< 1 Timothy 2 >

1 I exhort therefore, first of all, that supplications, prayers, intercessions, thanksgivings, be made for all men,
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika.
2 for kings and all those who are in prominence, so that we may live a quiet and peaceful life in all piety and propriety.
Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.
3 For this is good and acceptable in the sight of God our Savior,
Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu,
4 who wants all men to be saved and to come to knowledge of truth.
amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.
5 For there is one God, and one mediator of God and men, the man Jesus Christ,
Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.
6 who gave himself a ransom for all, the testimony for their own times.
Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera.
7 For which I was appointed a herald and an apostle (I speak the truth in Christ, I do not lie), a teacher of Gentiles in faith and truth.
Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.
8 I desire therefore the men to pray in every place, lifting up devout hands, apart from anger and argument.
Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.
9 And similarly, the women to adorn themselves in disciplined decorum, with reverence and sobriety, not with braided hair or gold or pearls or expensive apparel,
Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.
10 but (which is fitting for women professing godliness) through good works.
Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.
11 Let a woman learn in silence in all subjection.
Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu.
12 But I do not allow a woman to teach, nor to have authority of a man, but to be in quietness.
Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete.
13 For Adam was first formed, then Eve.
Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava.
14 And Adam was not deceived, but the woman, having been deceived, became in transgression.
Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa.
15 But she will be saved through childbearing, if they continue in faith and love and sanctification with sobriety.
Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.

< 1 Timothy 2 >