< 2 Mosebog 20 >

1 Gud talede alle disse Ord og sagde:
Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati:
2 Jeg er HERREN din Gud, som førte dig ud af Ægypten, af Trællehuset.
“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.
3 Du må ikke have andre Guder end mig.
“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.”
4 Du må ikke gøre dig noget udskåret Billede eller noget Afbillede af det, som er oppe i Himmelen eller nede på Jorden eller i Vandet under Jorden;
“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko.
5 du må ikke tilbede eller dyrke det, thi jeg HERREN din Gud er en nidkær Gud, der indtil tredje og fjerde Led straffer Fædres Brøde på Børn af dem, som hader mig,
Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.
6 men i tusind Led viser Miskundhed mod dem, der elsker mig og holder mine Bud!
Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga.
7 Du må ikke misbruge HERREN din Guds Navn, thi HERREN lader ikke den ustraffet, der misbruger hans Navn!
“Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.
8 Kom Hviledagen i Hu, så du holder den hellig!
“Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.
9 I seks Dage skal du arbejde og gøre al din Gerning,
Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi.
10 men den syvende Dag skal være Hviledag for HERREN din Gud; da må du intet Arbejde udføre, hverken du selv, din Søn eller Datter, din Træl eller Trælkvinde, dit Kvæg eller den fremmede inden dine Porte.
Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu.
11 Thi i seks Dage gjorde HERREN Himmelen, Jorden og Havet med alt, hvad der er i dem, og på den syvende Dag hvilede han; derfor har HERREN velsignet Hviledagen og helliget den.
Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.
12 Ær din Fader og din Moder, for at du kan få et langt Liv i det Land, HERREN din Gud vil give dig!
“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
13 Du må ikke slå ihjel!
“Usaphe.
14 Du må ikke bedrive Hor!
“Usachite chigololo.
15 Du må ikke stjæle!
“Usabe.
16 Du må ikke sige falsk Vidnesbyrd imod din Næste!
“Usapereke umboni womunamizira mnzako.
17 Du må ikke begære din Næstes Hus! Du må ikke begære din Næstes Hustru, hans Træl eller Trælkvinde, hans Okse eller Æsel eller noget, der hører din Næste til!
“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”
18 Men da hele Folket fornam Tordenen, Lynene og Stødene i Hornene og så det rygende Bjerg forfærdedes Folket og holdt sig skælvende i Frastand;
Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali.
19 og de sagde til Moses: "Tal du med os, så vil vi lytte til; men lad ikke Gud tale med os, at vi ikke skal dø!"
Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.”
20 Men Moses svarede Folket: "Frygt ikke, thi Gud er kommet for at prøve eder, og for at I kan lære at frygte for ham, så I ikke synder."
Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.”
21 Da holdt Folket sig i Frastand medens Moses nærmede sig Mulmet, hvori Gud var.
Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu.
22 HERREN sagde da til Moses: Således skal du sige til Israeliterne: I har selv set, at jeg har talet med eder fra Himmelen!
Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba.
23 I må ikke gøre eder Guder ved Siden af mig; Guder af Sølv eller Guld må I ikke gøre eder!
Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’”
24 Du skal bygge mig et Alter af Jord, og på det skal du ofre dine Brændofre og Takofre, dit Småkvæg og dit Hornkvæg; på ethvert Sted, hvor jeg lader mit Navn ihukomme, vil jeg komme til dig og velsigne dig.
Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani.
25 Men hvis du opfører mig Altre af Sten, må du ikke bygge dem af tilhugne Sten, thi når du svinger dit Værktøj derover, vanhelliger du dem.
Ngati mudzandimangira guwa lansembe lamiyala, musagwiritse ntchito miyala yosema, pakuti mudzalidetsa mukadzagwiritsa ntchito zida.
26 Du må ikke stige op til mit, Alter ad Trin, for at ikke din Blusel skal blottes over det.
Musamakwere pa makwerero popita pa guwa langa lansembe kuti mungaonetse maliseche anu.

< 2 Mosebog 20 >