< 詩篇 120 >
1 上行(或譯登階,下同)之詩。 我在急難中求告耶和華, 他就應允我。
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha.
2 耶和華啊,求你救我脫離說謊的嘴唇和詭詐的舌頭!
Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza, ndi kwa anthu achinyengo.
3 詭詐的舌頭啊,要給你甚麼呢? 要拿甚麼加給你呢?
Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?
Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.
Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!
Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere.
Ine ndine munthu wamtendere; koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.