< 1 Chronicles 1 >
2 Kenan, Mahalalel, Jared,
Kenani, Mahalaleli, Yaredi,
3 Enoch, Methuselah, Lamech,
Enoki, Metusela, Lameki, Nowa.
4 Noah, Shem, Ham, and Japheth.
Ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti.
5 The sons of Japheth: Gomer, and Magog, and Madai, and Javan, and Tubal, and Meshech, and Tiras.
Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
6 And the sons of Gomer: Ashkenaz, and Diphath, and Togarmah.
Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima
7 And the sons of Javan: Elishah, and Tarshish, Kittim, and Rodanim.
Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
8 The sons of Ham: Cush, and Mizraim, Put, and Canaan.
Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani
9 And the sons of Cush: Seba, and Havilah, and Sabta, and Raama, and Sabteca. And the sons of Raamah: Sheba, and Dedan.
Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani.
10 And Cush begot Nimrod; he began to be a mighty one on the earth.
Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.
11 And Mizraim begot Ludim, and Anamim, and Lehabim, and Naphtuhim,
Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
12 and Pathrusim, and Casluhim (from whence came the Philistines), and Caphtorim.
Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori.
13 And Canaan begot Sidon his firstborn, and Heth,
Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti,
14 and the Jebusite, and the Amorite, and the Girgashite,
Ayebusi, Aamori, Agirigasi
15 and the Hivite, and the Arkite, and the Sinite,
Ahivi, Aariki, Asini
16 and the Arvadite, and the Zemarite, and the Hamathite.
Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
17 The sons of Shem: Elam, and Asshur, and Arphaxad, and Lud, and Aram, and Uz, and Hul, and Gether, and Meshech.
Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
18 And Arphaxad begot Shelah, and Shelah begot Eber.
Aripakisadi anabereka Sela ndipo Selayo anabereka Eberi:
19 And to Eber were born two sons. The name of the one was Peleg, for in his days the earth was divided. And his brother's name was Joktan.
Eberi anabereka ana aamuna awiri: wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
20 And Joktan begot Almodad, and Sheleph, and Hazarmaveth, and Jerah,
Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
21 and Hadoram, and Uzal, and Diklah,
Hadoramu, Uzali, Dikila
22 and Ebal, and Abimael, and Sheba,
Obali, Abimaeli, Seba,
23 and Ophir, and Havilah, and Jobab; all these were the sons of Joktan.
Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
24 Shem, Arphaxad, Shelah,
Semu, Aripakisadi, Sela
27 Abram (the same is Abraham).
ndi Abramu (amene ndi Abrahamu).
28 The sons of Abraham: Isaac and Ishmael.
Ana a Abrahamu ndi awa: Isake ndi Ismaeli.
29 These are their generations: the firstborn of Ishmael, Nebaioth, then Kedar, and Adbeel, and Mibsam,
Zidzukulu zake zinali izi: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu,
30 Mishma, and Dumah, Massa, Hadad, and Tema,
Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema,
31 Jetur, Naphish, and Kedemah. These are the sons of Ishmael.
Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli.
32 And the sons of Keturah, Abraham's concubine: she bore Zimran, and Jokshan, and Medan, and Midian, and Ishbak, and Shuah. And the sons of Jokshan: Sheba, and Dedan.
Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa: Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. Ana a Yokisani ndi awa: Seba ndi Dedani
33 And the sons of Midian: Ephah, and Epher, and Hanoch, and Abida, and Eldaah. All these were the sons of Keturah.
Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura.
34 And Abraham begot Isaac. The sons of Isaac: Esau and Israel.
Abrahamu anabereka Isake. Ana a Isake anali awa: Esau ndi Israeli.
35 The sons of Esau: Eliphaz, Reuel, and Jeush, and Jalam, and Korah.
Ana aamuna a Esau anali awa: Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora.
36 The sons of Eliphaz: Teman, and Omar, Zephi, and Gatam, Kenaz, and Timna, and Amalek.
Ana a Elifazi anali awa: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi: Amene anabereka ndi Timna: Amaleki.
37 The sons of Reuel: Nahath, Zerah, Shammah, and Mizzah.
Ana a Reueli anali awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza.
38 And the sons of Seir: Lotan, and Shobal, and Zibeon, and Anah, and Dishon, and Ezer, and Dishan.
Ana a Seiri anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.
39 And the sons of Lotan: Hori, and Homam. And Timna was Lotan's sister.
Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
40 The sons of Shobal: Alian, and Manahath, and Ebal, Shephi, and Onam. And the sons of Zibeon: Aiah, and Anah.
Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana.
41 The sons of Anah: Dishon. And the sons of Dishon: Hamran, and Eshban, and Ithran, and Cheran.
Mwana wa Ana anali Disoni. Ana a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani
42 The sons of Ezer: Bilhan, and Zaavan, Jaakan. The sons of Dishan: Uz, and Aran.
Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Yaakani. Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani.
43 Now these are the kings that reigned in the land of Edom before any king reigned over the sons of Israel: Bela the son of Beor. And the name of his city was Dinhabah.
Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko: Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
44 And Bela died, and Jobab the son of Zerah of Bozrah reigned in his stead.
Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
45 And Jobab died, and Husham of the land of the Temanites reigned in his stead.
Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake.
46 And Husham died, and Hadad the son of Bedad, who smote Midian in the field of Moab, reigned in his stead. And the name of his city was Avith.
Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
47 And Hadad died, and Samlah of Masrekah reigned in his stead.
Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake.
48 And Samlah died, and Shaul of Rehoboth by the River reigned in his stead.
Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake.
49 And Shaul died, and Baal-hanan the son of Achbor reigned in his stead.
Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
50 And Baal-hanan died, and Hadad reigned in his stead. And the name of his city was Pai, and his wife's name was Mehetabel, the daughter of Matred, the daughter of Me-zahab.
Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
51 And Hadad died. And the chiefs of Edom were: chief Timna, chief Aliah, chief Jetheth,
Hadadi anamwaliranso. Mafumu a ku Edomu anali: Timna, Aliva, Yeteti,
52 chief Oholibamah, chief Elah, chief Pinon,
Oholibama, Ela, Pinoni,
53 chief Kenaz, chief Teman, chief Mibzar,
Kenazi, Temani, Mibezari,
54 chief Magdiel, chief Iram. These are the chiefs of Edom.
Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu.