< Ezdráš 9 >

1 A když se to vykonalo, přistoupili ke mně knížata, řkouce: Neoddělil se lid Izraelský, ani kněží a Levítové od národů zemí, ale činí podlé ohavností Kananejských, Hetejských, Ferezejských, Jebuzejských, Ammonitských, Moábských, Egyptských a Amorejských.
Zitachitika izi, atsogoleri anabwera kwa ine nati, “Aisraeli, kuphatikizanso ansembe ndi Alevi, sanadzipatule ku makhalidwe onyansa a anthu a mitundu ina amene ayandikana nafe: Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aigupto ndi Aamori.
2 Nebo nabrali sobě a synům svým dcer jejich, a smísili se símě svaté s národy zemí, a knížata a vrchnost první byla v tom přestoupení.
Zomwe zikuchitika ndi izi. Aisraeli ena ndi ana awo aamuna anayamba kukwatira ana aakazi a anthuwa. Choncho mtundu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a mʼderali. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo akupambana pa makhalidwe osakhulupirikawa.”
3 Kteroužto věc když jsem uslyšel, roztrhl jsem roucho své i plášť, a trhal jsem vlasy s hlavy své i z brady, a seděl jsem zděšený.
Nditamva zimenezi, ndinangʼamba chovala changa ndi mwinjiro wanga ndipo ndinamwetula tsitsi la kumutu kwanga ndi ndevu zanga nʼkukhala pansi ndili wokhumudwa.
4 I shromáždili se ke mně všickni, třesoucí se před řečmi Boha Izraelského pro přestoupení lidu přestěhovaného, já pak seděl jsem zděšený, až do oběti večerní.
Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.
5 Ale v čas oběti večerní vstal jsem od trápení svého, maje na sobě roucho roztržené i plášť svůj, a klekl jsem na kolena svá, rozprostíraje ruce své k Hospodinu Bohu svému.
Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga
6 A řekl jsem: Bože můj, stydím se a hanbím pozdvihnouti, Bože můj, tváři své k tobě; nebo nepravosti naše rozmnožily se nad hlavou, a provinění naše vzrostlo až k nebi.
ndipo ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo.
7 Ode dnů otců našich u veliké jsme vině až do tohoto dne, a pro nepravosti naše vydáni jsme my, králové naši i kněží naši v ruku králů zemí pod meč, v zajetí a v loupež, a v zahanbení tváři, tak jakž se to nyní děje.
Ndipo chifukwa cha machimo athu, ifeyo, mafumu athu, ndi ansembe athu takhala akutipereka mʼmanja mwa mafumu a mitundu ina ya anthu kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu zathu ndi kutichititsa manyazi monga zilili leromu.
8 Teď pak rychle stala se nám milost od Hospodina Boha našeho, že zanechal nám ostatků, a dal nám obydlí na místě svatém, aby osvítil oči naše Bůh náš, a dal nám maličké povydchnutí od služby naší.
“Koma tsopano, pa kanthawi kochepa, Inu Yehova Mulungu wathu mwaonetsa kukoma mtima. Inu mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kutipatsa cholowa mʼmalo anu oyera. Mwatipulumutsa ku ukapolo ndi kutipatsa mpumulo pangʼono mu ukapolo wathu.
9 Nebo ač jsme byli služebníci, však nenechal nás Bůh náš v porobě naší, ale naklonil k nám milostí krále Perské, dav nám život, abychom vyzdvihli dům Boha našeho, a zase obnovili pustiny jeho, nýbrž ohradil nás v Judstvu a v Jeruzalémě.
Ndifedi akapolo. Koma Inu Yehova simunatileke mu ukapolo wathu. Mwationetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Perisiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu pokonzanso mabwinja ake. Mwatitchinjiriza mʼdziko la Yuda ndi Yerusalemu.
10 Nyní tedy což díme, ó Bože náš, po těch věcech, poněvadž jsme opustili přikázaní tvá,
“Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, kodi tinganene chiyani titachita zoyipa zonsezi? Ife taphwanya malamulo anu
11 Kteráž jsi vydal skrze služebníky své proroky, řka: Země ta, do kteréž jdete, abyste jí dědičně vládli, jest země nečistá, pro nečistotu národů těch zemí, pro ohavnosti jejich, kterýmiž ji naplnili všudy naskrze v nečistotě své.
amene munawapereka kudzera mwa atumiki anu aneneri. Inu munati, ‘Dziko limene mukulowamolo kuti likhale cholowa chanu, ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya mʼmayikomo. Ndipo adzaza dzikolo ndi zochita zawo zonyansa.
12 Protož nyní dcer vašich nedávejte synům jejich, a dcer jejich nebeřte synům vašim, a nehledejte pokoje jejich a dobrého jejich, až na věky, abyste se zmocnili, a jedli dobré věci země, a k dědičnému vládařství zanechali ji synům svým až na věky.
Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’
13 Po všech pak těch věcech, kteréž na nás přišly pro zlé skutky naše, a pro veliké naše provinění, poněvadž ty, Bože náš, netrestal jsi nás podlé nepravostí našich, a dal jsi nám vysvobození takové,
“Tsono pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha ntchito zathu zoyipa ndi uchimo wathu waukulu, komanso pambuyo poona kuti Inu Mulungu wathu simunangotilanga kokha pangʼono kuyerekeza ndi kuchimwa kwathu komanso mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke,
14 Opět-liž bychom rušiti měli tvá přikázaní, a přízniti se s národy těmito ohavnými? Zdaliž bys se zůřivě nehněval na nás, až bys nás do konce vyhladil, tak že by žádný nezůstal a neušel?
kodi ife nʼkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu amitundu ina amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzatikwiyira ndi kutiwononga kwathunthu popanda wina wotsala kapena wopulumuka?
15 Hospodine Bože Izraelský, ty jsi spravedlivý; nebo jsme pozůstali ostatkové, jakž se to vidí dnešního dne. Aj, my jsme před tebou s proviněním svým, ač bychom neměli postavovati se před tváří tvou pro věci takové.
Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”

< Ezdráš 9 >