< Jošua 10 >
1 A kad ču jeruzalemski kralj Adoni-Sedek da je Jošua zauzeo Aj i da ga je izručio “heremu”, kletom uništenju, kao što je učinio s Jerihonom i njegovim kraljem, i da su stanovnici Gibeona učinili mir s Izraelom i uključili se među njih,
Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo.
2 vrlo se uplaši, jer je Gibeon bio značajan kao kakav kraljevski grad, veći od Aja, a svi žitelji njegovi bijahu ratnici.
Choncho iye ndi anthu ake anachita mantha aakulu, chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu kwambiri, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.
3 Zato jeruzalemski kralj Adoni-Sedek poruči Hohamu, kralju hebronskom, Piramu, kralju jarmutskom, Jafiji, kralju lakiškom, i Debiru, kralju eglonskom:
Chotsatira chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu inatuma uthenga kwa Hohamu mfumu ya Hebroni, Piramu mfumu ya Yarimuti, Yafiya mfumu ya Lakisi ndi Debri mfumu ya Egiloni.
4 “Dođite k meni i pomozite mi da udarimo na Gibeon, jer je učinio mir s Jošuom i Izraelcima!”
Iye anatumiza mawu kuti, “Bwerani mudzandithandize kumenyana ndi Gibiyoni, chifukwa anthu ake achita pangano la mtendere ndi Yoswa ndi Aisraeli.”
5 Udruži se tada pet kraljeva amorejskih: kralj jeruzalemski, kralj hebronski, kralj jarmutski, kralj lakiški i kralj eglonski; krenu oni i sva njihova vojska, opsjednu grad Gibeon i počnu ga napadati.
Mafumu asanu a Aamori aja, mfumu ya Yerusalemu, mfumu ya Hebroni, mfumu ya Yarimuti, mfumu ya Lakisi ndi mfumu ya Egiloni, anagwirizana. Iwo anasonkhanitsa ankhondo awo nazungulira mzinda wa Gibiyoni ndi kuwuthira nkhondo.
6 Tada Gibeonci poručiše Jošui u tabor u Gilgalu: “Ne napuštaj svojih slugu, nego se požuri k nama da nas izbaviš i da nam pomogneš, jer su se protiv nas udružili svi amorejski kraljevi koji žive u Gorju.”
Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.”
7 I pođe Jošua iz Gilgala, a s njim i svi ratnici, sve vrsni junaci.
Choncho Yoswa ananyamuka kuchoka ku Giligala ndi gulu lake la ankhondo pamodzi ndi anthu ake olimba mtima.
8 A Jahve reče Jošui: “Ne boj se! Ja sam ih predao u tvoje ruke i nijedan od njih neće se održati pred tobom.”
Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe.”
9 I udari na njih Jošua iznenadno, pošto je svu noć išao od Gilgala.
Atayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, Yoswa anawathira nkhondo mwadzidzidzi.
10 I smete ih Jahve pred Izraelcima, koji ih teško poraziše kod Gibeona i potjeraše prema strmini kojom se uzlazi u Bet-Horon. Tukli su ih sve do Azeke i do Makede.
Yehova anachititsa mantha adani aja atangoona gulu lankhondo la Israeli. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamori ku Gibiyoni ndipo anawathamangitsa mu msewu wopita ku Beti-Horoni ndi kuwapha njira yonse yopita ku Azeka ndi Makeda.
11 A dok su bježali pred Izraelom uz bethoronsku strminu, bacao je Jahve s neba na njih tuču kamenja sve do Azeke te su ginuli. I poginulo ih je više od tuče kamene nego što su ih pobili sinovi Izraelovi svojim mačevima.
Pamene ankathawa pamaso pa Israeli pa njira yochokera ku Beti-Horoni mpaka ku Azeka, Yehova anawagwetsera matalala akuluakulu kuchokera kumwamba ndipo ambiri mwa iwo anafa ndi matalala kuposa amene anaphedwa ndi lupanga la Israeli.
12 Onoga dana kada Jahve predade Amorejce sinovima Izraelovim, obrati se Jošua Jahvi i poviče pred Izraelcima: “Stani, sunce, iznad Gibeona, i mjeseče, iznad dola Ajalona!”
Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori mʼmanja mwa Israeli, Yoswa ananena kwa Yehova pamaso pa Israeli kuti, “Iwe dzuwa, ima pamwamba pa Gibiyoni, mwezi ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”
13 I stade sunce i zaustavi se mjesec sve dok se nije narod osvetio neprijateljima svojim. Ne piše li to u knjizi Pravednika? I stade sunce nasred neba i nije se nagnulo k zapadu gotovo cio dan.
Choncho dzuwa linayima, mwezinso unayima, mpaka dziko la Israeli litagonjetsa adani ake. Zimenezi zalembedwa mʼbuku la Yasari. Dzuwa linayima pamodzimodzi pakati pa thambo mlengalenga, osayendanso kwa tsiku lathunthu.
14 Nije bilo takva dana ni prije ni poslije da bi se Jahve odazvao glasu čovječjem. Tako je Jahve vojevao za Izraela.
Sipanakhaleponso tsiku ngati limeneli kuyambira kale, tsiku limene Yehova anamvera munthu. Izi zinatero chifukwa Yehova ankamenyera nkhondo Aisraeli.
15 Potom se vrati Jošua i sav Izrael s njim u tabor gilgalski.
Kenaka Yoswa anabwerera pamodzi ndi Aisraeli onse ku misasa ku Giligala.
16 A onih pet kraljeva uteče i sakri se u pećinu kod Makede.
Mafumu asanu aja anathawa ndi kukabisala ku phanga la Makeda.
17 Javiše Jošui: “Otkriveno je pet kraljeva sakrivenih u pećini kod Makede.”
Koma Yoswa anamva kuti mafumu asanu awapeza akubisala ku phanga la Makeda.
18 A Jošua reče: “Navalite veliko kamenje pećini na otvor i postavite ljude pred nju da je čuvaju.
Tsono Yoswa analamula kuti, “Mugubuduzire miyala ikuluikulu pa khomo la phangalo, ndipo muyike anthu ena kuti azilondera.
19 A vi se drugi ne zadržavajte, nego tjerajte svoje neprijatelje i tucite ih s leđa; ne dajte im da uđu u svoje gradove, jer ih Jahve, Bog vaš, predade u vaše ruke.”
Koma inu musakhaleko! Thamangitsani adani anu, muwathire nkhondo kuchokera kumbuyo ndipo musawalole kuti akafike ku mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.”
20 A kad Jošua i sinovi Izraelovi okončaše bitku teškim pokoljem - utekla im je samo nekolicina preživjelih u tvrde gradove -
Kotero Yoswa ndi Aisraeli anapha anthu aja, kupatulapo ochepa amene anathawa nakabisala ku mizinda yawo.
21 vrati se narod zdrav i čitav k Jošui u tabor u Makedi. I nitko više ni da pisne protiv sinova Izraelovih.
Kenaka gulu lonse la ankhondo linabwerera bwinobwino kwa Yoswa ku misasa ya ku Makeda, palibe aliyense mu mzindamo amene anaputanso Aisraeli.
22 Tada reče Jošua: “Otvorite ulaz u pećinu i odande mi izvedite onih pet kraljeva.”
Yoswa anati, “Tsekulani khomo la phangalo ndipo muwabweretse kwa ine mafumu asanuwo.”
23 I učine tako, izvedu k njemu iz pećine onih pet kraljeva: kralja jeruzalemskoga, kralja hebronskoga, kralja jarmutskoga, kralja lakiškog i kralja eglonskog.
Pamenepo mafumu asanu aja anatulutsidwa, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi, ndi mfumu ya ku Egiloni.
24 A kad ih izvedoše, pozva Jošua sve Izraelce i reče vojskovođama koji su ga pratili: “Priđite i stanite svojim nogama na vratove ovih kraljeva.” Oni pristupe i stanu im svojim nogama na vratove.
Atabwera nawo kwa Yoswa, iye anayitana Aisraeli onse. Ndipo analamula akuluakulu ake amene anapita naye limodzi kuti, “Bwerani kuno ndipo apondeni pakhosi mafumuwa.”
25 Reče Jošua: “Ne bojte se i ne plašite se! Hrabri budite i odlučni, jer će tako Jahve učiniti sa svim vašim neprijateljima s kojima se budete borili.”
Yoswa anawawuza kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Khalani amphamvu ndi olimba mtima popeza umo ndi mmene Yehova adzachitire ndi adani anu onse amene mudzamenyana nawo.”
26 Potom Jošua naredi da ih pogube i objese na pet stabala; i visjeli su ondje do večeri.
Kenaka Yoswa anawabaya ndi kuwapha mafumuwo ndipo anawapachika pa mitengo isanu ndipo anakhala pamenepo mpaka madzulo.
27 A o zalasku sunčanom zapovjedi Jošua te ih skidoše s drveća i baciše u istu onu pećinu u koju se bijahu sklonili te na otvor navališe golemo kamenje, koje je i danas ondje.
Dzuwa litalowa, Yoswa analamula kuti awachotse pa mitengo ija ndi kuwaponya mʼphanga limene ankabisalamo. Pa khomo pa phangalo anayikapo miyala ikuluikulu imene ilipo mpaka lero.
28 Istoga dana zauze Jošua Makedu: udari na grad oštricom mača i pogubi kralja njegova i sve živo u gradu izruči “heremu”, kletom uništenju, ne puštajući da itko utekne. I učini s kraljem makedskim kao što je učinio s kraljem jerihonskim.
Tsiku lomwelo Yoswa analanda mzinda wa Makeda. Iye anapha anthu a mu mzindamo ndi mfumu yake ndipo sanasiye aliyense wamoyo. Yoswa anachita ndi mfumu ya ku Makeda monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.
29 Ode zatim Jošua i sav Izrael iz Makede u Libnu i udari na nju.
Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Makeda nakafika ku Libina ndi kuthira nkhondo mzindawo.
30 I nju Jahve i njena kralja predade u ruke Izraelu, koji oštricom mača pobi sve živo u njoj; ne poštedje nikoga, a s kraljem Libne učini što i s kraljem jerihonskim.
Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Aisraeli. Ndipo Yoswa anapha onse amene anali mu mzindamo. Palibe amene anatsala wamoyo. Ndipo Yoswa anachita ndi mfumu ya Libina monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko.
31 Potom ode Jošua i svi Izraelci iz Libne u Lakiš, opsjede ga i napade.
Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Libina kupita ku Lakisi. Iye anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo.
32 Jahve predade Lakiš u ruke Izraela, koji ga osvoji sutradan: pobiše oštricom mača sve živo u njemu, onako kao što su učinili s Libnom.
Yehova anapereka Lakisi kwa Israeli; ndipo Yoswa anawulanda pa tsiku lachiwiri. Monga anachita ndi mzinda wa Libina, Yoswa anapha anthu onse okhala mu mzinda wa Lakisi, ndipo palibe amene anatsala ndi moyo.
33 Tada ustade Horam, kralj Gezera, da pomogne Lakišu, ali Jošua porazi njega i njegov narod tako te nitko ne preživje.
Nthawi imeneyi nʼkuti Horamu mfumu ya Gezeri itabwera kudzathandiza Lakisi koma Yoswa anamugonjetsa pamodzi ndi asilikali ake ndipo palibe anatsala wamoyo.
34 Jošua krenu zatim sa svim Izraelcima od Lakiša na Eglon. Opsjedoše grad i napadoše ga.
Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Lakisi nakafika ku Egiloni. Iwo anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo.
35 Osvojiše ga još istoga dana i pobiše sve oštricom mača. Sve živo izručiše kletom uništenju, kako su učinili s Lakišem.
Anawulanda tsiku lomwelo ndipo anapha aliyense amene anali mu mzindawo monga momwe anachitira ku Lakisi.
36 Onda Jošua sa svim Izraelom krenu od Eglona na Hebron i napade ga.
Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anachoka ku Egiloni nakafika ku Hebroni ndi kukawuthira nkhondo.
37 Osvojiše ga i pobiše sve oštricom mača, kralja i stanovništvo u svim mjestima koja mu pripadaju, ne poštedjevši nikoga. Učini s njime kao s Eglonom. Grad sa svim svojim stanovništvom bi izručen kletom uništenju.
Iwo analanda mzindawo napha ndi lupanga mfumu yake pamodzi ndi onse amene ankakhala mʼmenemo. Monga anachita ndi mzinda wa Egiloni, kuti sanasiye aliyense ndi moyo, anachitanso chimodzimodzi ndi mzinda wa Hebroni.
38 Napokon krenu Jošua i sav Izrael s njim na Debir i napadoše ga.
Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anatembenukira mzinda wa Debri ndi kukawuthira nkhondo.
39 Osvojiše ga i razoriše; kralja njegova i žitelje okolnih mjesta pobiše oštricom mača. Kletom uništenju izručiše sve njegovo stanovništvo. Ne poštedješe nikoga. I učini Jošua s Debirom i njegovim kraljem kao što je učinio s Hebronom i njegovim kraljem, s Libnom i njezinim kraljem.
Iwo analanda mzindawo ndi midzi ndi kupha mfumu yake pamodzi ndi onse okhala mʼmenemo. Anachita ndi mzinda wa Debri pamodzi ndi mfumu yake zofanana ndi zimene anachita ndi mzinda wa Libina ndi wa Hebroni.
40 Tako je Jošua zauzeo sav onaj kraj: Gorje i Negeb, Šefelu i Visočje - i sve njihove kraljeve. Ne ostavi preživjelih, već izruči kletom uništenju sve što je disalo, kako je zapovjedio Jahve, Bog Izraelov.
Motero Yoswa anagonjetsa dziko lonselo. Anapha mafumu onse a dera la kumapiri, dera la kummawa, dera la kumadzulo mʼmphepete mwa phiri, ndiponso dera la ku magomo, kummwera. Iye sanasiye wina aliyense wamoyo. Anapha onse amene anali moyo monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli analamulira.
41 I pobi ih Jošua sve od Kadeš Barnee do Gaze i sav kraj Gošen do Gibeona.
Yoswa anawagonjetsa iwo kuyambira ku Kadesi Barinea mpaka ku Gaza, ndiponso kuchokera ku chigawo chonse cha Goseni mpaka ku Gibiyoni.
42 Sve tamošnje kraljeve i zemlje njihove zauze Jošua ujedanput, jer se za Izraela borio Jahve, Bog Izraelov.
Yoswa anagonjetsa mafumu onsewa ndi kulanda dziko lawo kamodzinʼkamodzi chifukwa Yehova Mulungu wa Israeli anawamenyera nkhondo.
43 Naposljetku se Jošua i sav Izrael vratiše u tabor u Gilgalu.
Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anabwerera ku misasa yawo ku Giligala.