< Esajas 52 >
1 Vaagn op, vaagn op, ifør dig din Styrke, Zion, tag dit Højtidsskrud paa, Jerusalem, hellige By! Thi uomskaarne, urene Folk skal ej mer komme ind.
Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni, vala zilimbe. Vala zovala zako zokongola, iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika. Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwa sadzalowanso pa zipata zako.
2 Ryst Støvet af dig, staa op, tag Sæde, Jerusalem, fri dig for Halslænken, Zions fangne Datter!
Sasa fumbi lako; imirira nukhale pa mpando waufumu, iwe Yerusalemu. Inu omangidwa a ku Ziyoni, masulani maunyolo amene ali mʼkhosi mwanumo.
3 Thi saa siger HERREN: For intet solgtes I, og uden Sølv skal I løskøbes.
Pakuti Yehova akuti, “Sindinalandirepo kanthu pamene ndinakugulitsani, choncho mudzawomboledwa wopanda ndalama.”
4 Thi saa siger den Herre HERREN: I Begyndelsen drog mit Folk ned til Ægypten for at bo der som fremmed, og siden undertrykte Assyrien det uden Vederlag.
Pakuti Ambuye Yehova akuti, “Poyamba paja anthu anga anapita kukakhala ku Igupto; nawonso Asiriya awapondereza popanda chifukwa.”
5 Og nu? Hvad har jeg at gøre her? lyder det fra HERREN; mit Folk er jo ranet for intet. De, der hersker over det, brovter, lyder det fra HERREN, og mit Navn vanæres ustandseligt Dagen lang.
Tsopano Ine Yehova ndikuti, “Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu, amene amawalamulira amawanyoza,” akutero Yehova. “Ndipo tsiku lonse, akungokhalira kuchita chipongwe dzina langa.
6 Derfor skal mit Folk kende mit Navn paa hin Dag, at det er mig, som har talet, ja mig.
Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa; kotero adzadziwa kuti ndi Ine amene ndikuyankhula, Indedi, ndine.”
7 Hvor liflige er paa Bjergene Glædesbudets Fodtrin, han, som udraaber Fred, bringer gode Tidender, udraaber Frelse, som siger til Zion: »Din Gud har vist, han er Konge.«
Ngokongoladi mapazi a amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri. Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere, chisangalalo ndi chipulumutso. Iwo akubwera kudzawuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wako ndi mfumu!”
8 Hør, dine Vægtere raaber, de jubler til Hobe, thi de ser for deres Øjne HERREN vende hjem til Zion.
Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo; akuyimba pamodzi mwachimwemwe. Popeza akuona chamaso kubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.
9 Bryd ud til Hobe i Jubel, Jerusalems Tomter! Thi HERREN trøster sit Folk, genløser Jerusalem.
Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe, inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu.
10 Han blotter sin hellige Arm for al Folkenes Øjne, den vide Jord skal skue Frelsen fra vor Gud.
Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika pamaso pa anthu a mitundu yonse, ndipo anthu onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
11 Bort, bort, drag ud derfra, rør ej noget urent, bort, tvæt jer, I, som bærer HERRENS Kar!
Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko! Musakhudze kanthu kodetsedwa! Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehova tulukanimo ndipo mudziyeretse.
12 Thi i Hast skal I ej drage ud, I skal ikke flygte; nej, foran eder gaar HERREN, eders Tog slutter Israels Gud.
Koma simudzachoka mofulumira kapena kuchita chothawa; pakuti Yehova adzayenda patsogolo panu, Mulungu wa Israeli adzakutetezani kumbuyo kwanu.
13 Se, min Tjener faar Fremgang han stiger, løftes og ophøjes saare.
Taonani, mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake adzakwezedwa ndi kulemekezedwa ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.
14 Som mange blev maalløse over ham, — saa umenneskelig ussel saa han ud, han ligned ej Menneskenes Børn —
Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu. Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.
15 skal Folk i Mængde undres, Konger blive stumme over ham; thi hvad ikke var sagt dem, ser de, de skuer, hvad de ikke havde hørt.
Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye. Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona, ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.