< Józua 12 >

1 Tito pak jsou králové té země, kteréž pobili synové Izraelští, a opanovali zemi jejich, za Jordánem k východu slunce, od potoku Arnon až k hoře Hermon i všecky roviny k východu:
Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:
2 Seon, král Amorejský, kterýž bydlil v Ezebon, a panoval od Aroer, kteréž leží při břehu potoka Arnon, a u prostřed potoka toho, a polovici Galád, až do potoka Jabok, kterýž jest na pomezí synů Ammon,
Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.
3 A od rovin až k moři Ceneret k východu, a až k moři pouště, jenž jest moře slané k východu, kudyž se jde k Betsimot, a od polední strany ležící pod horou Fazga.
Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.
4 Pomezí také Oga, krále Bázan, z ostatků Refaimských, kterýž bydlil v Astarot a v Edrei,
Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi.
5 A kterýž panoval na hoře Hermon a v Sálecha, i ve vší krajině Bázan až ku pomezí Gessuri a Machati, a nad polovicí Galád, ku pomezí Seona, krále Ezebon.
Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.
6 Mojžíš, služebník Hospodinův, a synové Izraelští pobili je; a dal ji Mojžíš služebník Hospodinův k vládařství pokolení Rubenovu, Gádovu a polovici pokolení Manassesova.
Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.
7 Tito pak jsou králové země té, kteréž pobil Jozue a synové Izraelští za Jordánem k západu, od Balgad, kteréž jest na poli Libánském, až k hoře lysé, kteráž se táhne až do Seir, a dal ji Jozue pokolením Izraelským k vládařství po dílích jejich,
Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.
8 Na horách i na rovinách, i po polích, i v údolích, i na poušti a na poledne, zemi Hetejského, Amorejského, Kananejského, Ferezejského, Hevejského a Jebuzejského:
Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:
9 Král Jericha jeden, král Hai, kteréž bylo na straně Bethel, jeden;
mfumu ya Yeriko imodzi mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi
10 Král Jeruzalémský jeden, král Hebron jeden;
mfumu ya Yerusalemu imodzi mfumu ya Hebroni imodzi
11 Král Jarmut jeden, král Lachis jeden;
mfumu ya Yarimuti imodzi mfumu ya Lakisi imodzi
12 Král Eglon jeden, král Gázer jeden;
mfumu ya Egiloni imodzi mfumu ya Gezeri imodzi
13 Král Dabir jeden, král Gader jeden;
mfumu ya Debri imodzi mfumu ya Gederi imodzi
14 Král Horma jeden, král Arad jeden;
mfumu ya Horima imodzi mfumu ya Aradi imodzi
15 Král Lebna jeden, král Adulam jeden;
mfumu ya Libina imodzi mfumu ya Adulamu imodzi
16 Král Maceda jeden, král Bethel jeden;
mfumu ya Makeda imodzi mfumu ya Beteli imodzi
17 Král Tafua jeden, král Chefer jeden;
mfumu ya Tapuwa imodzi mfumu ya Heferi imodzi
18 Král Afek jeden, král Sáron jeden;
mfumu ya Afeki imodzi mfumu ya Lasaroni imodzi
19 Král Mádon jeden, král Azor jeden;
mfumu ya Madoni imodzi mfumu ya Hazori imodzi
20 Král Simron Meron jeden, král Achzaf jeden;
mfumu ya Simuroni Meroni imodzi mfumu ya Akisafu imodzi
21 Král Tanach jeden, král Mageddo jeden;
mfumu ya Taanaki imodzi mfumu ya Megido imodzi
22 Král Kedes jeden, král Jekonam z Karmelu jeden;
mfumu ya Kadesi imodzi mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi
23 Král Dor z krajiny Dor jeden, král z Goim v Galgal jeden;
mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi mfumu ya Goyini ku Giligala imodzi
24 Král Tersa jeden. Všech králů třidceti a jeden.
mfumu ya Tiriza imodzi mafumu onse pamodzi analipo 31.

< Józua 12 >