< Luke 3 >
1 Now in the fifteenth year of the government of Tiberius Caesar, Pontius Pilate being governor of Judaea, and Herod tetrarch of Galilee, and Philip his brother tetrarch of Ituraea and the region of Trachonitis, and Lysanias tetrarch of Abilene,
Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene.
2 in the high priesthood of Annas and Caiaphas, [the] word of God came upon John, the son of Zacharias, in the wilderness.
Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu.
3 And he came into all the district round the Jordan, preaching [the] baptism of repentance for [the] remission of sins,
Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo.
4 as it is written in [the] book of [the] words of Esaias the prophet: Voice of one crying in the wilderness: Prepare ye the way of [the] Lord, make straight his paths.
Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti: “Mawu a wofuwula mʼchipululu, konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.
5 Every gorge shall be filled up, and every mountain and hill shall be brought low, and the crooked [places] shall become a straight [path], and the rough places smooth ways,
Chigwa chilichonse chidzadzazidwa ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa, misewu yokhotakhota idzawongoledwa, ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.
6 and all flesh shall see the salvation of God.
Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”
7 He said therefore to the crowds which went out to be baptised by him, Offspring of vipers, who has forewarned you to flee from the coming wrath?
Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera?
8 Produce therefore fruits worthy of repentance; and begin not to say in yourselves, We have Abraham for [our] father, for I say unto you that God is able of these stones to raise up children to Abraham.
Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana.
9 And already also the axe is applied to the root of the trees; every tree therefore not producing good fruit is cut down and cast into [the] fire.
Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”
10 And the crowds asked him saying, What should we do then?
Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?”
11 And he answering says to them, He that has two body-coats, let him give to him that has none; and he that has food, let him do likewise.
Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”
12 And tax-gatherers came also to be baptised, and they said to him, Teacher, what should we do?
Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?”
13 And he said to them, Take no more [money] than what is appointed to you.
Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.”
14 And persons engaged in military service also asked him saying, And we, what should we do? And he said to them, Oppress no one, nor accuse falsely, and be satisfied with your pay.
Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”
15 But as the people were in expectation, and all were reasoning in their hearts concerning John whether he might be the Christ,
Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu.
16 John answered all, saying, I indeed baptise you with water, but the mightier than I is coming, the thong of whose sandals I am not fit to unloose; he shall baptise you with [the] Holy Spirit and fire;
Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto.
17 whose winnowing-fan is in his hand, and he will thoroughly purge his threshing-floor, and will gather the wheat into his garner, but the chaff he will burn with fire unquenchable.
Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.”
18 Exhorting then many other things also he announced [his] glad tidings to the people.
Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.
19 But Herod the tetrarch, being reproved by him as to Herodias, the wife of his brother, and as to all the wicked things which Herod had done,
Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita,
20 added this also to all [the rest], that he shut up John in prison.
Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.
21 And it came to pass, all the people having been baptised, and Jesus having been baptised and praying, that the heaven was opened,
Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka.
22 and the Holy Spirit descended in a bodily form as a dove upon him; and a voice came out of heaven, Thou art my beloved Son, in thee I have found my delight.
Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”
23 And Jesus himself was beginning to be about thirty years old; being as was supposed son of Joseph; of Eli,
Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe, mwana wa Heli,
24 of Matthat, of Levi, of Melchi, of Janna, of Joseph,
mwana wa Matate, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe
25 of Mattathias, of Amos, of Naoum, of Esli, of Naggai,
mwana wa Matati, mwana wa Amosi, mwana wa Naomi, mwana wa Esli, mwana wa Nagai,
26 of Maath, of Mattathias, of Semei, of Joseph, of Juda,
mwana wa Maati, mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni, mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda
27 of Joannes, of Resa, of Zorobabel, of Salathiel, of Neri,
mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli, mwana wa Neri,
28 of Melchi, of Addi, of Cosam, of Elmodam, of Er,
mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,
29 of Joses, of Eliezer, of Joreim, of Matthat, of Levi,
mwana wa Jose, mwana wa Eliezara, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,
30 of Simeon, of Juda, of Joseph, of Jonan, of Eliakim,
mwana wa Simeoni, mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu,
31 of Meleas, of Menan, of Mattatha, of Nathan, of David,
mwana wa Meleya, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natani, mwana wa Davide,
32 of Jesse, of Obed, of Booz, of Salmon, of Naasson,
mwana wa Yese, mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni,
33 of Aminadab, of Aram, of Esrom, of Phares, of Juda,
mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni, mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,
34 of Jacob, of Isaac, of Abraham, of Terah, of Nachor,
mwana wa Yakobo, mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,
35 of Seruch, of Ragau, of Phalek, of Eber, of Sala,
mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi, mwana wa Sela,
36 of Cainan, of Arphaxad, of Sem, of Noe, of Lamech,
mwana wa Kainane, mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,
37 of Methusala, of Enoch, of Jared, of Maleleel, of Cainan,
mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli, mwana wa Kainane,
38 of Enos, of Seth, of Adam, of God.
mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.