< 那鴻書 3 >
1 禍哉!這流人血的城, 充滿謊詐和強暴- 搶奪的事總不止息。
Tsoka kwa mzinda wopha anthu, mzinda wodzaza ndi mabodza, mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo, mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse!
Kulira kwa zikwapu, mkokomo wa mikombero, kufuwula kwa akavalo ndiponso phokoso la magaleta!
3 馬兵爭先,刀劍發光, 槍矛閃爍,被殺的甚多, 屍首成了大堆, 屍骸無數,人碰着而跌倒,
Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo, kungʼanima kwa malupanga ndi kunyezimira kwa mikondo! Anthu ambiri ophedwa, milumilu ya anthu akufa, mitembo yosawerengeka, anthu akupunthwa pa mitemboyo.
4 都因那美貌的妓女多有淫行, 慣行邪術,藉淫行誘惑列國, 用邪術誘惑多族。
Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere, wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga, amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake, ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.
5 萬軍之耶和華說:我與你為敵; 我必揭起你的衣襟,蒙在你臉上, 使列國看見你的赤體, 使列邦觀看你的醜陋。
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikutsutsana nawe. Ndidzakuvula chovala chako. Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wako ndipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse.
6 我必將可憎污穢之物拋在你身上, 辱沒你,為眾目所觀。
Ndidzakuthira zonyansa, ndidzakuchititsa manyazi ndiponso kukusandutsa chinthu choseketsa.
7 凡看見你的,都必逃跑離開你, 說:尼尼微荒涼了!有誰為你悲傷呢? 我何處尋得安慰你的人呢?
Onse amene adzakuona adzakuthawa ndipo adzati, ‘Ninive wasanduka bwinja, adzamulira ndani?’ Kodi ndingamupeze kuti munthu woti nʼkukutonthoza?”
8 你豈比挪亞們強呢? 挪亞們坐落在眾河之間,周圍有水; 海作她的濠溝, 又作她的城牆。
Kodi ndiwe wopambana Tebesi, mzinda wokhala mʼmbali mwa Nailo, wozunguliridwa ndi madzi? Mtsinjewo unali chitetezo chake, madziwo anali linga lake.
9 古實和埃及是她無窮的力量; 弗人和路比族是她的幫手。
Mphamvu zake zinali Kusi ndi Igupto, Puti ndi Libiya anali ena mwa abwenzi ake.
10 但她被遷移,被擄去; 她的嬰孩在各市口上也被摔死。 人為她的尊貴人拈鬮; 她所有的大人都被鍊子鎖着。
Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa ndipo anapita ku ukapolo. Ana ake anawaphwanyitsa pansi mʼmisewu yonse ya mu mzindamo. Anachita maere ogawana anthu ake otchuka, ndipo anthu ake onse amphamvu anamangidwa ndi maunyolo.
11 你也必喝醉,必被埋藏, 並因仇敵的緣故尋求避難所。
Iwenso Ninive udzaledzera; udzabisala ndipo udzafunafuna malo othawirako kuopa mdani.
12 你一切保障必像無花果樹上初熟的無花果, 若一搖撼就落在想吃之人的口中。
Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyu yokhala ndi zipatso zoyambirira kucha; pamene agwedeza mitengoyo, nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya.
13 你地上的人民如同婦女; 你國中的關口向仇敵敞開; 你的門閂被火焚燒。
Tayangʼana ankhondo ako, onse ali ngati akazi! Zipata za dziko lako zatsekukira adani ako; moto wapsereza mipiringidzo yake.
14 你要打水預備受困; 要堅固你的保障, 踹土和泥,修補磚窯。
Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu, limbitsani chitetezo chanu! Pondani dothi, ikani mʼchikombole, konzani khoma la njerwa!
15 在那裏,火必燒滅你; 刀必殺戮你, 吞滅你如同蝻子。 任你加增人數多如蝻子, 多如蝗蟲吧!
Kumeneko moto udzakupserezani; lupanga lidzakukanthani ndipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala. Chulukanani ngati ziwala, chulukanani ngati dzombe!
Mwachulukitsa chiwerengero cha anthu a malonda anu mpaka kupambana nyenyezi za mlengalenga, koma iwo ngati dzombe akuwononga dziko ndipo kenaka akuwuluka nʼkuchoka.
17 你的首領多如蝗蟲; 你的軍長彷彿成群的螞蚱, 天涼的時候齊落在籬笆上, 日頭一出便都飛去, 人不知道落在何處。
Akalonga ako ali ngati dzombe, akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombe limene lamatirira pa khoma nthawi yozizira, koma pamene dzuwa latuluka limawuluka, ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita.
18 亞述王啊,你的牧人睡覺; 你的貴冑安歇; 你的人民散在山間,無人招聚。
Iwe mfumu ya ku Asiriya, abusa ako agona tulo; anthu ako olemekezeka amwalira. Anthu ako amwazikira ku mapiri popanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa.
19 你的損傷無法醫治; 你的傷痕極其重大。 凡聽你信息的必都因此向你拍掌。 你所行的惡誰沒有時常遭遇呢?
Palibe chimene chingachize bala lako; chilonda chako sichingapole. Aliyense amene amamva za iwe amawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako, kodi alipo amene sanazilawepo nkhanza zako zosatha?