< 民數記 22 >
1 以色列人起行,在摩押平原、約旦河東,對着耶利哥安營。
Aisraeli anayenda kupita ku zigwa za Mowabu nakamanga misasa yawo tsidya lina la Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko.
2 以色列人向亞摩利人所行的一切事,西撥的兒子巴勒都看見了。
Tsono Balaki mwana wa Zipori anaona zonse zimene Aisraeli anachitira Aamori,
ndipo Amowabu anaopa anthuwo chifukwa analipo ambiri. Amowabuwo anachita mantha kwambiri mpaka ananjenjemera chifukwa cha Aisraeli.
4 對米甸的長老說:「現在這眾人要把我們四圍所有的一概餂盡,就如牛餂盡田間的草一般。」那時西撥的兒子巴勒作摩押王。
Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.” Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo,
5 他差遣使者往大河邊的毗奪去,到比珥的兒子巴蘭本鄉那裏,召巴蘭來,說:「有一宗民從埃及出來,遮滿地面,與我對居。
anatumiza amithenga kwa Balaamu mwana wa Beori, yemwe anali ku Petori, pafupi ndi mtsinje, mʼdziko la kwawo kuti akamuyitane. Balaki anati: “Taonani, anthu ochokera ku Igupto abwera, adzaza dziko lonse ndipo akufuna kuchita nane nkhondo.
6 這民比我強盛,現在求你來為我咒詛他們,或者我能得勝,攻打他們,趕出此地。因為我知道,你為誰祝福,誰就得福;你咒詛誰,誰就受咒詛。」
Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.”
7 摩押的長老和米甸的長老手裏拿着卦金,到了巴蘭那裏,將巴勒的話都告訴了他。
Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena.
8 巴蘭說:「你們今夜在這裏住宿,我必照耶和華所曉諭我的回報你們。」摩押的使臣就在巴蘭那裏住下了。
Balaamu anawawuza kuti, “Mugone konkuno usiku uno, ndipo ndikuyankhani zomwe Yehova andiwuze.” Choncho akuluakulu a Amowabu anagona kwa Balaamu.
9 上帝臨到巴蘭那裏,說:「在你這裏的人都是誰?」
Mulungu anabwera kwa Balaamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iwewa ndani?”
10 巴蘭回答說:「是摩押王西撥的兒子巴勒打發人到我這裏來,說:
Balaamu anayankha Mulungu kuti, “Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ananditumizira uthenga uwu:
11 『從埃及出來的民遮滿地面,你來為我咒詛他們,或者我能與他們爭戰,把他們趕出去。』」
‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’”
12 上帝對巴蘭說:「你不可同他們去,也不可咒詛那民,因為那民是蒙福的。」
Koma Mulungu anawuza Balaamu kuti, “Usapite nawo. Usawatemberere anthu amenewo chifukwa ndi odalitsika.”
13 巴蘭早晨起來,對巴勒的使臣說:「你們回本地去吧,因為耶和華不容我和你們同去。」
Mmawa mwake Balaamu anadzuka ndi kuwuza akuluakulu a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko la kwanu chifukwa Yehova sanandilole kuti ndipite nanu.”
14 摩押的使臣就起來,回巴勒那裏去,說:「巴蘭不肯和我們同來。」
Kotero akuluakulu a Mowabu anabwerera kwa Balaki ndi kukanena kuti, “Balaamu wakana kubwera nafe.”
Kenaka Balaki anatumanso akuluakulu ena ambiri ndi olemekezeka kwambiri kuposa oyamba aja ndipo
16 他們到了巴蘭那裏,對他說:「西撥的兒子巴勒這樣說:『求你不容甚麼事攔阻你不到我這裏來,
anafika kwa Balaamu nati; “Zomwe Balaki mwana wa Zipori akunena ndi izi: ‘Usalole kuti china chilichonse chikulepheretse kubwera kwa ine,
17 因為我必使你得極大的尊榮。你向我要甚麼,我就給你甚麼;只求你來為我咒詛這民。』」
chifukwa ndidzakulipira bwino kwambiri ndipo ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene. Bwera ndipo uwatemberere anthu amenewa mʼmalo mwanga.’”
18 巴蘭回答巴勒的臣僕說:「巴勒就是將他滿屋的金銀給我,我行大事小事也不得越過耶和華-我上帝的命。
Koma Balaamu anayankha atumiki a Balaki kuti, “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingachite chilichonse chachikulu kapena chachingʼono kuposa kuchita lamulo la Yehova Mulungu wanga.
19 現在我請你們今夜在這裏住宿,等我得知耶和華還要對我說甚麼。」
Tsopano mukhale kuno usiku uno monga ena anachitira, ndidzaona chimene Yehova adzandiwuza.”
20 當夜,上帝臨到巴蘭那裏,說:「這些人若來召你,你就起來同他們去,你只要遵行我對你所說的話。」
Usiku umenewo Mulungu anabwera kwa Balaamu ndipo anati, “Popeza anthu awa abwera kudzakuyitana, nyamuka, pita nawo koma ukachite zokhazo zimene ndikuwuze.”
21 巴蘭早晨起來,備上驢,和摩押的使臣一同去了。
Balaamu anadzuka mmawa, namanga bulu wake wamkazi ndipo anapita ndi akuluakulu a Mowabu.
22 上帝因他去就發了怒;耶和華的使者站在路上敵擋他。他騎着驢,有兩個僕人跟隨他。
Koma Mulungu anakwiya kwambiri pamene ankapita ndipo mngelo wa Yehova anayima pa njira kutsutsana naye. Balaamu anakwera bulu wake wamkazi ndipo antchito ake awiri anali naye.
23 驢看見耶和華的使者站在路上,手裏有拔出來的刀,就從路上跨進田間,巴蘭便打驢,要叫牠回轉上路。
Pamene buluyo anaona mngelo wa Yehova atayima pa njira ndi lupanga mʼmanja mwake, anapatukira kumbali kwa msewu napita kutchire. Balaamu anamumenya kuti abwerere mu msewu.
24 耶和華的使者就站在葡萄園的窄路上;這邊有牆,那邊也有牆。
Kenaka mngelo wa Yehova anayima mʼkanjira kakangʼono pakati pa minda iwiri ya mpesa yokhala ndi makoma mbali zonse
25 驢看見耶和華的使者,就貼靠牆,將巴蘭的腳擠傷了;巴蘭又打驢。
Bulu uja ataona mngelo wa Yehova anadzipanikiza ku khoma, kukhukhuza phazi la Balaamu kukhomako. Ndipo pomwepo Balaamu anamenya buluyo kachiwiri.
26 耶和華的使者又往前去,站在狹窄之處,左右都沒有轉折的地方。
Kenaka mngelo wa Yehova anapita patsogolo ndi kuyima pamalo opanikizika pomwe panalibe poti nʼkutembenukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere.
27 驢看見耶和華的使者,就臥在巴蘭底下,巴蘭發怒,用杖打驢。
Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anagona pansi Balaamu ali pa msana, ndipo iye anakwiya ndi kumumenya ndi ndodo yake.
28 耶和華叫驢開口,對巴蘭說:「我向你行了甚麼,你竟打我這三次呢?」
Pamenepo Yehova anayankhulitsa bulu uja, ndipo buluyo anati kwa Balaamu, “Ndakuchitirani chiyani kuti mundimenye katatuka?”
29 巴蘭對驢說:「因為你戲弄我,我恨不能手中有刀,把你殺了。」
Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.”
30 驢對巴蘭說:「我不是你從小時直到今日所騎的驢嗎?我素常向你這樣行過嗎?」巴蘭說:「沒有。」
Buluyo anati kwa Balaamu, “Kodi sindine bulu wanu, amene mumakwera nthawi zonse kufikira lero? Kodi ndinakuchitiranipo zoterezi?” Iye anati “Ayi.”
31 當時,耶和華使巴蘭的眼目明亮,他就看見耶和華的使者站在路上,手裏有拔出來的刀,巴蘭便低頭俯伏在地。
Pomwepo Yehova anatsekula maso Balaamu ndipo anaona mngelo wa Yehovayo ali chiyimire pa njira ndi lupanga losolola. Tsono iye anawerama nalambira pamaso pake.
32 耶和華的使者對他說:「你為何這三次打你的驢呢?我出來敵擋你,因你所行的,在我面前偏僻。
Mngelo wa Yehova anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako katatu? Taona, Ine ndabwera kudzakutsutsa chifukwa ulendo wakowu ndi woyipa pamaso panga.
33 驢看見我就三次從我面前偏過去;驢若沒有偏過去,我早把你殺了,留牠存活。」
Buluyu anandiona ndi kupatuka katatu aka. Akanakhala kuti sanapatuke, ndikanakupha tsopano, koma buluyu nʼkanamusiya ndi moyo.”
34 巴蘭對耶和華的使者說:「我有罪了。我不知道你站在路上阻擋我;你若不喜歡我去,我就轉回。」
Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.”
35 耶和華的使者對巴蘭說:「你同這些人去吧!你只要說我對你說的話。」於是巴蘭同着巴勒的使臣去了。
Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki.
36 巴勒聽見巴蘭來了,就往摩押京城去迎接他;這城是在邊界上,在亞嫩河旁。
Balaki atamva kuti Balaamu akubwera, anapita kukakumana naye ku mzinda wa Mowabu umene unali mʼmalire a Arinoni, mʼmphepete mwa dziko lake.
37 巴勒對巴蘭說:「我不是急急地打發人到你那裏去召你嗎?你為何不到我這裏來呢?我豈不能使你得尊榮嗎?」
Balaki anati kwa Balaamu, “Kodi sindinakutumizire uthenga woti ubwere msanga? Chifukwa chiyani sunabwere kwa ine? Kodi sindingathe kukulipira mokwanira?”
38 巴蘭說:「我已經到你這裏來了!現在我豈能擅自說甚麼呢?上帝將甚麼話傳給我,我就說甚麼。」
Balaamu anayankha Balaki kuti, “Taonani, ndabwera kwa inu lero, kodi ine ndili ndi mphamvu zoti nʼkuyankhula chilichonse? Inetu ndiyenera kuyankhula zokhazo zimene Mulungu wandiwuza.”
Pamenepo Balaamu anapita pamodzi ndi Balaki ku Kiriati-Huzoti.
Balaki anapereka nsembe ngʼombe ndi nkhosa, ndipo anapereka zina kwa Balaamu ndi kwa akuluakulu omwe anali naye.
41 到了早晨,巴勒領巴蘭到巴力的高處;巴蘭從那裏觀看以色列營的邊界。
Mmawa mwake Balaki anatenga Balaamu napita limodzi ku Bamoti Baala, ndipo kumeneko anakaonako gulu lina la Aisraeliwo.