< John 6 >
1 After these things Jesus went away beyond the sea of Galilee, [or] of Tiberias,
Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya),
2 and a great crowd followed him, because they saw the signs which he wrought upon the sick.
ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala.
3 And Jesus went up into the mountain, and there sat with his disciples:
Kenaka Yesu anakwera pa phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake.
4 but the passover, the feast of the Jews, was near.
Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi.
5 Jesus then, lifting up his eyes and seeing that a great crowd is coming to him, says to Philip, Whence shall we buy loaves that these may eat?
Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, “Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?”
6 But this he said trying him, for he knew what he was going to do.
Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.
7 Philip answered him, Loaves for two hundred denarii are not sufficient for them, that each may have some little [portion].
Filipo anamuyankha Iye kuti, “Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!”
8 One of his disciples, Andrew, Simon Peter's brother, says to him,
Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati,
9 There is a little boy here who has five barley loaves and two small fishes; but this, what is it for so many?
“Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?”
10 [And] Jesus said, Make the men sit down. Now there was much grass in the place: the men therefore sat down, in number about five thousand.
Yesu anati, “Awuzeni anthuwa akhale pansi.” Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000.
11 And Jesus took the loaves, and having given thanks, distributed [them] to those that were set down; and in like manner of the small fishes as much as they would.
Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.
12 And when they had been filled, he says to his disciples, Gather together the fragments which are over and above, that nothing may be lost.
Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.”
13 They gathered [them] therefore together, and filled twelve hand-baskets full of fragments of the five barley loaves, which were over and above to those that had eaten.
Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.
14 The men therefore, having seen the sign which Jesus had done, said, This is truly the prophet which is coming into the world.
Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, “Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi.”
15 Jesus therefore knowing that they were going to come and seize him, that they might make [him] king, departed again to the mountain himself alone.
Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuwumiriza kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri pa yekha.
16 But when evening was come, his disciples went down to the sea,
Pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira ku nyanja,
17 and having gone on board ship, they went over the sea to Capernaum. And it had already become dark, and Jesus had not come to them,
kumene iwo analowa mʼbwato ndi kuyamba kuwoloka nyanja kupita ku Kaperenawo. Tsopano kunali kutada ndipo Yesu anali asanabwerere kwa iwo.
18 and the sea was agitated by a strong wind blowing.
Mphepo yamphamvu inawomba ndipo nyanja inalusa.
19 Having rowed then about twenty-five or thirty stadia, they see Jesus walking on the sea and coming near the ship; and they were frightened.
Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha.
20 But he says to them, It is I: be not afraid.
Koma Iye anawawuza kuti, “Ndine, musaope.”
21 They were willing therefore to receive him into the ship; and immediately the ship was at the land to which they went.
Ndipo iwo analola kumutenga mʼbwatomo, nthawi yomweyo bwatolo linafika ku gombe la nyanja kumene ankapita.
22 On the morrow the crowd which stood on the other side of the sea, having seen that there was no other little ship there except that into which his disciples had got, and that Jesus had not gone with his disciples into the ship, but [that] his disciples had gone away alone;
Pa tsiku lotsatira gulu la anthu limene linatsala kumbali ina yanyanjayo linaona kuti panali bwato limodzi lokha, ndipo kuti Yesu sanalowe mʼbwatomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzirawo anapita okha.
23 (but other little ships out of Tiberias came near to the place where they ate bread after the Lord had given thanks; )
Kenaka mabwato ena ochokera ku Tiberiya anafika pafupi ndi pamalo pamene anthu anadya buledi Ambuye atayamika.
24 when therefore the crowd saw that Jesus was not there, nor his disciples, they got into the ships, and came to Capernaum, seeking Jesus.
Nthawi yomwe gulu la anthu linaona kuti Yesu kapena ophunzira ake sanali pamenepo, ilo linalowanso mʼmabwatowo ndi kupita ku Kaperenawo kukamufunafuna Yesu.
25 And having found him the other side of the sea, they said to him, Rabbi, when art thou arrived here?
Atamupeza mbali ina ya nyanjayo, iwo anamufunsa Iye kuti, “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?”
26 Jesus answered them and said, Verily, verily, I say to you, Ye seek me not because ye have seen signs, but because ye have eaten of the loaves and been filled.
Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta.
27 Work not [for] the food which perishes, but [for] the food which abides unto life eternal, which the Son of man shall give to you; for him has the Father sealed, [even] God. (aiōnios )
Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.” (aiōnios )
28 They said therefore to him, What should we do that we may work the works of God?
Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”
29 Jesus answered and said to them, This is the work of God, that ye believe on him whom he has sent.
Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.”
30 They said therefore to him, What sign then doest thou that we may see and believe thee? what dost thou work?
Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani?
31 Our fathers ate the manna in the wilderness, as it is written, He gave them bread out of heaven to eat.
Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’”
32 Jesus therefore said to them, Verily, verily, I say to you, [It is] not Moses that has given you the bread out of heaven; but my Father gives you the true bread out of heaven.
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba.
33 For the bread of God is he who comes down out of heaven and gives life to the world.
Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.”
34 They said therefore to him, Lord, ever give to us this bread.
Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.”
35 [And] Jesus said to them, I am the bread of life: he that comes to me shall never hunger, and he that believes on me shall never thirst at any time.
Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
36 But I have said to you, that ye have also seen me and do not believe.
Monga ndakuwuzani kale, ngakhale kuti mwandiona simukukhulupirirabe.
37 All that the Father gives me shall come to me, and him that comes to me I will not at all cast out.
Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja.
38 For I am come down from heaven, not that I should do my will, but the will of him that has sent me.
Pakuti Ine ndinatsika kuchokera kumwamba osati kudzachita chifuniro changa koma cha Iye amene anandituma Ine.
39 And this is the will of him that has sent me, that of all that he has given me I should lose nothing, but should raise it up in the last day.
Ndipo chifuniro cha Iye amene anandituma Ine nʼchakuti ndisatayepo ngakhale ndi mmodzi yemwe mwa onse amene Iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza.
40 For this is the will of my Father, that every one who sees the Son, and believes on him, should have life eternal; and I will raise him up at the last day. (aiōnios )
Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.” (aiōnios )
41 The Jews therefore murmured about him, because he said, I am the bread which has come down out of heaven.
Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.”
42 And they said, Is not this Jesus the son of Joseph, whose father and mother we have known? how then does he say, I am come down out of heaven?
Iwo anati, “Kodi uyu si Yesu, mwana wa Yosefe, amene abambo ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga Iyeyu akunena bwanji kuti, ‘Ine ndinatsika kuchokera kumwamba?’”
43 Jesus therefore answered and said to them, Murmur not among yourselves.
Yesu anayankha kuti, “Musangʼungʼudze pakati panu.”
44 No one can come to me except the Father who has sent me draw him, and I will raise him up in the last day.
Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
45 It is written in the prophets, And they shall be all taught of God. Every one that has heard from the Father [himself], and has learned [of him], comes to me;
Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine.
46 not that any one has seen the Father, except he who is of God, he has seen the Father.
Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate.
47 Verily, verily, I say to you, He that believes [on me] has life eternal. (aiōnios )
Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha. (aiōnios )
48 I am the bread of life.
Ine ndine chakudya chamoyo.
49 Your fathers ate the manna in the wilderness and died.
Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa.
50 This is the bread which comes down out of heaven, that one may eat of it and not die.
Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe.
51 I am the living bread which has come down out of heaven: if any one shall have eaten of this bread he shall live for ever; but the bread withal which I shall give is my flesh, which I will give for the life of the world. (aiōn )
Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.” (aiōn )
52 The Jews therefore contended among themselves, saying, How can he give us this flesh to eat?
Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?”
53 Jesus therefore said to them, Verily, verily, I say unto you, Unless ye shall have eaten the flesh of the Son of man, and drunk his blood, ye have no life in yourselves.
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.
54 He that eats my flesh and drinks my blood has life eternal, and I will raise him up at the last day: (aiōnios )
Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. (aiōnios )
55 for my flesh is truly food and my blood is truly drink.
Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni.
56 He that eats my flesh and drinks my blood dwells in me and I in him.
Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye.
57 As the living Father has sent me and I live on account of the Father, he also who eats me shall live also on account of me.
Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.
58 This is the bread which has come down out of heaven. Not as the fathers ate and died: he that eats this bread shall live for ever. (aiōn )
Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.” (aiōn )
59 These things he said in [the] synagogue, teaching in Capernaum.
Iye ankanena izi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge mu Kaperenawo.
60 Many therefore of his disciples having heard [it] said, This word is hard; who can hear it?
Pakumva izi ambiri a ophunzira ake anati, “Ichi ndi chiphunzitso chovuta. Angachilandire ndani?”
61 But Jesus, knowing in himself that his disciples murmur concerning this, said to them, Does this offend you?
Pozindikira kuti ophunzira ake ankangʼungʼudza, Yesu anawafunsa kuti, “Kodi izi zikukukhumudwitsani?
62 If then ye see the Son of man ascending up where he was before?
Nanga mutaona Mwana wa Munthu akukwera kupita kumene Iye anali poyamba!
63 It is the Spirit which quickens, the flesh profits nothing: the words which I have spoken unto you are spirit and are life.
Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.
64 But there are some of you who do not believe. For Jesus knew from the beginning who they were who did not believe, and who would deliver him up.
Komabe alipo ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti Yesu ankadziwa kuyambira pachiyambi ena mwa iwo amene samakhulupirira ndi amene adzamupereka Iye.
65 And he said, Therefore said I unto you, that no one can come to me unless it be given to him from the Father.
Iye anapitiriza kunena kuti, “Ichi ndi chifukwa chake ndinakuwuzani kuti palibe wina angabwere kwa Ine pokhapokha Atate atamuthandiza.”
66 From that [time] many of his disciples went away back and walked no more with him.
Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye.
67 Jesus therefore said to the twelve, Will ye also go away?
Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, “Kodi inu mukufuna kuchokanso?”
68 Simon Peter answered him, Lord, to whom shall we go? thou hast words of life eternal; (aiōnios )
Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha. (aiōnios )
69 and we have believed and known that thou art the holy one of God.
Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu.”
70 Jesus answered them, Have not I chosen you the twelve? and of you one is a devil.
Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi Ine sindinakusankheni inu khumi ndi awiri? Komabe mmodzi wa inu ndi mdierekezi.”
71 Now he spoke of Judas [the son] of Simon, Iscariote, for he [it was who] should deliver him up, being one of the twelve.
(Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka).