< Acts 15 >

1 Then some men came down from Judea and were teaching the brothers, “Unless you are circumcised according to the custom of Moses, you cannot be saved.”
Anthu ena ochokera ku Yudeya anafika ku Antiokeya ndipo amaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuchita mdulidwe potsata mwambo wa Mose, simungapulumuke.”
2 And after engaging these men in sharp debate, Paul and Barnabas were appointed, along with some other believers, to go up to Jerusalem to see the apostles and elders about this question.
Zimenezi zinachititsa Paulo ndi Barnaba kuti atsutsane nawo kwambiri. Kotero Paulo ndi Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi abale ena kuti apite ku Yerusalemu kukaonana ndi atumwi ndi akulu ampingo kukakambirana za nkhaniyi.
3 Sent on their way by the church, they passed through Phoenicia and Samaria, recounting the conversion of the Gentiles and bringing great joy to all the brothers.
Mpingo unawaperekeza, ndipo pamene amadutsa ku Foinike ndi Samariya, iwo anafotokoza momwe a mitundu ina anatembenukira mtima. Nkhani imeneyi inakondweretsa kwambiri abale onse.
4 On their arrival in Jerusalem, they were welcomed by the church and apostles and elders, to whom they reported all that God had done through them.
Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.
5 But some believers from the party of the Pharisees stood up and declared, “The Gentiles must be circumcised and required to obey the law of Moses.”
Kenaka, okhulupirira ena amene kale anali a gulu la Afarisi anayimirira ndipo anati, “Anthu a mitundu ina ayenera kuchita mdulidwe ndi kusunga malamulo a Mose.”
6 So the apostles and elders met to look into this matter.
Atumwi ndi akulu ampingo anasonkhana kuti akambirane za nkhaniyi.
7 After much discussion, Peter got up and said to them, “Brothers, you know that in the early days God made a choice among you that the Gentiles would hear from my lips the message of the gospel and believe.
Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira.
8 And God, who knows the heart, showed His approval by giving the Holy Spirit to them, just as He did to us.
Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife.
9 He made no distinction between us and them, for He cleansed their hearts by faith.
Iye sanasiyanitse pakati pa ife ndi iwo, pakuti anayeretsa mitima yawo mwachikhulupiriro.
10 Now then, why do you test God by placing on the necks of the disciples a yoke that neither we nor our fathers have been able to bear?
Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza?
11 On the contrary, we believe it is through the grace of the Lord Jesus that we are saved, just as they are.”
Osatero! Ife tikukhulupirira kuti tinapulumutsidwa mwachisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, monga iwonso anachitira.”
12 The whole assembly fell silent as they listened to Barnabas and Paul describing the signs and wonders God had done among the Gentiles through them.
Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo.
13 When they had finished speaking, James declared, “Brothers, listen to me!
Iwo atatha kuyankhula, Yakobo anayankhula nati: “Abale, tandimverani.
14 Simon has told us how God first visited the Gentiles to take from them a people to be His own.
Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake.
15 The words of the prophets agree with this, as it is written:
Mawu a aneneri akuvomereza zimenezi, monga kwalembedwa kuti,
16 ‘After this I will return and rebuild the fallen tent of David. Its ruins I will rebuild, and I will restore it,
“‘Zitatha izi Ine ndidzabwerera ndipo ndidzamanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzakonzanso malo amene anagumuka, ndi kuyimanganso,
17 so that the remnant of men may seek the Lord, and all the Gentiles who are called by My name, says the Lord who does these things
kuti anthu otsalawo afunefune Ambuye, ndi anthu onse a mitundu ina amene atchedwa ndi dzina langa, akutero Ambuye, amene amachita zinthu zimenezi
18 that have been known for ages.’ (aiōn g165)
zinaululidwa kuyambira kalekale.’ (aiōn g165)
19 It is my judgment, therefore, that we should not cause trouble for the Gentiles who are turning to God.
“Chifukwa chake, ine ndikuweruza kuti tisamavute anthu a mitundu ina amene atembenuka mtima kutsata Mulungu.
20 Instead, we should write and tell them to abstain from food polluted by idols, from sexual immorality, from the meat of strangled animals, and from blood.
Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi.
21 For Moses has been proclaimed in every city from ancient times and is read in the synagogues on every Sabbath.”
Pakuti malamulo a Mose akhala akulalikidwa mu mzinda uliwonse, kuyambira kalekale ndipo amawerengedwa mʼMasunagoge tsiku la Sabata.”
22 Then the apostles and elders, with the whole church, decided to select men from among them to send to Antioch with Paul and Barnabas. They chose Judas called Barsabbas and Silas, two leaders among the brothers,
Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale,
23 and sent them with this letter: The apostles and the elders, your brothers, To the brothers among the Gentiles in Antioch, Syria, and Cilicia: Greetings.
kuti akapereke kalata yonena kuti, Kuchokera kwa atumwi ndi akulu ampingo, abale anu, Kwa anthu a mitundu ina okhulupirira a ku Antiokeya, Siriya ndi Kilikiya: Tikupereka moni.
24 It has come to our attention that some went out from us without our authorization and unsettled you, troubling your minds by what they said.
Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani.
25 So we all agreed to choose men to send to you along with our beloved Barnabas and Paul,
Tsono ife tagwirizana kuti, tisankhe anthu ena ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa Paulo ndi Barnaba,
26 men who have risked their lives for the name of our Lord Jesus Christ.
anthu amene anapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
27 Therefore we are sending Judas and Silas to tell you in person the same things we are writing.
Nʼchifukwa chake, tikutumiza Yudasi ndi Sila kuti adzachitire umboni ndi mawu a pakamwa pawo za zimene ife talemba.
28 It seemed good to the Holy Spirit and to us not to burden you with anything beyond these essential requirements:
Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi:
29 You must abstain from food sacrificed to idols, from blood, from the meat of strangled animals, and from sexual immorality. You will do well to avoid these things. Farewell.
Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi. Tsalani bwino.
30 So the men were sent off and went down to Antioch, where they assembled the congregation and delivered the letter.
Anthu aja anatumidwa ndipo anafika ku Antiokeya, kumene anasonkhanitsa mpingo pamodzi napereka kalatayo.
31 When the people read it, they rejoiced at its encouraging message.
Anthuwo anawerenga kalatayo ndipo abalewo anakondwa chifukwa cha mawu ake achirimbikitso.
32 Judas and Silas, who themselves were prophets, said much to encourage and strengthen the brothers.
Yudasi ndi Sila amene analinso aneneri, ananena zambiri zowalimbikitsa ndi kuwapatsa mphamvu abalewo.
33 After spending some time there, they were sent off by the brothers in peace to return to those who had sent them.
Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abale aja anatsanzikana nawo mwamtendere kuti abwerere kwa amene anawatuma.
Koma Sila anasankha kuti akhale komweko.
35 But Paul and Barnabas remained at Antioch, along with many others, teaching and preaching the word of the Lord.
Koma Paulo ndi Barnaba anatsalira ku Antiokeya kumene iwo pamodzi ndi ena ambiri anaphunzitsa ndi kulalikira Mawu a Ambuye.
36 Some time later Paul said to Barnabas, “Let us go back and visit the brothers in every town where we proclaimed the word of the Lord, to see how they are doing.”
Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.”
37 Barnabas wanted to take John, also called Mark.
Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo.
38 But Paul thought it best not to take him, because he had deserted them in Pamphylia and had not accompanied them in the work.
Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito.
39 Their disagreement was so sharp that they parted company. Barnabas took Mark and sailed for Cyprus,
Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro.
40 but Paul chose Silas and left, commended by the brothers to the grace of the Lord.
Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka.
41 And he traveled through Syria and Cilicia, strengthening the churches.
Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.

< Acts 15 >