< Jeremiáš 7 >
1 Slovo, kteréž se stalo k Jeremiášovi od Hospodina, řkoucí:
Mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeremiya ndi awa,
2 Postav se v braně domu Hospodinova, a ohlašuj tam slovo toto, a rci: Slyšte slovo Hospodinovo všickni Judští, kteříž vcházíte do bran těchto, abyste se klaněli Hospodinu.
“Ima pa chipata cha Nyumba ya Yehova ndipo kumeneko ukalalikire uthenga uwu: “‘Imvani mawu a Yehova, inu nonse anthu a ku Yuda amene mumalowa pa chipata ichi kudzapembedza Yehova.
3 Takto praví Hospodin zástupů, Bůh Izraelský: Polepšte cest svých i předsevzetí svých, a způsobím to, abyste bydlili na místě tomto.
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kukhala pa malo ano.
4 Neskládejte naděje své v slovích lživých, říkajíce: Chrám Hospodinův, chrám Hospodinův, chrám Hospodinův jest.
Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’
5 Ale jestliže všelijak polepšíte cest svých, a předsevzetí svých, jestliže spravedlivě soud konati budete mezi mužem a mezi bližním jeho;
Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama,
6 Příchozího, sirotka a vdovy neutisknete, a krve nevinné nevylejete na místě tomto, a za bohy cizími nebudete-li choditi k svému zlému:
ngati mutaleka kuzunza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye ndi kuleka kupha anthu osalakwa pa malo ano, ndipo ngati muleka kutsatira milungu ina, kuti ingakuwonongeni,
7 Tedy způsobím, abyste bydlili na místě tomto, v zemi, kterouž jsem dal otcům vašim, od věků až na věky.
Ine ndidzakulolani kukhala pa malo ano, mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu mpaka muyaya.
8 Aj, vy skládáte naději svou v slovích lživých, kteráž neprospívají.
Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu.
9 Zdaliž kradouce, mordujíce a cizoložíce i křivě přisahajíce a kadíce Bálovi; též chodíce za bohy cizími, jichž neznáte,
“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe,
10 Předce choditi a postavovati se budete před oblíčejem mým v domě tomto, kterýž nazván jest od jména mého, a říkati: Vyproštěni jsme, abyste páchali ty všecky ohavnosti?
ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi?
11 Což peleší lotrovskou jest dům tento před očima vašima, kterýž nazván jest od jména mého? Aj, takéť já vidím, dí Hospodin.
Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.”
12 Ale jděte aspoň na místo mé, kteréž bylo v Sílo, kdež jsem byl způsobil příbytek jménu svému z počátku, a vizte, co jsem učinil jemu pro nešlechetnost lidu svého Izraelského.
“‘Pitani tsopano ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziwika ndi Dzina langa, ndipo mukaone zimene ndinachita kumeneko chifukwa cha kuyipa kwa anthu anga Aisraeli.
13 Protož nyní, že činíte všecky skutky tyto, dí Hospodin, a když mluvím k vám, ráno vstávaje, a to ustavičně, tedy neposloucháte, a když volám na vás, tedy neozýváte se:
Tsono popeza munkachita zonsezi, ngakhale Ine kukuyankhulani koma inu osamvera, kukuyitanani koma inu osayankha,
14 Protož učiním domu tomuto, kterýž nazván jest od jména mého, v němž vy doufáte, i místu tomuto, kteréž jsem dal vám a otcům vašim, jako jsem učinil Sílo;
choncho ndidzachita pa Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langayi, Nyumba ya Yehova imene mumayidalira, malo amene ndinapereka kwa inu ndi makolo anu, zomwe ndinachita ku Silo.
15 A zavrhu vás od tváři své, jako jsem zavrhl bratří vaše, všecko símě Efraimovo.
Ndidzakuthamangitsani pamaso panga, ngati momwe ndinachitira abale anu onse, anthu a Efereimu.’”
16 Ty tedy nemodl se za lid tento, aniž pozdvihuj za ně hlasu a modlitby, aniž se přimlouvej ke mně; nebo tě nikoli nevyslyším.
“Choncho iwe Yeremiya usawapempherere anthu awa ngakhale kuwapepesera kapenanso kuwapembedzera; usandidandaulire, chifukwa Ine sindidzakumvera.
17 Zdaliž sám nevidíš, co oni činí v městech Judských a po ulicích Jeruzalémských?
Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu?
18 Synové zbírají dříví, a otcové zaněcují oheň, ženy pak zadělávají těsto, aby pekly koláče tvoru nebeskému, a obětovali oběti mokré bohům cizím, aby mne popouzeli.
Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima.
19 Zdaliž to proti mně jest, že mne oni popouzejí? dí Hospodin. Zdali není proti nim k zahanbení tváři jejich?
Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.”
20 Pročež takto praví Panovník Hospodin: Aj, hněv můj a prchlivost má vylita bude na místo toto, na lidi i na hovada, i na dříví polní, i na úrody země, a hořeti bude, tak že neuhasne.
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika.
21 Takto praví Hospodin zástupů, Bůh Izraelský: Zápaly své přidejte k obětem svým, a jezte maso.
“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Wonjezerani nsembe zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo ndipo mudye nyama yakeyo!
22 Nebo jsem nemluvil s otci vašimi, aniž jsem přikázal jim v ten den, v kterýž jsem je vyvedl z země Egyptské, o zápalích a obětech.
Pakuti pamene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto ndi kuyankhula nawo, sindinawalamulire kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zinazo,
23 Ale toto přikázal jsem jim, řka: Poslouchejte hlasu mého, a budu vaším Bohem, a vy budete mým lidem, a choďte po vší cestě, kterouž jsem vám přikázal, aby vám dobře bylo.
koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.
24 Však neposlechli, aniž naklonili ucha svého, ale chodili po radách, a podlé zdání srdce svého zlého. Obrátili se ke mně hřbetem a ne tváří svou.
Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo.
25 Od toho času, jakž vyšli otcové vaši z země Egyptské, až do tohoto dne posílal jsem k vám všecky služebníky své proroky, každý den ráno vstávaje, a to ustavičně.
Kuyambira tsiku limene makolo awo anachoka ku Igupto mpaka lero lino, ndakhala ndikuwatumizira atumiki anga, aneneri.
26 Však neposlechli mne, aniž naklonili ucha svého, ale zatvrdivše šíji svou, hůře činili nežli otcové jejich.
Koma anthuwo sanandimvere kapena kusamalira. Anawumitsa mitima yawo ndi kuchita zoyipa kuposa makolo awo.
27 Když jim mluvíš všecka slova tato, ani tebe neposlouchají, a když voláš na ně, neohlašují se tobě.
“Ngakhale iwe uwawuze zonsezi koma sadzakumvera. Ngakhale uwayitane koma sadzakuyankha.
28 Protož rciž jim: Tento jest národ, kteříž neposlouchají hlasu Hospodina Boha svého, aniž přijímají naučení. Zhynula pravda, a vymizela z úst jejich.
Nʼchifukwa chake udzawawuze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere Yehova Mulungu wake, wosalola kulangizidwa. Choonadi chatha; chazimirira pa milomo yawo.’
29 Ohol vlasy své a zavrz, a naříkej hlasem na místech vysokých; nebo zavrhl Hospodin a opustil rodinu, na kterouž se velmi hněvá.
“Tsono meta tsitsi lako ndi kulitaya. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, pakuti Yehova waukana ndi kuwusiya mʼbado umene wamukwiyitsawu.”
30 Činili zajisté synové Judovi, což zlého jest před očima mýma, dí Hospodin. Nastavěli ohavností svých v domě tom, kterýž nazván jest od jména mého, aby poškvrnili jej.
“Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa.
31 Nadto vzdělali výsosti Tofet, kteréž jest v údolí syna Hinnom, aby pálili syny své i dcery své ohněm, čehož jsem nepřikázal, aniž vstoupilo na srdce mé.
Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe.
32 Protož aj, dnové jdou, dí Hospodin, kdyžto nebude slouti více Tofet, ani údolí syna Hinnom, ale údolí mordu, a pochovávati budou v Tofet, nebo nebude dostávati místa.
Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika.
33 I budou mrtvá těla lidu tohoto za pokrm ptactvu nebeskému a šelmám zemským, a nebude žádného, kdo by odstrašil.
Ndipo mitembo ya anthu amenewa idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo, ndipo palibe wina amene adzazipirikitse.
34 Způsobím také, aby přestal v městech Judských a v ulicích Jeruzalémských hlas radosti a hlas veselé, hlas ženicha a hlas nevěsty; nebo pustinou učiněna bude země.
Ndidzathetsa nyimbo zonse zachisangalalo ndi zachikondwerero mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu. Sikudzamvekanso mawu a chikondwerero a mkwatibwi ndi mkwati pakuti dzikolo lidzasanduka chipululu.”