< 詩篇 5 >
1 大衛的詩,交與伶長。用吹的樂器。 耶和華啊,求你留心聽我的言語, 顧念我的心思!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide. Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova, ganizirani za kusisima kwanga
2 我的王我的上帝啊,求你垂聽我呼求的聲音! 因為我向你祈禱。
Mverani kulira kwanga kofuna thandizo, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.
3 耶和華啊,早晨你必聽我的聲音; 早晨我必向你陳明我的心意,並要警醒!
Mmawa, Yehova mumamva mawu anga; Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu ndi kudikira mwachiyembekezo.
4 因為你不是喜悅惡事的上帝, 惡人不能與你同居。
Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa; choyipa sichikhala pamaso panu.
5 狂傲人不能站在你眼前; 凡作孽的,都是你所恨惡的。
Onyada sangathe kuyima pamaso panu; Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.
6 說謊言的,你必滅絕; 好流人血弄詭詐的,都為耶和華所憎惡。
Mumawononga iwo amene amanena mabodza; anthu akupha ndi achinyengo, Yehova amanyansidwa nawo.
7 至於我,我必憑你豐盛的慈愛進入你的居所; 我必存敬畏你的心向你的聖殿下拜。
Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu, ndidzalowa mʼNyumba yanu; mwa ulemu ndidzaweramira pansi kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.
8 耶和華啊,求你因我的仇敵,憑你的公義引領我, 使你的道路在我面前正直。
Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu chifukwa cha adani anga ndipo wongolani njira yanu pamaso panga.
9 因為,他們的口中沒有誠實; 他們的心裏滿有邪惡; 他們的喉嚨是敞開的墳墓; 他們用舌頭諂媚人。
Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike; mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko. Kummero kwawo kuli ngati manda apululu; ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.
10 上帝啊,求你定他們的罪! 願他們因自己的計謀跌倒; 願你在他們許多的過犯中把他們逐出, 因為他們背叛了你。
Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu! Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo. Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri, pakuti awukira Inu.
11 凡投靠你的,願他們喜樂,時常歡呼, 因為你護庇他們; 又願那愛你名的人都靠你歡欣。
Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere; lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe. Aphimbeni ndi chitetezo chanu, iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.
12 因為你必賜福與義人; 耶和華啊,你必用恩惠如同盾牌四面護衛他。
Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama; mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.