< 2 Mosebog 15 >

1 Ved den Lejlighed sang Moses og Israeliterne denne Sang for HERREN: Jeg vil synge for HERREN, thi han er højt ophøjet, Hest og Rytter styrted han i Havet!
Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wakwezeka mʼchigonjetso. Kavalo ndi wokwera wake, Iye wawaponya mʼnyanja.
2 HERREN er min Styrke og min Lovsang, og han blev mig til Frelse. Han er min Gud, og jeg vil prise ham, min Faders Gud, og jeg vil ophøje ham.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda, Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza.
3 HERREN er en Krigshelt, HERREN er hans Navn!
Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.
4 Faraos Vogne og Krigsmagt styrted han i Havet, hans ypperste Vognkæmpere drukned i det røde Hav,
Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo Iye wawaponya mʼnyanja. Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao amizidwa mʼNyanja Yofiira.
5 Strømmene dækked dem, de sank som Sten i Dybet.
Nyanja yakuya inawaphimba; Iwo anamira pansi ngati mwala.”
6 Din højre, HERRE, er herlig i Kraft, din højre, HERRE, knuser Fjenden.
Yehova, dzanja lanu lamanja ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake. Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja linaphwanya mdani.
7 I din Højheds Vælde fælder du dine Modstandere, du slipper din Harme løs, den fortærer dem som Straa.
Ndi ulemerero wanu waukulu, munagonjetsa okutsutsani. Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu; ndipo unawapsereza ngati udzu.
8 Ved din Næses Pust dyngedes Vandene op, Vandene stod som en Vold, Strømmene stivnede midt i Havet.
Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu madzi anawunjikana pamodzi. Nyanja yakuya ija inasanduka madzi owuma gwaa kufika pansi.
9 Fjenden tænkte: »Jeg sætter efter dem, indhenter dem, uddeler Bytte, stiller mit Begær paa dem; jeg drager mit Sværd, min Haand skal udrydde dem.«
Mdaniyo anati, “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira. Ndidzagawa chuma chawo; ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa. Ine ndidzasolola lupanga langa, ndi mkono wanga ndidzawawononga.”
10 Du blæste med din Aande, Havet skjulte dem; de sank som Bly i de vældige Vande.
Koma Inu munawuzira mphepo yanu, ndipo nyanja inawaphimba. Iwo anamira ngati chitsulo mʼmadzi amphamvu.
11 Hvo er som du blandt Guder, HERRE, hvo er som du, herlig i Hellighed, frygtelig i Stordaad, underfuld i dine Gerninger!
Ndithu Yehova, pakati pa milungu, ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera, ndiponso wotamandika wolemekezeka, chifukwa cha ntchito zanu, zazikulu ndi zodabwitsa?
12 Du udrakte din højre, og Jorden slugte dem.
Munatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko linawameza.
13 Du leded i din Miskundhed det Folk, du genløste, du førte det i din Vælde til din hellige Bolig.
Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera anthu amene munawawombola. Ndi mphamvu zanu munawatsogolera ku malo anu woyera.
14 Folkene hørte det og bæved, Skælven greb Filisterlandets Folk.
Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha, mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti.
15 Da forfærdedes Edoms Høvdinger, Moabs Fyrster grebes af Rædsel, Kana'ans Beboere tabte alle Modet.
Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu, otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha, ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.
16 Skræk og Angst faldt over dem, ved din Arms Vælde blev de maalløse som Sten, til dit Folk var naaet frem, o HERRE, til Folket, du vandt dig, var naaet frem.
Onse agwidwa ndi mantha woopsa. Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu, iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu, Inu Yehova atadutsa; inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula.
17 Du førte dem frem og planted dem i din Arvelods Bjerge, paa det Sted du beredte dig til Bolig, HERRE, i den Helligdom, Herre, som dine Hænder grundfæsted.
Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa pa phiri lanu. Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo; malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.
18 HERREN er Konge i al Evighed!
“Yehova adzalamula mpaka muyaya.”
19 Thi da Faraos Heste med hans Vogne og Ryttere drog ud i Havet, lod HERREN Havets Vande strømme tilbage over dem, medens Israeliterne gik gennem Havet paa tør Bund.
Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma.
20 Da greb Profetinden Mirjam, Arons Søster, Pauken, og alle Kvinderne fulgte hende med Pauker og Danse,
Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina.
21 og Mirjam sang for: Syng for HERREN, thi han er højt ophøjet, Hest og Rytter styrted han i Havet!
Miriamu anawayimbira nyimbo iyi: “Imbirani Yehova, chifukwa iye wapambana. Kavalo ndi wokwerapo wake Iye wawamiza mʼnyanja.”
22 Derpaa lod Moses Israel bryde op fra det røde Hav, og de drog ud i Sjurs Ørken, og de vandrede tre Dage i Ørkenen uden at finde Vand.
Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi.
23 Saa naaede de Mara, men de kunde ikke drikke Vandet for dets bitre Smag, thi det var bittert; derfor kaldte man Stedet Mara.
Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara).
24 Da knurrede Folket mod Moses og sagde: »Hvad skal vi drikke?«
Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”
25 Men han raabte til HERREN, og da viste HERREN ham en bestemt Slags Træ; og da han kastede det i Vandet, blev Vandet drikkeligt. Der gav han dem Bestemmelser om Lov og Ret, og der satte han dem paa Prøve.
Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino. Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa.
26 Og han sagde: »Hvis du vil høre paa HERREN din Guds Røst og gøre, hvad der er ret i hans Øjne, og lytte til hans Bud og holde dig alle hans Bestemmelser efterrettelig, saa vil jeg ikke bringe nogen af de Sygdomme over dig, som jeg bragte over Ægypterne, men jeg HERREN er din Læge!«
Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”
27 Derpaa kom de til Elim, hvor der var tolv Vandkilder og halvfjerdsindstyve Palmetræer, og de lejrede sig ved Vandet der.
Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.

< 2 Mosebog 15 >