< Exodus 16 >
1 And they went on their way from Elim, and all the children of Israel came into the waste land of Sin, which is between Elim and Sinai, on the fifteenth day of the second month after they went out of the land of Egypt.
Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai.
2 And all the children of Israel were crying out against Moses and Aaron in the waste land:
Mʼchipululumo gulu lonse linadandaulira Mose ndi Aaroni
3 And the children of Israel said to them, It would have been better for the Lord to have put us to death in the land of Egypt, where we were seated by the flesh-pots and had bread enough for our needs; for you have taken us out to this waste of sand, to put all this people to death through need of food.
kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!”
4 Then the Lord said to Moses, See, I will send down bread from heaven for you; and the people will go out every day and get enough for the day's needs; so that I may put them to the test to see if they will keep my laws or not.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga.
5 And on the sixth day they are to make ready what they get in, and it will be twice as much as they get on the other days.
Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.”
6 And Moses and Aaron said to all the children of Israel, This evening it will be clear to you that it is the Lord who has taken you out of the land of Egypt:
Kotero Mose ndi Aaroni anati kwa Aisraeli onse, “Nthawi yamadzulo inu mudzadziwa kuti ndi Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.
7 And in the morning you will see the glory of the Lord; for your angry words against the Lord have come to his ears: and what are we that you are crying out against us?
Ndipo mmawa mudzaona ulemerero wa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu. Kodi ife ndi yani kuti muzitidandaulira?”
8 And Moses said, The Lord will give you meat for your food at evening, and in the morning bread in full measure; for your outcry against the Lord has come to his ears: for what are we? your outcry is not against us but against the Lord.
Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.”
9 And Moses said to Aaron, Say to all the people of Israel, Come near before the Lord for he has given ear to your outcry.
Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’”
10 And while Aaron was talking to the children of Israel, their eyes were turned in the direction of the waste land, and they saw the glory of the Lord shining in the cloud.
Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo.
11 And the Lord said to Moses,
Yehova anati kwa Mose,
12 The outcry of the children of Israel has come to my ears: say to them now, At nightfall you will have meat for your food, and in the morning bread in full measure; and you will see that I am the Lord your God.
“Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”
13 And it came about that in the evening little birds came up and the place was covered with them: and in the morning there was dew all round about the tents.
Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo.
14 And when the dew was gone, on the face of the earth was a small round thing, like small drops of ice on the earth.
Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale.
15 And when the children of Israel saw it, they said to one another, What is it? for they had no idea what it was. And Moses said to them, It is the bread which the Lord has given you for your food.
Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, “Kodi timeneti nʼchiyani?” Popeza sanatidziwe. Mose anawawuza kuti, “Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye.
16 This is what the Lord has said, Let every man take up as much as he has need of; at the rate of one omer for every person, let every man take as much as is needed for his family.
Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’”
17 And the children of Israel did so, and some took more and some less.
Aisraeli anachita zonse anawawuza. Ena anatola zambiri ena zochepa.
18 And when it was measured, he who had taken up much had nothing over, and he who had little had enough; every man had taken what he was able to make use of.
Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya.
19 And Moses said to them, Let nothing be kept till the morning.
Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.”
20 But they gave no attention to Moses, and some of them kept it till the morning and there were worms in it and it had an evil smell: and Moses was angry with them.
Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima.
21 And they took it up morning by morning, every man as he had need: and when the sun was high it was gone.
Mmawa uliwonse aliyense amatola zimene amazifuna, ndipo dzuwa likatentha zimasungunuka.
22 And on the sixth day they took up twice as much of the bread, two omers for every person: and all the rulers of the people gave Moses word of it.
Tsiku lachisanu ndi chimodzi anatuta malita anayi munthu aliyense, ndipo atsogoleri a mpingo wonse anabwera kudzawuza Mose za zimenezi.
23 And he said, This is what the Lord has said, Tomorrow is a day of rest, a holy Sabbath to the Lord: what has to be cooked may be cooked; and what is over, put on one side to be kept till the morning.
Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’”
24 And they kept it till the morning as Moses had said: and no smell came from it, and it had no worms.
Choncho anasunga mpaka mmawa monga Mose anawalamulira, ndipo sananunkhe kapena kuchita mphutsi.
25 And Moses said, Make your meal today of what you have, for this day is a Sabbath to the Lord: today you will not get any in the fields.
Mose anati, “Idyani lero chifukwa lero ndi Sabata la Yehova. Lero simukapeza chilichonse kunjaku.
26 For six days you will get it, but on the seventh day, the Sabbath, there will not be any.
Muzitola chakudya masiku asanu ndi limodzi koma tsiku la chisanu ndi chiwiri ndi la Sabata, simukapeza chilichonse kunjaku.”
27 But still on the seventh day some of the people went out to get it, and there was not any.
Komabe anthu ena anapita kuti akatole chakudya tsiku lachisanu ndi chiwiri, koma sanapeze kanthu.
28 And the Lord said to Moses, How long will you go against my orders and my laws?
Ndipo Yehova anafunsa Mose nati, “Kodi inu muzipitirira kukana kusunga malamulo ndi malangizo anga mpaka liti?
29 See, because the Lord has given you the Sabbath, he gives you on the sixth day bread enough for two days; let every man keep where he is; let no man go out of his place on the seventh day.
Taonani, popeza Yehova wakupatsani Sabata nʼchifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi amakupatsani chakudya cha masiku awiri. Aliyense azikhala pamene ali pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, pasapezeke wotuluka kunja.”
30 So the people took their rest on the seventh day.
Kotero anthu anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri.
31 And this bread was named manna by Israel: it was white, like a grain seed, and its taste was like cakes made with honey.
Aisraeli anatchula chakudyacho Mana. Chakudyacho chinkaoneka ngati mbewu zamapira, zoyera. Ndipo chinkakoma ngati chothira uchi.
32 And Moses said, This is the order which the Lord has given: Let one omer of it be kept for future generations, so that they may see the bread which I gave you for your food in the waste land, when I took you out from the land of Egypt.
Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’”
33 And Moses said to Aaron, Take a pot and put one omer of manna in it, and put it away before the Lord, to be kept for future generations.
Choncho Mose anati kwa Aaroni, “Tenga mtsuko ndipo uyikemo malita awiri a mana. Ndipo uyike manawo pamaso pa Yehova kusungira mibado imene ikubwera.”
34 So Aaron put it away in front of the holy chest to be kept, as the Lord gave orders to Moses.
Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aaroni anayika mtsuko uja pafupi ndi bokosi la Chipangano kuti manawo asungike.
35 And the children of Israel had manna for their food for forty years, till they came to a land with people in it, till they came to the edge of the land of Canaan.
Aisraeli anadya mana zaka 40, mpaka pamene anafika ku dziko kumene amati akakhazikeko. Iwo anadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a Kanaani.
36 Now an omer is the tenth part of an ephah.
(Malita awiri amafanana ndi gawo lakhumi la efa).