< 民數記 13 >

1 耶和華曉諭摩西說:
Yehova anawuza Mose kuti,
2 「你打發人去窺探我所賜給以色列人的迦南地,他們每支派中要打發一個人,都要作首領的。」
“Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.”
3 摩西就照耶和華的吩咐從巴蘭的曠野打發他們去;他們都是以色列人的族長。
Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli.
4 他們的名字:屬呂便支派的有撒刻的兒子沙母亞。
Mayina awo ndi awa: kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri;
5 屬西緬支派的有何利的兒子沙法。
kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori;
6 屬猶大支派的有耶孚尼的兒子迦勒。
kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune;
7 屬以薩迦支派的有約色的兒子以迦。
kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe;
8 屬以法蓮支派的有嫩的兒子何希阿。
kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni;
9 屬便雅憫支派的有拉孚的兒子帕提。
kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu;
10 屬西布倫支派的有梭底的兒子迦疊。
kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi;
11 約瑟的子孫,屬瑪拿西支派的有穌西的兒子迦底。
kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi;
12 屬但支派的有基瑪利的兒子亞米利。
kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali;
13 屬亞設支派的有米迦勒的兒子西帖。
kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli;
14 屬拿弗他利支派的有縛西的兒子拿比。
kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi;
15 屬迦得支派的有瑪基的兒子臼利。
kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki.
16 這就是摩西所打發、窺探那地之人的名字。摩西就稱嫩的兒子何希阿為約書亞。
Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa).
17 摩西打發他們去窺探迦南地,說:「你們從南地上山地去,
Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri.
18 看那地如何,其中所住的民是強是弱,是多是少,
Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri.
19 所住之地是好是歹,所住之處是營盤是堅城。
Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga?
20 又看那地土是肥美是瘠薄,其中有樹木沒有。你們要放開膽量,把那地的果子帶些來。」(那時正是葡萄初熟的時候。)
Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa).
21 他們上去窺探那地,從尋的曠野到利合,直到哈馬口。
Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati.
22 他們從南地上去,到了希伯崙;在那裏有亞衲族人亞希幔、示篩、撻買。(原來希伯崙城被建造比埃及的鎖安城早七年。)
Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto).
23 他們到了以實各谷,從那裏砍了葡萄樹的一枝,上頭有一掛葡萄,兩個人用槓抬着,又帶了些石榴和無花果來。(
Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu.
24 因為以色列人從那裏砍來的那掛葡萄,所以那地方叫做以實各谷。)
Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko.
25 過了四十天,他們窺探那地才回來,
Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija.
26 到了巴蘭曠野的加低斯,見摩西、亞倫,並以色列的全會眾,回報摩西、亞倫,並全會眾,又把那地的果子給他們看;
Ndipo atabwerako anapita kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa Aisraeli onse ku Kadesi mʼchipululu cha Parani. Kumeneko anafotokozera anthu onse nawaonetsanso zipatso za mʼdzikolo.
27 又告訴摩西說:「我們到了你所打發我們去的那地,果然是流奶與蜜之地;這就是那地的果子。
Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi.
28 然而住那地的民強壯,城邑也堅固寬大,並且我們在那裏看見了亞衲族的人。
Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko.
29 亞瑪力人住在南地;赫人、耶布斯人、亞摩利人住在山地;迦南人住在海邊並約旦河旁。」
Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.”
30 迦勒在摩西面前安撫百姓,說:「我們立刻上去得那地吧!我們足能得勝。」
Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.”
31 但那些和他同去的人說:「我們不能上去攻擊那民,因為他們比我們強壯。」
Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.”
32 探子中有人論到所窺探之地,向以色列人報惡信,說:「我們所窺探、經過之地是吞吃居民之地,我們在那裏所看見的人民都身量高大。
Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali.
33 我們在那裏看見亞衲族人,就是偉人;他們是偉人的後裔。據我們看,自己就如蚱蜢一樣;據他們看,我們也是如此。」
Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.”

< 民數記 13 >