< Haggaj 1 >
1 I Kong Darius's andet Aar, i den sjette Maaned, paa den første Dag i Maaneden, kom Herrens Ord ved Profeten Haggaj til Serubabel, Sealthiels Søn, Landshøvdingen i Juda, og til Josua, Jozadaks Søn, Ypperstepræsten, saalunde:
Chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Yehova anapatsa mneneri Hagai uthenga wopita kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, ndiponso kwa mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki:
2 Saa siger den Herre Zebaoth: Dette Folk, de sige: Tiden er ikke kommen, Tiden til at bygge Herrens Hus.
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu awa amanena kuti, ‘Nthawi sinafike yoti nʼkumanga Nyumba ya Yehova.’”
3 Og Herrens Ord kom ved Profeten Haggaj, saaledes:
Tsono Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti,
4 Er det Tid for eder at bo i eders panelede Huse, medens dette Hus er øde?
“Kodi ino ndi nthawi yoti inuyo muzikhala mʼnyumba zomanga bwino, pamene Nyumba yangayi ikanali bwinja?”
5 Og nu, saa siger den Herre Zebaoth: Giver Agt paa eders Veje!
Tsono zimene Yehova Wamphamvuzonse akunena ndi izi, “Ganizirani bwino njira zanu.
6 I udsaa meget og høste lidet ind, I æde og blive ikke mætte, I drikke og blive ikke læskede, I klæde eder og blive ikke varme, og den, som faar Løn, faar sin Løn i en hullet Pung.
Mwadzala zambiri, koma mwakolola zochepa. Mumadya, koma simukhuta. Mumamwa, koma ludzu lanu silitha. Mumavala, koma simumva kutentha. Mumalandira malipiro, koma ndalama zanu zimatha ngati mwaziyika mʼthumba lobowoka.”
7 Saa siger den Herre Zebaoth: Giver Agt paa eders Veje!
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ganizirani bwino njira zanu.
8 Gaar op paa Bjerget, og henter Tømmer, og bygger Huset, saa vil jeg have Behag deri og bevise mig herlig, siger Herren.
Pitani ku mapiri ndipo mukatenge matabwa oti mudzamangire Nyumba yanga, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiramo ulemu,” akutero Yehova.
9 I vente meget, og se, det bliver til lidet, og naar I have ført det hjem, da blæser jeg det bort. Hvorfor? siger den Herre Zebaoth. For mit Hus's Skyld, som er øde, medens I have travlt, hver med sit eget Hus.
“Mumayembekezera zambiri, koma taonani mwapeza pangʼono pokha. Zimene munazibweretsa ku nyumba, Ine ndinazimwaza. Nʼchifukwa chiyani?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Chifukwa Nyumba yanga ikanali bwinja, pamene aliyense wa inu watanganidwa kumanga nyumba yake.
10 Derfor lukke Himlene sig til over eder, saa at de ikke give Dug, og Jorden har tilbageholdt sin Grøde.
Choncho, chifukwa cha inu, mitambo yaleka kugwetsa mvula ndipo dziko lapansi laleka kutulutsa zomera.
11 Thi jeg kaldte Tørke over Jorden og over Bjergene og over Kornet og over Mosten og over Olien og over det, som Jorden frembringer, og over Folket og over Kvæget og over alt, hvad der udføres med Hænder.
Ndabweretsa chilala pa minda ndi pa mapiri, chilala chawumitsa tirigu, mphesa, mafuta a olivi ndi chilichonse chimene chimamera pa nthaka, pa anthu ndi pa ngʼombe, ndi pa ntchito zonse za manja anu.”
12 Da adløde Serubabel, Sealthiels Søn, og Josua, Jozadaks Søn, Ypperstepræsten, og hele det overblevne Folk Herrens deres Guds Røst og Profeten Haggajs Ord, eftersom Herren deres Gud havde sendt ham; og Folket frygtede for Herrens Ansigt.
Pamenepo Zerubabeli mwana wa Sealatieli, mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndi anthu onse otsala anamvera mawu a Yehova Mulungu wawo ndi uthenga wa Hagai, chifukwa anatumidwa ndi Yehova Mulungu wawo. Ndipo anthuwo anaopa Yehova.
13 Da sagde Haggaj, Herrens Sendebud, som Budskab fra Herren til Folket, saaledes: Jeg er med eder, siger Herren.
Tsono Hagai, mthenga wa Yehova, anapereka kwa anthuwo uthenga uwu wa Yehova: “Ine ndili nanu,” akutero Yehova.
14 Og Herren vakte Aanden hos Serubabel, Sealthiels Søn, Judas Landshøvding, og Aanden hos Ypperstepræsten Josua, Jozadaks Søn, og Aanden hos alt det overblevne Folk, og de kom og gjorde Arbejdet paa den Herre Zebaoths, deres Guds Hus
Kotero Yehova anakhudza mtima wa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, mtima wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso mitima ya anthu onse otsala. Iwo anabwera ndi kuyamba ntchito yomanga Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wawo,
15 paa den fire og tyvende Dag i Maaneden, i den sjette Maaned, i Kong Darius's andet Aar.
pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chimodzi, wa chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo.