< 詩篇 141 >
1 大衛的詩。 耶和華啊,我曾求告你, 求你快快臨到我這裏! 我求告你的時候, 願你留心聽我的聲音!
Salimo la Davide. Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.
2 願我的禱告如香陳列在你面前! 願我舉手祈求,如獻晚祭!
Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga.
4 求你不叫我的心偏向邪惡, 以致我和作孽的人同行惡事; 也不叫我吃他們的美食。
Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.
5 任憑義人擊打我,這算為仁慈; 任憑他責備我,這算為頭上的膏油; 我的頭不要躲閃。 正在他們行惡的時候,我仍要祈禱。
Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.
6 他們的審判官被扔在巖下; 眾人要聽我的話,因為這話甘甜。
Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri, ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.
7 我們的骨頭散在墓旁, 好像人耕田、刨地的土塊。 (Sheol )
Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza, ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.” (Sheol )
8 主-耶和華啊,我的眼目仰望你; 我投靠你,求你不要將我撇得孤苦!
Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse; ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.
9 求你保護我脫離惡人為我設的網羅 和作孽之人的圈套!
Mundipulumutse ku misampha imene anditchera, ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.
Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo, mpaka ine nditadutsa mwamtendere.