< Apostelenes gerninger 3 >

1 Men Peter og Johannes gik op i Helligdommen ved Bedetimen, den niende Time.
Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana.
2 Og en Mand, som var lam fra Moders Liv af, blev baaren frem; ham satte de daglig ved den Dør til Helligdommen, som kaldtes den skønne, for at han kunde bede dem, som gik ind i Helligdommen, om Almisse.
Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo.
3 Da han saa Peter og Johannes, idet de vilde gaa ind i Helligdommen, bad han om at faa en Almisse.
Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama.
4 Da saa Peter tillige med Johannes fast paa ham og sagde: „Se paa os!”
Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!”
5 Og han gav Agt paa dem, efterdi han ventede at faa noget af dem.
Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo.
6 Men Peter sagde: „Sølv og Guld ejer jeg ikke, men hvad jeg har, det giver jeg dig: I Jesu Kristi Nazaræerens Navn staa op og gaa!”
Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.”
7 Og han greb ham ved den højre Haand og rejste ham op.
Ndipo anamugwira dzanja lamanja, namuthandiza kuti ayimirire ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi akakolo ake analimba.
8 Men straks bleve hans Ben og Ankler stærke, og han sprang op og stod og gik omkring og gik med dem ind i Helligdommen, hvor han gik omkring og sprang og lovede Gud.
Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu.
9 Og hele Folket saa ham gaa omkring og love Gud.
Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu,
10 Og de kendte ham som den, der havde siddet ved den skønne Port til Helligdommen for at faa Almisse; og de bleve fulde af Rædsel og Forfærdelse over det, som var timedes ham.
anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira.
11 Medens han nu holdt fast ved Peter og Johannes, løb alt Folket rædselsslaget sammen om dem i den Søjlegang, som kaldes Salomons.
Wopempha uja akuyenda pamodzi ndi Petro ndi Yohane, anthu onse anadabwa ndipo anawathamangira iwo kumalo wotchedwa Khonde la Solomoni.
12 Men da Peter saa det, talte han til Folket: „I israelitiske Mænd! Hvorfor undre I eder over dette? eller hvorfor stirre I paa os, som om vi af egen Magt eller Gudfrygtighed havde gjort, at han kan gaa?
Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu?
13 Abrahams og Isaks og Jakobs Gud, vore Fædres Gud, har herliggjort sin Tjener Jesus, hvem I prisgave og fornægtede for Pilatus, da han dømte, at han skulde løslades.
Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule.
14 Men I fornægtede den hellige og retfærdige og bade om, at en Morder maatte skænkes eder.
Koma inu munamukana Woyera ndi Wolungamayo ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wakupha anthu.
15 Men Livets Fyrste sloge I ihjel, hvem Gud oprejste fra de døde, hvorom vi ere Vidner.
Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi.
16 Og i Troen paa hans Navn har hans Navn styrket denne, hvem I se og kende, og Troen, som virkedes ved ham, har givet denne hans Førlighed i Paasyn af eder alle.
Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.
17 Og nu, Brødre! jeg ved, at I handlede i Uvidenhed, ligesom ogsaa eders Raadsherrer.
“Tsopano abale ine ndikudziwa kuti inu munachita zimenezi mosadziwa, monga momwenso anachitira atsogoleri anu.
18 Men Gud har saaledes fuldbyrdet, hvad han forud forkyndte ved alle Profeternes Mund, at hans Salvede skulde lide.
Koma umu ndi mmene Mulungu anakwaniritsira zimene zinanenedwa kale ndi aneneri onse, kuti Khristu adzamva zowawa.
19 Derfor fatter et andet Sind og vender om, for at eders Synder maa blive udslettede, for at Vederkvægelsens Tider maa komme fra Herrens Aasyn,
Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye,
20 og han maa sende den for eder bestemte Kristus, Jesus,
ndi kuti Iye atumize Yesu Khristu amene anasankhidwa chifukwa cha inu.
21 hvem Himmelen skal modtage indtil alle Tings Genoprettelses Tider, hvorom Gud har talt ved sine hellige Profeters Mund fra de ældste Dage. (aiōn g165)
Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima. (aiōn g165)
22 Moses sagde: „En Profet skal Herren eders Gud oprejse eder af eders Brødre ligesom mig; ham skulle I høre i alt, hvad han end vil tale til eder.
Pakuti Mose anati, ‘Ambuye Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri monga ine kuchokera pakati pa anthu anu; mumvere zonse zimene iye akuwuzeni.
23 Men det skal ske, hver Sjæl, som ikke hører den Profet, skal udryddes af Folket.”
Aliyense amene sadzamvera mawu a mneneriyo, adzayenera kuchotsedwa pakati pa abale ake.’
24 Men ogsaa alle Profeterne, fra Samuel af og derefter, saa mange som talte, have ogsaa forkyndt disse Dage.
“Ndipo aneneri onse ambiri amene anayankhula kuyambira Samueli, ananeneratu za masiku ano.
25 I ere Profeternes Sønner og Sønner af den Pagt, som Gud sluttede med vore Fædre, da han sagde til Abraham: „Og i din Sæd skulle alle Jordens Slægter velsignes.”
Inu ndinu ana a aneneri ndiponso ana apangano limene Mulungu anachita ndi makolo anu. Iye anati kwa Abrahamu, ‘Anthu onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa zidzukulu zako.’
26 For eder først har Gud oprejst sin Tjener og sendt ham for at velsigne eder, naar enhver af eder vender om fra sin Ondskab.”
Pamene Mulungu anaukitsa mtumiki wake, anamutuma Iye poyamba kwa inu kuti akudalitseni pobweza aliyense wa inu ku zoyipa zake.”

< Apostelenes gerninger 3 >