< Efeserne 5 >
1 Vorder derfor Guds Efterlignere som elskede Børn,
Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu.
2 og vandrer i Kærlighed, ligesom også Kristus elskede os og gav sig selv hen for os som en Gave og et Slagtoffer, Gud til en velbehagelig Lugt.
Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.
3 Men Utugt og al Urenhed eller Havesyge bør end ikke nævnes iblandt eder, som det sømmer sig for hellige,
Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu.
4 ej heller ublu Væsen eller dårlig Snak eller letfærdig Skæmt, hvilket er utilbørligt, men hellere Taksigelse.
Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika.
5 Thi dette vide og erkende I, at ingen utugtig eller uren eller havesyg, hvilket er en Afgudsdyrker, har Arv i Kristi og Guds Rige.
Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.
6 Ingen bedrage eder med tomme Ord; thi for disse Ting kommer Guds Vrede over Genstridighedens Børn.
Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera.
7 Derfor, bliver ikke meddelagtige med dem!
Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.
8 Thi I vare forhen Mørke, men nu ere I Lys i Herren; vandrer som Lysets Børn;
Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika
9 (Lysets Frugt viser sig jo i al Godhed og Retfærdighed og Sandhed, )
(pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi).
10 så I prøve, hvad der er velbehageligt for Herren.
Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye.
11 Og haver ikke Samfund med Mørkets ufrugtbare Gerninger. Men revser dem hellere;
Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse.
12 thi hvad der lønligt bedrives af dem, er skammeligt endog at sige;
Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri.
13 men alt dette bliver åbenbaret, når det revses af Lyset. Thi alt det, som bliver åbenbaret, er Lys.
Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala.
14 Derfor hedder det: "Vågn op, du, som sover, og stå op fra de døde, og Kristus skal lyse for dig!"
Nʼchifukwa chake Malemba akuti, “Dzuka, wamtulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuwalira.”
15 Ser derfor nøje til, hvorledes I vandre, ikke som uvise, men som vise,
Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru.
16 så I købe den belejlige Tid, efterdi Dagene ere onde.
Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa.
17 Derfor bliver ikke uforstandige, men skønner, hvad Herrens Villie er.
Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite.
18 Og drikker eder ikke drukne i Vin, i hvilket der er Ryggesløshed, men lader eder fylde med Ånden,
Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.
19 så I tale hverandre til med Salmer og Lovsange og åndelige Viser og synge og spille i eders Hjerte for Herren
Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu.
20 og altid sige Gud og Faderen Tak for alle Ting i vor Herres Jesu Kristi Navn
Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
21 og underordne eder under hverandre i Kristi Frygt;
Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.
22 Hustruerne skulle underordne sig under deres egne Mænd, som under Herren;
Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye.
23 thi en Mand er sin Hustrus Hoved, ligesom også Kristus er Menighedens Hoved. Han er sit Legemes Frelser.
Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake.
24 Dog, ligesom Menigheden underordner sig under Kristus, således skulle også Hustruerne underordne sig under deres Mænd i alle Ting.
Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse.
25 I Mænd! elsker eders Hustruer, ligesom også Kristus elskede Menigheden og hengav sig selv for den,
Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo
26 for at han kunde hellige den, idet han rensede den ved Vandbadet med et Ord,
kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake.
27 for at han selv kunde fremstille Menigheden for sig som herlig, uden Plet eller Rynke eller noget deslige, men for at den måtte være hellig og ulastelig.
Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro.
28 Således ere Mændene skyldige at elske deres egne Hustruer som deres egne Legemer; den, som elsker sin egen Hustru, elsker sig selv.
Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha.
29 Ingen har jo nogen Sinde hadet sit eget Kød, men han nærer og plejer det, ligesom også Kristus Menigheden.
Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake
30 Thi vi ere Lemmer på hans Legeme.
pakuti ndife ziwalo za thupi lake.
31 Derfor skal et Menneske forlade sin Fader og Moder og holde fast ved sin Hustru, og de to skulle være eet Kød.
“Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”
32 Denne Hemmelighed er stor - jeg sigter nemlig til Kristus og til Menigheden.
Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo.
33 Dog, også I skulle elske hver især sin egen Hustru som sig selv; men Hustruen have Ærefrygt for Manden!
Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.