< 詩篇 60 >

1 大衛與兩河間的亞蘭並瑣巴的亞蘭爭戰的時候,約押轉回,在鹽谷攻擊以東,殺了一萬二千人。那時,大衛作這金詩,叫人學習,交與伶長。調用為證的百合花。 上帝啊,你丟棄了我們,使我們破敗; 你向我們發怒,求你使我們復興!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere. Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza. Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
2 你使地震動,而且崩裂; 求你將裂口醫好,因為地搖動。
Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba, konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
3 你叫你的民遇見艱難; 你叫我們喝那使人東倒西歪的酒。
Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto; inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.
4 你把旌旗賜給敬畏你的人, 可以為真理揚起來。 (細拉)
Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera kuti tisonkhanireko pothawa uta.
5 求你應允我們,用右手拯救我們, 好叫你所親愛的人得救。
Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja, kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
6 上帝已經指着他的聖潔說:我要歡樂; 我要分開示劍,丈量疏割谷。
Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika: “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.
7 基列是我的,瑪拿西也是我的。 以法蓮是護衛我頭的; 猶大是我的杖。
Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso; Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera, Yuda ndi ndodo yanga yaufumu
8 摩押是我的沐浴盆; 我要向以東拋鞋。 非利士啊,你還能因我歡呼嗎?
Mowabu ndi mbale yanga yosambira, pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga, pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”
9 誰能領我進堅固城? 誰能引我到以東地?
Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa? Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
10 上帝啊,你不是丟棄了我們嗎? 上帝啊,你不和我們的軍兵同去嗎?
Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.
11 求你幫助我們攻擊敵人, 因為人的幫助是枉然的。
Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu, pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.
12 我們倚靠上帝才得施展大能, 因為踐踏我們敵人的就是他。
Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano ndipo tidzapondaponda adani athu.

< 詩篇 60 >