani mitengo ya mkungudza ndi payini.
9 My workers will bring the logs down from Lebanon to the sea, and I will have them floated in rafts by sea to wherever you decide. I will have the rafts broken apart there, and you can take the logs away. In return I would like you to provide food for my household.”
Anthu anga adzatsika nayo kuchokera ku Lebanoni mpaka ku nyanja, ndipo adzayiyandamitsa pa nyanja mpaka ku malo amene munene. Kumeneko ndidzayimasula ndipo mudzayitenga. Ndipo inu mudzakwaniritsa chokhumba changa pondipatsa chakudya cha banja langa laufumu.”
10 So Hiram provided Solomon with as much cedar and cypress timber that he wanted,
Motero Hiramu anapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi payini imene ankayifuna,
11 Solomon gave Hiram 20,000 cors of wheat for food and 20,000 cors of olive oil for his household. Solomon provided this to Hiram every year.
ndipo Solomoni anamupatsa Hiramu mitanga ya tirigu 20,000 ngati chakudya cha pa nyumba yake, kuwonjezera pa migolo ya mafuta a olivi yokwana 20,000. Solomoni anapitiriza kupereka zimenezi chaka ndi chaka.
12 The Lord gave Solomon wisdom just as he had promised him. Hiram and Solomon had a good relationship and they made a peace treaty with each other.
Yehova anamupatsa Solomoni nzeru monga momwe analonjezera. Panali ubale wa mtendere pakati pa Solomoni ndi Hiramu, ndipo awiriwa anachita pangano.
13 King Solomon drafted a labor force of 30,000 from all of Israel.
Mfumu Solomoni inasonkhanitsa anthu ogwira ntchito ya thangata mʼdziko lonse la Israeli ndipo anthu athangatawo analipo 30,000.
14 He sent them in shifts of 10,000 each month to Lebanon, so that they were one month in Lebanon and two months at home, Adoniram was in charge of the labor force.
Iye ankatumiza anthu 10,000 ku Lebanoni pa mwezi mosinthanasinthana, kotero kuti ankakhala ku Lebanoniko mwezi umodzi ndipo kwawo ankakhalako miyezi iwiri. Adoniramu ndiye ankayangʼanira ogwira ntchito yathangatayo.
15 Solomon had 70,000 porters and 80,000 stonecutters in the hill country,
Solomoni anali ndi anthu amtengatenga 70,000, anthu 80,000 osema miyala ku mapiri,
16 as well as 3,300 foremen he placed in charge of the workers.
ndi akapitawo 33,000 amene ankayangʼanira ntchitoyi ndiponso anthu ogwira ntchito zina.
17 Following the king's orders, they quarried large blocks of stone that were expensive to produce, and laid these dressed stones as the foundation for the Temple.
Molamulidwa ndi mfumu, anakumba ndi kusema miyala ikuluikulu kwambiri yoti akamangire maziko a Nyumba ya Mulungu.
18 So Solomon's and Hiram's builders, together with the Gebalites, cut the stone. They prepared the timber and stone to build the Temple.
Amisiri a Solomoni ndi a Hiramu ndiponso anthu a ku Gebala anasema miyala ndi kukonza matabwa ndi miyala yomangira Nyumba ya Mulungu.