< Jeremias 50 >
1 Det ord Herren talte mod Babel, mod kaldærenes land, ved profeten Jeremias.
Uthenga umene Yehova anayankhula ndi mneneri Yeremiya wonena za mzinda wa Babuloni ndi anthu ake ndi uwu:
2 Forrkynd det blandt Folkene, kundgør det, rejs et Banner, kundgør det, dølg det ikke, sig: Babel er indtaget, Bel gjort til Skamme, Merodak knust, til Skamme er dets Afguder blevet, knust dets Afgudsbilleder.
“Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina, kweza mbendera ndipo ulengeze; usabise kanthu, koma uwawuze kuti, ‘Babuloni wagwa; mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi, nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha. Milungu yake yagwidwa ndi mantha ndipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’
3 Thi et Folk fra Nord drager op imod det og gør dets Land til en Ørken, så ingen bor der; både Mennesker og Dyr er flygtet.
Mtundu wa anthu wochokera kumpoto wadzathira nkhondo Babuloni ndi kusandutsa bwinja dziko lake. Kumeneko sikudzakhalanso munthu kapena nyama.
4 I hine Dage og til hin Tid, lyder det fra HERREN, skal israeliterne, sammen med Judæerne, komme: de skal vandre under Gråd og søge HERREN deres Gud;
“Masiku amenewo, nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yuda onse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna.
5 de skal spørge om Vej til Zion, did er deres Ansigtervendt; de skal komme og klynge sig til HERREN i en evig Pagt, der aldrig glemmes.
Adzafunsa njira ya ku Ziyoni ndi kuyamba ulendo wopita kumeneko. Iwo adzadzipereka kwa Yehova pochita naye pangano lamuyaya limene silidzayiwalika.
6 En Flok bortkomne Får var mit Folk, deres Hyrder havde ført dem vild, på Afveje i Bjergene; de flakkede fra Bjerg til Høj, glemte deres Hvilested.
“Anthu anga ali ngati nkhosa zotayika; abusa awo anawasocheretsa mʼmapiri. Iwo anayendayenda mʼmapiri ndi mʼzitunda mpaka kuyiwala kwawo.
7 Enhver, som traf på dem, fortærede dem; deres Fjender sagde: "Vi er sagesløse!" Det skete, fordi de syndede mod HERREN, Retfærds græsgangen og deres fædres Håb, HERREN.
Aliyense amene anawapeza anawawononga; adani awo anati, ‘Ife si olakwa, chifukwa iwo anachimwira Yehova, amene ali mpumulo wawo weniweni ndi amene makolo awo anamukhulupirira.’
8 Fly ud af Babel, drag bort fra kaldæernes Land, bliv som Bukke foran en Hjord!
“Thawaniko ku Babuloni; chokani mʼdziko la Ababuloni. Muyambe inu kutuluka ngati atonde amene amatsogolera ziweto.
9 Thi se, jeg vækker fra Nordens Land en Sværm af vældige Folk og fører dem frem mod Babel, og de skal ruste sig imod det; fra den Kant skal det indtages; dens Pile er som den sejrsæle Helts, der ikke vender tomhændet hjem.
Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto kudzamenyana ndi Babuloni. Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni. Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso, yosapita padera.
10 Kaldæa gøres til Bytte; alle, som gør det til Bytte, mættes, lyder det fra HERREN.
Motero Ababuloni adzafunkhidwa; ndipo onse omufunkha adzakhuta,” akutero Yehova.
11 Glæd eder kun og jubl, I, som plyndrede min Arvelod, spring som Kalve i Engen, vrinsk som Hingste
“Inu Ababuloni, munawononga anthu anga osankhika. Ndiye pano mukukondwa, mukusangalala. Mukulumphalumpha mokondwa ngati mwana wangʼombe wopuntha tirigu ndiponso mukulira monyada ngati ngʼombe zazimuna.
12 eders Moder skal dybt beskæmmes; hun, som bar eder, skal blive til Skamme. Se, det ringeste af Folkene, en Ørken, tørt Land og Ødemark!
Koma mzinda wanu udzachititsidwa manyazi kwambiri. Mzinda umene uli ngati mayi wanu udzanyazitsidwa. Babuloni adzasanduka chitsirizira cha anthu onse. Mzinda wawo udzakhala ngati thengo, ngati dziko lowuma lachipululu.
13 For HERRENs Vredes Skyld skal det ligge ubeboet hen og overalt være en Ørken; alle, som kommer forbi Babel, skal slås af Rædsel og spotte over alle dets Sår.
Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova Babuloni adzakhala wopanda anthu ndipo adzakhala chipululu chokhachokha. Onse odutsa kumeneko adzachita mantha ndipo azidzangotsonya chifukwa cha chiwonongeko chake chachikulu.
14 Rust eder mod Babel på alle Kanter, alle, som spænder Bue; skyd på det, spar ikke på Pile, thi mod HERREN har det syndet.
“Inu okoka uta, konzekani kuti muthire nkhondo mzinda wa Babuloni mbali zonse. Muponyereni mivi yanu yonse chifukwa anachimwira Yehova.
15 Jubl over det fra alle kanter: "Det har udrakt sin Hånd, dets Støttemure er faldet, dets Volde nedbrudt." Thi det er HERRENs Hævn. Hævn eder på det, gør med det, som det selv har gjort!
Mufuwulireni mbali zonse pakuti wagonja. Nsanja zake zagwa. Malinga ake agwetsedwa. Kumeneku ndiko kulipsira kwa Yehova. Mulipsireni, mumuchite zomwe iye anachitira anthu ena.
16 Udryd af Babel den, der sår, og den, der svinger Le i Høstens Tid! For det hærgende Sværd vender enhver hjem til sit Folk, enhver flyr til sit Land.
Chotsani ku Babuloni munthu wofesa mbewu aliyense, ndiponso wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthawi yokolola. Poona lupanga la ozunza anzawo, aliyense adzabwerera kwa anthu ake; adzathawira ku dziko la kwawo.
17 En adsplittet Hjord er Israel, Løver har spredt det. Først fortærede Assyrerkongen det, og nu sidst har Kong Nebukadrezar af Babel gnavet dets Knogler.
“Aisraeli ali ngati nkhosa zomwe zabalalika pothamangitsidwa ndi mikango. Mfumu ya ku Asiriya ndiye inayamba kuwapha Aisraeliwo. Wotsiriza anali Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni amene anachita ngati kuphwanya mafupa ake.”
18 Derfor, så siger Hærskarers HERRE, Israels Gud: Se, jeg hjemsøger Babels Konge og hans Land, som jeg hjemsøgte Assyrerkongen;
Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi dziko lake monga momwe ndinalangira mfumu ya ku Asiriya.
19 og jeg fører Israel tilbage til dets Græsgang; det skal græsse på Karmel og Basan og mættes i Efraims Bjerge og Gilead.
Koma ndidzabwezera Israeli ku msipu wake ndipo adzadya mʼminda ya ku Karimeli ndi Basani; adzadya nakhuta ku mapiri a ku Efereimu ndi Giliyadi.
20 I hine Dage og til hin Tid, lyder det fra HERREN, skal man søge efter Israels Brøde, og den er der ikke, efter Judas Synder, og de findes ikke; thi jeg tilgiver dem, jeg lader blive til Rest,
Masiku amenewo, nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “anthu adzafunafuna zolakwa za Israeli koma sadzapeza nʼchimodzi chomwe, ndipo adzafufuza machimo a Yuda, koma sadzapeza ndi limodzi lomwe, chifukwa otsala amene ndawasiya ndidzawakhululukira.
21 Drag op mod Meratajims Land, drag op imod det og mod dem, som bor i Pekod, læg øde, læg Band på dem, så lyder det fra HERREN, gør nøje, som jeg har budt dig!
“Lithireni nkhondo dziko la Merataimu ndi anthu okhala ku Pekodi. Muwaphe ndi lupanga ndi kuwawonongeratu,” akutero Yehova. “Chitani zonse monga momwe ndakulamulani.
22 Krigslarm lyder i Landet, alt bryder sammen.
Mʼdziko muli phokoso la nkhondo, phokoso la chiwonongeko chachikulu!
23 Hvor er dog al Jordens Hammer knækket og brudt, hvor er dog Babel blevet til Rædsel blandt Folkene!
Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekera uja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi. Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ina!
24 Jeg lagde dig Snarer, du fangedes, Babel, og mærked det ej; du grebes, og fast blev du holdt, thi du kæmped mod HERREN.
Ndinakutchera msampha, iwe Babuloni, ndipo wakodwamo iwe wosazindikira kanthu; unapezeka ndiponso unakodwa chifukwa unalimbana ndi Yehova.
25 HERREN lukked op for sit Forråd og fremtog sin Vredes Værktøj. Thi et Værk har Herren, Hærskarers HERRE, for i Kaldæernes Land.
Yehova watsekula nyumba ya zida zake ndipo watulutsa zida za ukali wake, pakuti Ambuye Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ntchito yoti agwire mʼdziko la Ababuloni.
26 Træng derind fra Ende til anden, luk op for dets Lader, dyng det op som Neg og læg Band derpå, lad intet levnes.
Mumenyane naye Babuloni mbali zonse. Anthu ake muwawunjike ngati milu ya tirigu. Muwawononge kotheratu ndipo pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.
27 ødelæg alle dets Okser, før dem ned til Slagtning! Ve dem, deres Dag er kommet, Hjemsøgelsens Tid.
Iphani ankhondo ake onse. Onse aphedwe ndithu. Tsoka lawagwera pakuti tsiku lawo lachilango lafika.
28 Hør, hvor de flyr og redder sig fra Babels Land for at melde i Zion om Hævnen fra HERREN vor Gud, Hævn for hans Helligdom.
Tikumva anthu othawa nkhondo ochokera ku Babuloni akulengeza mu Yerusalemu za kulipsira kwa Yehova Mulungu wathu. Iye akulipsira chifukwa chowononga Nyumba yake.
29 Kald Skytterne sammen mod Babel, enhver, som spænder Bue, slå Ring omkring det, lad ingen få Lov at slippe; gengæld det efter dets Gerning; efter alt, hvad det gjorde, skal I gøre imod det; thi Frækhed viste det mod HERREN, Israels Hellige.
“Itanani anthu oponya mivi kudzathira nkhondo Babuloni. Muyitanenso onse amene amakoka mauta. Mangani misasa ya nkhondo momuzungulira; musalole munthu aliyense kuthawa. Muchiteni monga momwe iye anachitira anthu ena. Iyeyu ananyoza Yehova, Woyera wa Israeli.
30 Derfor falder dets Ynglinge på dets Torve, alle Krigsfolkene omkommer på hin Dag, lyder det fra HERREN.
Nʼchifukwa chake, anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo ake; ankhondo ake onse adzaphedwa tsiku limenelo,” akutero Yehova.
31 Se, jeg kommer over dig, "Frækhed", lyder det fra Herren, Hærskarers HERRE, thi din Dag er kommet, Hjemsøgelsens Tid.
“Taona, ndikukuthira nkhondo, iwe wodzikuzawe,” akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, “chifukwa tsiku lako lafika, nthawi yoti ndikulange yakwana.
32 Da falder "Frækhed" og styrter, og ingen rejser det. Jeg sætter Ild på dets Byer, og den fortærer alt deromkring.
Wodzikuzawe udzapunthwa nʼkugwa ndipo palibe amene adzakudzutse; ndidzayatsa moto mʼmizinda yake umene udzanyeketsa onse amene amuzungulira.”
33 Så siger Hærskarers HERRE: Både med Israeliterne og Judæerne er der handlet ilde; alle de, der bortførte dem, holder fast på dem, vægrer sig ved at give dem fri.
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a ku Israeli akuzunzidwa, pamodzi ndi anthu a ku Yuda, ndipo onse amene anawagwira ukapolo awagwiritsitsa, akukana kuwamasula.
34 Deres Genløser er stærk, Hærskarers HERRE er hans Navn; han vil føre deres Strid og give Jorden Ro og Babels Indbyggere Uro.
Koma Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu; dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. Iye adzawateteza molimba pa mlandu wawo nʼcholinga choti abweretse mtendere mʼdziko lawo, koma adzavutitsa okhala ku Babuloni.”
35 Sværd over Kaldæerne, lyder det fra HERREN, og over Babels Indbyggere, over dets Fyrster og Vismænd!
Yehova akuti, “Imfa yalunjika pa Ababuloni, pa akuluakulu ake ndi pa anthu ake a nzeru!
36 Sværd over Sandsigerne, så de bliver Tåber! Sværd over dets Belte, så de taber Modet!
Imfa yalunjika pa aneneri abodza kuti asanduke zitsiru. Imfa yalunjika pa ankhondo ake kuti agwidwe ndi mantha aakulu.
37 Sværd over dets Heste og Vogne og over alt det blandede Slæng i dets Midte, så de bliver til Kvinder! Sværd over dets Skatte, så de plyndres!
Imfa ilunjike pa akavalo ake ndi magaleta ake. Ilunjikanso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pawo kuti asanduke ngati akazi. Chiwonongeko chilunjikenso pa chuma chake kuti chidzafunkhidwe.
38 Tørke over dets Vande, så de tørres ud! Thi det er et Land for Gudebilleder, og de gør sig til af dem, de frygter.
Chilala chilunjike pa madzi ake kuti aphwe. Babuloni ndi dziko la mafano, ndipo anthu afika poyaluka nawo mafanowo.
39 Derfor skal Ørkendyr bo der sammen med Sjakaler, også Strudse skal bo der; aldrig mer skal det bebos, men være ubeboet fra Slægt til Slægt.
“Nʼchifukwa chake nyama zakuthengo ndi afisi zidzakhala kumeneko ndipo kudzakhalanso akadzidzi. Kumeneko sikudzapezekako anthu, ndithu anthu sadzakhalako pa mibado yonse.
40 Som det gik, da Gud omstyrtede Sodoma og Gomorra og Nabobyerne, lyder det fra HERREN, skal intet Menneske bo der, intet Menneskebarn dvæle der.
Monga momwe Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora pamodzi ndi mizinda yonse yozungulira,” akutero Yehova, “momwemonso palibe amene adzakhale kumeneko; anthu sadzayendanso mʼmenemo.
41 Se, der kommer et Folk fra Nord, et vældigt Folk og mange Konger bryder op fra det yderste af Jorden.
“Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri, wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
42 De fører Bue og Spyd, er grumme uden Barmhjertighed, deres Røst er som Havets Brusen, de rider på Heste, rustet som en Mand til Strid mod dig, Babels Datter!
Atenga mauta ndi mikondo; ndi anthu ankhanza ndipo alibe chifundo. Phokoso lawo likumveka ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo awo, ndipo akonzekera kudzakuthira nkhondo iwe Babuloni.
43 Babels Konge hørte Rygtet derom, og hans Hænder blev slappe, Rædsel greb ham, Skælven som den fødende Kvindes.
Mfumu ya ku Babuloni yamva za mbiri yawo, ndipo yalobodokeratu. Ikuda nkhawa, ikumva ululu ngati wa mayi pa nthawi yake yochira.
44 Som en Løve, der fra Jordans Stolthed skrider op til den stedsegrønne Græsgang, således vil jeg i et Nu drive dem bort derfra. Thi hvem er den udvalgte, jeg vil sætte over dem? Thi hvem er min Lige, og hvem kræver mig til Regnskab? Hvem er den Hyrde, der står sig mod mig?
Taonani, monga mkango wochokera ku nkhalango ya ku Yorodani kupita ku msipu wobiriwira, momwemonso ine ndidzapirikitsa Babuloni mʼdziko lake mwadzidzidzi. Pambuyo pake ndidzawayikira wowalamulira amene ndamufuna Ine. Wofanana nane ndani ndipo ndani amene angalimbane nane? Ndi mtsogoleri wa dziko uti amene anganditengere ku bwalo la milandu?”
45 Hør derfor det Råd, HERREN har for mod Babel, og de Tanker, han har tænkt mod Kaldæernes Land: Visselig skal Hjordens ringeste slæbes bort, visselig skal deres Græsgang forfærdes over dem.
Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Babuloni. Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
46 Ved Råbet: "Babel er indtaget!" skal Jorden skælve, og deres Skrig skal høres blandt Folkene.
Akadzagwa Babuloni padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera, ndipo kulira kwawo kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.