< Micah 5 >

1 Now, O daughter of troops, mobilize your troops; for a siege is laid against us! With a rod they will strike the cheek of the judge of Israel.
Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo, pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe. Adzakantha ndi ndodo pa chibwano cha wolamulira wa Israeli.
2 But you, Bethlehem Ephrathah, who are small among the clans of Judah, out of you will come forth for Me One to be ruler over Israel — One whose origins are of old, from the days of eternity.
“Koma iwe Betelehemu Efurata, ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda, mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzalamulira Israeli, amene chiyambi chake nʼchakalekale, nʼchamasiku amakedzana.”
3 Therefore Israel will be abandoned until she who is in labor has given birth; then the rest of His brothers will return to the children of Israel.
Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwa mpaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire. Ndipo abale ake onse otsalira adzabwerera kudzakhala pamodzi ndi Aisraeli.
4 He will stand and shepherd His flock in the strength of the LORD, in the majestic name of the LORD His God. And they will dwell securely, for then His greatness will extend to the ends of the earth.
Iye adzalimbika, ndipo adzaweta nkhosa zake mwa mphamvu ya Yehova, mu ulemerero wa dzina la Yehova Mulungu wake. Ndipo iwo adzakhala mu mtendere, pakuti ukulu wake udzakhala ponseponse pa dziko lapansi.
5 And He will be our peace when Assyria invades our land and tramples our citadels. We will raise against it seven shepherds, even eight leaders of men.
Ndipo Iye adzakhala mtendere wawo. Asiriya akadzalowa mʼdziko lathu ndi kuyamba kuthira nkhondo malo athu otetezedwa, tidzawadzutsira abusa asanu ndi awiri, ngakhalenso atsogoleri asanu ndi atatu.
6 And they will rule the land of Assyria with the sword, and the land of Nimrod with the blade drawn. So He will deliver us when Assyria invades our land and marches into our borders.
Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Asiriya akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu kudzatithira nkhondo.
7 Then the remnant of Jacob will be in the midst of many peoples like dew from the LORD, like showers on the grass, which do not wait for man or linger for mankind.
Otsalira a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvumbi pa udzu, omwe sulamulidwa ndi munthu kapena kudikira lamulo la anthu.
8 Then the remnant of Jacob will be among the nations, in the midst of many peoples, like a lion among the beasts of the forest, like a young lion among flocks of sheep, which tramples and tears as it passes through, with no one to rescue them.
Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu, mʼgulu la anthu a mitundu yambiri, ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango. Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa, amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula, ndipo palibe angathe kuzilanditsa.
9 Your hand will be lifted over your foes, and all your enemies will be cut off.
Mudzagonjetsa adani anu, ndipo adani anu onse adzawonongeka.
10 “In that day,” declares the LORD, “I will remove your horses from among you and wreck your chariots.
Yehova akuti, “Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onse ndi kuphwasula magaleta anu.
11 I will remove the cities of your land and tear down all your strongholds.
Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanu ndi kugwetsa malinga anu onse.
12 I will cut the sorceries from your hand, and you will have no fortune-tellers.
Ndidzawononga ufiti wanu ndipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula.
13 I will also cut off the carved images and sacred pillars from among you, so that you will no longer bow down to the work of your own hands.
Ndidzawononga mafano anu osema pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu; simudzagwadiranso zinthu zopanga ndi manja anu.
14 I will root out the Asherah poles from your midst and demolish your cities.
Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu, ndipo ndidzawononga mizinda yanu.
15 I will take vengeance in anger and wrath upon the nations that have not obeyed Me.”
Ndidzayilanga mwaukali ndi mokwiya mitundu imene sinandimvere Ine.”

< Micah 5 >