< 2 Královská 15 >
1 Léta sedmmecítmého Jeroboáma krále Izraelského kraloval Azariáš syn Amaziáše, krále Judského.
Mʼchaka cha 27 cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
2 V šestnácti letech byl, když počal kralovati, a kraloval padesáte dvě létě v Jeruzalémě. Jméno matky jeho bylo Jecholia z Jeruzaléma.
Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 16 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu.
3 Ten činil, což dobrého jest před očima Hospodinovýma vedlé všech věcí, kteréž činil Amaziáš otec jeho.
Iyeyo anachita zabwino pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake.
4 A však výsostí nezkazili, ještě lid obětoval a kadil na výsostech.
Komabe malo opembedzerako mafano sanawachotse ndipo anthu anapitirizabe kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.
5 Ranil pak Hospodin krále, tak že byl malomocný až do dne smrti své, a bydlil v domě obzvláštním. Pročež Jotam syn královský držel správu nad domem, soudě lid země.
Ndipo Yehova analanga mfumu ndi nthenda ya khate mpaka tsiku limene inamwalira. Tsono mfumuyo inkakhala mʼnyumba yakeyake yapadera. Mwana wake Yotamu ndiye amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu ndiponso ndiye amene ankalamulira anthu mʼdzikomo.
6 O jiných pak činech Azariášových, i cožkoli činil, psáno jest v knize o králích Judských.
Ntchito zina za Azariya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
7 I usnul Azariáš s otci svými, a pochovali jej s otci jeho v městě Davidově, a kraloval Jotam syn jeho místo něho.
Azariya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
8 Léta třidcátého osmého Azariáše krále Judského kraloval Zachariáš syn Jeroboamův nad Izraelem v Samaří šest měsíců.
Mʼchaka cha 38 cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira miyezi isanu ndi umodzi.
9 A činil to, což jest zlého před očima Hospodinovýma, jakž činívali otcové jeho, neuchýliv se od hříchů Jeroboáma syna Nebatova, kterýž přivedl k hřešení Izraele.
Ndipo iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira makolo ake. Iye sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.
10 I spikl se proti němu Sallum syn Jábes a bil ho před lidem, i zabil jej a kraloval místo něho.
Salumu mwana wa Yabesi anachitira chiwembu Zekariya. Anamukantha anthu akuona, namupha, ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.
11 O jiných pak věcech Zachariášových zapsáno jest v knize o králích Izraelských.
Ntchito zina za Zekariya, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
12 Toť jest slovo Hospodinovo, kteréž mluvil k Jéhu, řka: Synové tvoji do čtvrtého kolena seděti budou na stolici Izraelské. A tak se stalo.
Awa ndiwo mawu a Yehova amene anayankhula kwa Yehu kuti, “Ana ako adzalamulira Israeli mpaka mʼbado wachinayi.”
13 Sallum syn Jábesův kraloval léta třidcátého devátého Uziáše krále Judského, a kraloval jeden měsíc v Samaří.
Salumu mwana wa Yabesi anakhala mfumu mʼchaka cha 39 cha ulamuliro wa Uziya mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Samariya mwezi umodzi.
14 Nebo přitáhl Manahem syn Gádi z Tersa, a přišed do Samaří, porazil Sallum syna Jábes v Samaří, a zabiv jej, kraloval na místě jeho.
Ndipo Menahemu mwana wa Gadi anachoka ku Tiriza napita ku Samariya nakantha Salumu mwana wa Yabesi ku Samariya, namupha ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwake.
15 O jiných pak činech Sallum i spiknutí jeho, kteréž učinil, zapsáno jest v knize o králích Izraelských.
Ntchito zina za Salumu ndiponso za chiwembu chimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
16 Tehdy pohubil Manahem město Tipsach, a všecky, kteříž byli v něm, i všecky končiny jeho od Tersa, proto že mu ho neotevřeli. I pomordoval je, a všecky těhotné jejich zroztínal.
Nthawi imeneyo Menahemu, kuchokera ku Tiriza, anakathira nkhondo mzinda wa Tipisa ndi anthu onse amene anali mʼmenemo ndi dera lonse lozungulira chifukwa iwo anakana kutsekula zipata zawo. Iye anatenga katundu yense mu mzinda wa Tipisa ndi kutumbula akazi onse oyembekezera.
17 Léta třidcátého devátého Azariáše krále Judského kraloval Manahem syn Gádi nad Izraelem v Samaří za deset let.
Mʼchaka cha 39 cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira mu Samariya zaka khumi.
18 A činil to, což jest zlého před očima Hospodinovýma, neodvrátiv se od hříchů Jeroboáma syna Nebatova, (kterýž přivedl Izraele k hřešení, ) po všecky dny své.
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Nthawi yonse ya ulamuliro wake sanasiye machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.
19 Když pak vytáhl Ful král Assyrský proti zemi té, dal Manahem Fulovi deset tisíc centnéřů stříbra, aby mu byl nápomocen k utvrzení království v rukou jeho.
Tsono Puli mfumu ya ku Asiriya inadzathira nkhondo dzikolo ndipo Menahemu anapatsa Puliyo makilogalamu 34,000 a siliva kuti amuthandize ndi kulimbikitsa ufumu wake.
20 I uložil Manahem daň na Izraele, na všecky bohaté, aby dávali králi Assyrskému jeden každý po padesáti lotech stříbra. Takž obrátiv se král Assyrský, nemeškal se více tu v zemi.
Menahemu anapeza ndalamazo kudzera mu msonkho umene ankakhometsa Aisraeli. Munthu aliyense wachuma ankapereka masekeli a siliva makumi asanu kwa mfumu ya ku Asiriya. Choncho mfumu ya ku Asiriya inabwerera ndipo sinakhalenso mʼdzikomo.
21 O jiných pak činech Manahemových, a cožkoli činil, zapsáno jest v knize o králích Izraelských.
Ntchito zina za Menahemu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
22 I usnul Manahem s otci svými, a kraloval Pekachia syn jeho místo něho.
Menahemu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Pekahiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
23 Léta padesátého Azariáše, krále Judského, kraloval Pekachia syn Manahemův nad Izraelem v Samaří dvě létě.
Mʼchaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka ziwiri.
24 A činil to, což jest zlého před očima Hospodinovýma, neuchýliv se od hříchů Jeroboáma syna Nebatova, kterýž k hřešení přivedl Izraele.
Pekahiya anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Iye sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, omwe anachimwitsa nawo Israeli.
25 Tedy spuntoval se proti němu Pekach syn Romeliův, hejtman jeho, s Argobem i s Ariášem, a zabil jej v Samaří na paláci domu královského, maje s sebou padesáte mužů Galádských. A zabiv jej, kraloval místo něho.
Ndipo Peka mwana wa Remaliya, mtsogoleri wake wa ankhondo, anamuchita chiwembu. Iye pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi anapha Pekahiya pamodzi ndi Arigobu ndi Ariyeli mʼchipinda choteteza nyumba ya mfumu mu Samariya. Kotero Peka anapha Pekahiya ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.
26 Jiní pak skutkové Pekachia a všecko, což činil, zapsáno jest v knize o králích Izraelských.
Ntchito zina za Pekahiya ndi zonse zimene anachita zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
27 Léta padesátého druhého Azariáše krále Judského kraloval Pekach syn Romeliův nad Izraelem v Samaří dvadceti let.
Mʼchaka cha 52 cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira zaka makumi awiri.
28 A činil to, což jest zlého před očima Hospodinovýma, aniž odstoupil od hříchů Jeroboáma syna Nebatova, kterýž k hřešení přivedl Izraele.
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.
29 Za dnů Pekacha krále Izraelského přitáhl Tiglatfalazar král Assyrský, a vzal Jon a Abel, dům Maacha a Janoe, Kedes a Azor, i Galád a Galilei, i všecku zemi Neftalím, a přenesl obyvatele jejich do Assyrie.
Nthawi ya Peka mfumu ya Israeli, Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kudzalanda Iyoni, Abeli-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi ndi Hazori. Mfumu ya ku Asiriya inatenga Giliyadi ndi Galileya, kuphatikizanso madera onse a Nafutali ndipo anatumiza Aisraeli ku Asiriya.
30 Tedy spuntoval se Ozee syn Ela, proti Pekachovi synu Romeliovu, a raniv ho, zabil jej, a kraloval na místě jeho léta dvadcátého Jotama syna Uziášova.
Kenaka Hoseya mwana wa Ela anachitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya. Anamukantha ndi kumupha ndipo anakhala mfumu mʼmalo mwake mʼchaka makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.
31 O jiných pak činech Pekachových, a cožkoli činil, zapsáno jest v knize o králích Izraelských.
Ntchito zina za Peka ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
32 Léta druhého Pekacha syna Romelia, krále Izraelského, kraloval Jotam syn Uziáše, krále Judského.
Mʼchaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.
33 V pětmecítma letech byl, když počal kralovati, a šestnácte let kraloval v Jeruzalémě. Jméno matky jeho Jerusa, dcera Sádochova.
Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Amayi ake anali Yerusa mwana wa Zadoki.
34 A činil to, což pravého jest před očima Hospodinovýma. Všecko, jakž činil Uziáš otec jeho, tak činil.
Iye anachita zabwino pamaso pa Yehova monga anachitira Uziya abambo ake.
35 A však výsosti nebyly zkaženy, ještě lid obětoval a kadil na výsostech. On vystavěl bránu hořejší domu Hospodinova.
Komabe malo opembedzera mafano sanawachotse ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.
36 O jiných pak činech Jotamových, a cožkoli činil, zapsáno jest v knize o králích Judských.
Ntchito zina za Yotamu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
37 Za dnů těch počal Hospodin posílati na Judu Rezina krále Syrského a Pekacha syna Romeliova.
(Nthawi imeneyo, Yehova anayamba kumatuma Rezini mfumu ya Aaramu ndi Peka mwana wa Remaliya kudzamenyana ndi Yuda).
38 I usnul Jotam s otci svými, a pochován jest s otci svými v městě Davida otce svého. I kraloval Achas syn jeho místo něho.
Yotamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Ahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.