< Jeremias 49 >

1 Om Ammoniterne. Saa siger HERREN: Har Israel ingen Sønner, eller har det ingen Arving? Hvorfor har Milkom taget Gad i Eje og hans Folk bosat sig i dets Byer?
Yehova ananena izi: Amoni, “Kodi Israeli alibe ana aamuna? Kapena alibe mlowamʼmalo? Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi? Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
2 Se, derfor skal Dage komme, lyder det fra HERREN, da jeg lader Krigsskrig lyde mod Rabba i Ammon, og det skal blive en Grusdynge, og dets Døtre skal gaa op i Luer. Da arver Israel sine Arvinger, siger HERREN.
Koma nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo ku Raba, likulu la Amoni; ndipo malo awo opembedzera milungu yawo adzatenthedwa ndi moto. Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,” akutero Yehova.
3 Klag, Hesjbon, thi Aj er ødelagt; skrig, I Rabbas Døtre, klæd jer i Sæk og klag, gaa rundt i Foldene! Thi Milkom vandrer i Landflygtighed, hans Præster og Fyrster til Hobe.
“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika! Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba! Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu; thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga, chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
4 Hvorfor gør du dig til af dine Dale, du frafaldne Datter, som stoler paa dine Skatte og siger: »Hvem kan komme til mig?«
Chifukwa chiyani mukunyadira chigwa chanu, inu anthu osakhulupirika amene munadalira chuma chanu nʼkumati: ‘Ndani angandithire nkhondo?’
5 Se, jeg lader Rædsel komme over dig fra alle Kanter, lyder det fra Hærskarers HERRE. I skal drives bort i hver sin Retning, og ingen samler de flygtende.
Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe zochokera kwa onse amene akuzungulira,” akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse. “Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake. Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.
6 Men siden vender jeg Ammoniternes Skæbne, lyder det fra HERREN.
“Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,” akutero Yehova.
7 Om Edom. Saa siger Hærskarers HERRE: Er der ikke mer Visdom i Teman, svigter de kloges Raad, er deres Visdom raadden?
Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu: “Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani? Kodi anzeru analeka kupereka uphungu? Kodi nzeru zawo zinatheratu?
8 Fly, søg Ly i det dybe, I, som bor i Dedan! Thi Esaus Ulykke sender jeg over ham, Straffens Tid.
Inu anthu a ku Dedani, thawani, bwererani ndi kukabisala ku makwalala chifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esau popeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.
9 Gæstes du af Vinhøstmænd, levner de ej Efterslæt, af Tyve om Natten, ødelægger de, hvad de lyster.
Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha? Anthu akuba akanafika usiku akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
10 Thi selv blotter jeg Esau, hans Skjulesteder røber jeg; at gemme sig evner han ikke. Han er ødelagt ved Brødres og Naboers Arm, han er borte.
Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau. Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo, kotero kuti sadzathanso kubisala. Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka. Palibe wonena kuti,
11 Lad mig om dine faderløse, jeg holder dem i Live, dine Enker kan stole paa mig.
‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza. Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’”
12 Thi saa siger HERREN: Se, de, hvem det ikke tilkom at tømme Bægeret, maa tømme det, og du skulde gaa fri? Du gaar ikke fri, men kommer til at tømme det.
Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho.
13 Thi jeg sværger ved mig selv, lyder det fra HERREN: til Rædsel og Spot, til Ørk og til et Forbandelsens Tegn skal Bozra blive, og alle dets Byer skal blive til evige Tomter.
Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
14 Fra HERREN har jeg hørt en Tidende: Et Bud skal sendes ud blandt Folkene: Samler eder! Drag ud imod det og rejs jer til Strid!
Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova: Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti, “Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu! Konzekerani nkhondo!”
15 Se, ringe har jeg gjort dig iblandt Folkene, foragtet blandt Mennesker.
“Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina. Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.
16 Rædsel over dig! Dit Hjertes Overmod bedrog dig. Du, som bor i Klippekløft og klynger dig til Fjeldtop: Bygger du Rede højt som Ørnen, jeg styrter dig ned, saa lyder det fra HERREN.
Kuopseza kwako kwakunyenga; kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri. Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.
17 Edom skal blive til Rædsel; alle, der kommer forbi, skal slaas af Rædsel og spotte over alle dets Saar.
“Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake.
18 Som det gik, da Sodoma og Gomorra og Nabobyerne omstyrtedes, siger HERREN, skal intet Menneske bo der, intet Menneskebarn dvæle der.
Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora, pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,” akutero Yehova, “motero palibe munthu amene adzakhala mu Edomu.
19 Som en Løve, der fra Jordans Stolthed skrider op til den stedsegrønne Græsgang, saaledes vil jeg i et Nu drive dem bort derfra. Thi hvem er den udvalgte, jeg vil sætte over dem? Thi hvem er min Lige, og hvem kræver mig til Regnskab? Hvem er den Hyrde, der staar sig mod mig?
“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani kupita ku malo a msipu wobiriwira, Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo. Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine. Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani? Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
20 Hør derfor det Raad, HERREN har for mod Edom, og de Tanker, han har mod Temans Indbyggere: Visselig skal Hjordens ringeste slæbes bort, visselig skal deres Græsgang forfærdes over dem.
Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani. Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
21 Ved Braget af deres Fald skal Jorden skælve; Skriget kan høres til det røde Hav.
Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera; kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
22 Se, som en Ørn med udbredte Vinger svæver han over Bozra; og Edoms Heltes Hjerte bliver paa hin Dag som en nødstedt Kvindes Hjerte.
Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
23 Om Damaskus. Til Skamme er Hamat og Arpad, thi de hører ond Tidende; de er ude af sig selv, i Uro som Havet, der ikke kan falde til Ro.
Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa: “Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha chifukwa amva nkhani yoyipa. Mitima yawo yagwidwa ndi mantha ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
24 Damaskus er modfaldent, vender sig til Flugt, Angst falder over det, Vaande og Veer griber det som en fødende Kvinde.
Anthu a ku Damasiko alefuka. Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu. Ali ndi nkhawa komanso mantha ngati za mayi pa nthawi yake yochira.
25 Ve det! Forladt er den lovpriste By, Glædens Stad.
Mzinda wotchuka ndi wachikondwerero uja wasiyidwa!
26 Derfor falder dets Ynglinge paa dets Torve, alle Krigsfolkene omkommer paa hin Dag, lyder det fra Hærskarers HERRE.
Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa; ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
27 Jeg sætter Ild paa Damaskus's Mur, og den skal fortære Benhadads Borge.
“Ndidzatentha malinga a Damasiko; moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”
28 Om Kedar og Hazors Riger, som Kong Nebukadrezar af Babel slog. Saa siger HERREN: Kom og drag op mod Kedar, ødelæg Østens Sønner!
Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa: “Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara. Kawonongeni anthu a kummawako.
29 Man skal tage deres Telte og Hjorde, deres Telttæpper, alle deres Kar, bortføre Kamelerne fra dem og raabe til dem: »Trindt om er Rædsel!«
Landani matenti awo ndi nkhosa zawo, ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo. Mutengenso ngamira zawo. Anthu adzafuwula kwa iwo kuti, ‘Kuli zoopsa mbali zonse!’
30 Fly i Hast, søg Ly i det dybe, Hazors Borgere, lyder det fra HERREN. Thi Kong Nebukadrezar af Babel har oplagt et Raad imod eder og undfanget en Tanke imod eder.
“Thawani mofulumira! Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,” akutero Yehova. “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu; wakonzekera zoti alimbane nanu.
31 Kom, drag op mod et roligt Folk, der bor i Tryghed, lyder det fra HERREN, uden Porte og Slaaer; de bor for sig selv.
“Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere, umene ukukhala mosatekeseka,” akutero Yehova, “mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo; anthu ake amakhala pa okha.
32 Deres Kameler gøres til Bytte, deres mange Hjorde til Rov. Jeg spreder dem, der har rundklippet Haar, for alle Vinde, og fra alle Kanter bringer jeg Undergang over dem, lyder det fra HERREN.
Ngamira zawo zidzafunkhidwa, ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa. Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali. Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,” akutero Yehova.
33 Hazor bliver Sjakalers Bo, en Ørken til evig Tid; der skal ej bo et Menneske, ej dvæle et Menneskebarn.
“Hazori adzasanduka bwinja, malo okhalamo nkhandwe mpaka muyaya. Palibe munthu amene adzayendemo.”
34 HERRENS Ord, som kom til Profeten Jeremias om Elam i Kong Zedekias af Judas første Regeringstid:
Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu:
35 Saa siger Hærskarers HERRE: Jeg knækker Elams Bue, det ypperste af deres Kraft;
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, umene uli chida chawo champhamvu.
36 og jeg bringer over Elam de fire Vinde fra de fire Verdenshjørner og spreder dem for alle disse Vinde; der skal ikke være et Folk, som de bortdrevne Elamiter ikke kommer hen til.
Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamu kuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga; ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi, ndipo sipadzakhala dziko limene anthu a ku Elamu sadzafikako.
37 Jeg knuser dem foran deres Fjender og dem, der staar dem efter Livet, og jeg sender Ulykke over dem, min glødende Vrede, lyder det fra HERREN. Jeg sender Sværdet efter dem, til jeg faar dem udslettet.
A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo. Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga ndipo adzakhala pa mavuto,” akutero Yehova. “Ndidzawapirikitsa ndi lupanga mpaka nditawatheratu.
38 Jeg rejser min Trone i Elam og tilintetgør der baade Konge og Fyrster, lyder det fra HERREN.
Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamu ndipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,” akutero Yehova.
39 Men i de sidste Dage vender jeg Elams Skæbne, lyder det fra HERREN.
“Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezera anthu a ku Elamu dziko lawo,” akutero Yehova.

< Jeremias 49 >