< 尼希米記 5 >

1 百姓和他們的妻大大呼號,埋怨他們的弟兄猶大人。
Tsono anthu ena ndi akazi awo anayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzawo.
2 有的說:「我們和兒女人口眾多,要去得糧食度命」;
Ena ankanena kuti, “Ife ndi ana athu aamuna ndi aakazi, tilipo ochuluka kwambiri. Choncho tikufuna tirigu kuti tidye ndi kukhala ndi moyo.”
3 有的說:「我們典了田地、葡萄園、房屋,要得糧食充飢」;
Panali ena amene ankanena kuti, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu ya mphesa ndi nyumba zathu ngati chikole kuti tipeze tirigu chifukwa njala yakula.”
4 有的說:「我們已經指着田地、葡萄園,借了錢給王納稅。
Panalinso ena amene ankanena kuti, “ife tinachita kukongola ndalama zoti tipereke msonkho wa minda ndi mitengo yathu ya mphesa kwa mfumu.
5 我們的身體與我們弟兄的身體一樣;我們的兒女與他們的兒女一般。現在我們將要使兒女作人的僕婢,我們的女兒已有為婢的;我們並無力拯救,因為我們的田地、葡萄園已經歸了別人。」
Ngakhale kuti ndife amodzi ndi abale athuwa, ndipo ngakhalenso ana athu ndi ofanana ndi ana awo, ife tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo. Ena mwa ana athu aakazi atengedwa kale ukapolo. Ife tilibe mphamvu yochitapo kanthu popeza anthu ena anatenga kale minda yathu ndi mitengo yathu ya mphesa.”
6 我聽見他們呼號說這些話,便甚發怒。
Nditamva madandawulo awo ndi zimene amanenazi ndinapsa mtima kwambiri.
7 我心裏籌劃,就斥責貴冑和官長說:「你們各人向弟兄取利!」於是我招聚大會攻擊他們。
Nditalingalira bwino ndinatsimikiza zoti ndichitepo kanthu ndipo kenaka ndinawadzudzula anthu olemekezeka ndi akuluakuluwo. Ndinawawuza kuti, “Zoona ndithu inu nʼkumalipiritsana chiwongoladzanja chachikulu anthu apachibale nokhanokha!” Choncho ndinayitanitsa msonkhano waukulu kuti ndiwazenge mlandu
8 我對他們說:「我們盡力贖回我們弟兄,就是賣與外邦的猶大人;你們還要賣弟兄,使我們贖回來嗎?」他們就靜默不語,無話可答。
ndipo ndinati, “Monga zakhaliramu ife tikutha kuwombola abale anthu amene anagulitsidwa ukapolo kwa anthu ena. Kodi tsopano inu mukugulitsanso abale anu kwa anzawo kuti ife tiwumirizidwe kuwawombola?” Iwo anakhala chete, chifukwa sanapeze mawu oti anene.
9 我又說:「你們所行的不善!你們行事不當敬畏我們的上帝嗎?不然,難免我們的仇敵外邦人毀謗我們。
Kotero ndinapitiriza kunena kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi inu simungakhale ndi moyo woopa Mulungu wathu kuti tipewe kunyoza kwa adani athu, anthu a mitunda inayi?
10 我和我的弟兄與僕人也將銀錢糧食借給百姓;我們大家都當免去利息。
Ine ndi abale anga ndiponso antchito anga tikuwakongozanso anthuwa ndalama ndi tirigu. Ndipo tiyeni tilekeretu zolandira chiwongoladzanja!
11 如今我勸你們將他們的田地、葡萄園、橄欖園、房屋,並向他們所取的銀錢、糧食、新酒,和油,百分之一的利息都歸還他們。」
Abwezereni lero lomwe minda yawo, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndiponso nyumba zawo. Muwabwezerenso chiwongoladzanja cha ndalama, tirigu, vinyo ndi mafuta zimene munatenga.”
12 眾人說:「我們必歸還,不再向他們索要,必照你的話行。」我就召了祭司來,叫眾人起誓,必照着所應許的而行。
Iwo anayankha kuti, “Ife tidzawabwezera zimenezi popanda kupemphapo kanthu kalikonse kwa iwo. Tidzachita monga mwanena.” Pambuyo pake ndinayitanitsa ansembe ndipo pamaso pawo ndinawalumbiritsa atsogoleriwo ndi akuluakuluwo kuti adzachitadi zomwe analonjezazo.
13 我也抖着胸前的衣襟,說:「凡不成就這應許的,願上帝照樣抖他離開家產和他勞碌得來的,直到抖空了。」會眾都說:「阿們!」又讚美耶和華。百姓就照着所應許的去行。
Ndipo inenso ndinakutumula chovala changa ndi kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu wosasunga malonjezano ake. Amulande nyumba yake ndi katundu wake ndi kumusandutsa mʼmphawi!” Apo msonkhano wonse unati, “Ameni” natamanda Yehova. Ndipo anthu aja anachita monga analonjezera.
14 自從我奉派作猶大地的省長,就是從亞達薛西王二十年直到三十二年,共十二年之久,我與我弟兄都沒有吃省長的俸祿。
Ndiponso kuyambira nthawi imene anandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda, kuchokera chaka cha makumi awiri mpaka chaka cha 32 muulamuliro wa ufumu wa Aritasasita, ndiye kuti kwa zaka zokwana 12, ine ngakhale abale anga sitinalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa.
15 在我以前的省長加重百姓的擔子,每日索要糧食和酒,並銀子四十舍客勒,就是他們的僕人也轄制百姓;但我因敬畏上帝不這樣行。
Koma abwanamkubwa akale ankasautsa anthu. Iwo ankalanda anthu chakudya ndi vinyo ndi kuwalipiritsanso masekeli asiliva makumi anayi. Ngakhalenso antchito awo amavutitsa anthu kwambiri. Koma ine sindinachite zimenezo chifukwa ndimaopa Mulungu.
16 並且我恆心修造城牆,並沒有置買田地;我的僕人也都聚集在那裏做工。
Ndiponso ndinadzipereka kugwira ntchito yomanga khoma la mzinda wa Yerusalemu popanda ngakhale kugulapo munda. Antchito anganso anasonkhana komweko kuti agwire ntchito ndipo sitinafunenso malo ena.
17 除了從四圍外邦中來的猶大人以外,有猶大平民和官長一百五十人在我席上吃飯。
Kuwonjezera apa, ndinkadyetsa Ayuda, akuluakulu kuphatikizanso anthu amene ankabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ya anthu otizungulira okwanira 150.
18 每日預備一隻公牛,六隻肥羊,又預備些飛禽;每十日一次,多預備各樣的酒。雖然如此,我並不要省長的俸祿,因為百姓服役甚重。
Tsiku lililonse pamaphikidwa ngʼombe imodzi, nkhosa zabwino zisanu ndi imodzi pamodzi ndi nkhuku. Ndipo pakutha pa masiku khumi aliwonse pankakhala matumba achikopa ochuluka a vinyo wa mitundu yonse. Ngakhale zinali choncho, Ine sindinatenge chakudya choperekedwa kwa bwanamkubwa, chifukwa izi zinali zosautsa anthu.
19 我的上帝啊,求你記念我為這百姓所行的一切事,施恩與我。
Kuti zinthu zindiyendere bwino, kumbukirani Yehova Mulungu wanga pa zonse zimene ndachitira anthu awa.

< 尼希米記 5 >