< 耶利米哀歌 1 >
1 先前滿有人民的城, 現在何竟獨坐! 先前在列國中為大的, 現在竟如寡婦; 先前在諸省中為王后的, 現在成為進貢的。
Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha, umene kale unali wodzaza ndi anthu! Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu! Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye. Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi, tsopano wasanduka kapolo.
2 她夜間痛哭,淚流滿腮; 在一切所親愛的中間沒有一個安慰她的。 她的朋友都以詭詐待她, 成為她的仇敵。
Ukulira mowawidwa mtima usiku wonse, misozi ili pa masaya pake. Mwa abwenzi ake onse, palibe ndi mmodzi yemwe womutonthoza. Abwenzi ake onse amuchitira chiwembu; onse akhala adani ake.
3 猶大因遭遇苦難, 又因多服勞苦就遷到外邦。 她住在列國中,尋不着安息; 追逼她的都在狹窄之地將她追上。
Yuda watengedwa ku ukapolo, kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa. Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina; ndipo alibe malo opumulira. Onse omuthamangitsa iye amupitirira, ndipo alibe kwina kothawira.
4 錫安的路徑因無人來守聖節就悲傷; 她的城門淒涼; 她的祭司歎息; 她的處女受艱難,自己也愁苦。
Misewu yopita ku Ziyoni ikulira, chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake. Zipata zake zonse zili pululu, ansembe akubuwula. Anamwali ake akulira, ndipo ali mʼmasautso woopsa.
5 她的敵人為首; 她的仇敵亨通; 因耶和華為她許多的罪過使她受苦; 她的孩童被敵人擄去。
Adani ake asanduka mabwana ake; odana naye akupeza bwino. Yehova wamubweretsera mavuto chifukwa cha machimo ake ambiri. Ana ake atengedwa ukapolo pamaso pa mdani.
6 錫安城的威榮全都失去。 她的首領像找不着草場的鹿; 在追趕的人前無力行走。
Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni wachokeratu. Akalonga ake ali ngati mbawala zosowa msipu; alibe mphamvu zothawira owathamangitsa.
7 耶路撒冷在困苦窘迫之時, 就追想古時一切的樂境。 她百姓落在敵人手中,無人救濟; 敵人看見,就因她的荒涼嗤笑。
Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake, Yerusalemu amakumbukira chuma chonse chimene mʼmasiku amakedzana chinali chake. Anthu ake atagwidwa ndi adani ake, panalibe aliyense womuthandiza. Adani ake ankamuyangʼana ndi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake.
8 耶路撒冷大大犯罪, 所以成為不潔之物; 素來尊敬她的,見她赤露就都藐視她; 她自己也歎息退後。
Yerusalemu wachimwa kwambiri ndipo potero wakhala wodetsedwa. Onse amene ankamulemekeza pano akumunyoza, chifukwa aona umaliseche wake. Iye mwini akubuwula ndipo akubisa nkhope yake.
9 她的污穢是在衣襟上; 她不思想自己的結局, 所以非常地敗落, 無人安慰她。 她說:耶和華啊,求你看我的苦難, 因為仇敵誇大。
Uve wake umaonekera pa zovala zake; iye sanaganizire za tsogolo lake. Nʼchifukwa chake kugwa kwake kunali kwakukulu; ndipo analibe womutonthoza. “Inu Yehova, taonani masautso anga, pakuti mdani wapambana.”
10 敵人伸手,奪取她的美物; 她眼見外邦人進入她的聖所- 論這外邦人,你曾吩咐不可入你的會中。
Adani amulanda chuma chake chonse; iye anaona mitundu ya anthu achikunja ikulowa mʼmalo ake opatulika, amene Inu Mulungu munawaletsa kulowa mu msonkhano wanu.
11 她的民都歎息,尋求食物; 他們用美物換糧食,要救性命。 他們說:耶和華啊,求你觀看, 因為我甚是卑賤。
Anthu ake onse akubuwula pamene akufunafuna chakudya; asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya kuti akhale ndi moyo. “Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani, chifukwa ine ndanyozeka.”
12 你們一切過路的人哪,這事你們不介意嗎? 你們要觀看: 有像這臨到我的痛苦沒有- 就是耶和華在他發烈怒的日子使我所受的苦?
“Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu nonse mukudutsa? Yangʼanani ndipo muone. Kodi pali mavuto ofanana ndi amene andigwerawa, amene Ambuye anandibweretsera pa tsiku la ukali wake?
13 他從高天使火進入我的骨頭, 剋制了我; 他鋪下網羅,絆我的腳, 使我轉回; 他使我終日淒涼發昏。
“Anatumiza moto kuchokera kumwamba, unalowa mpaka mʼmafupa anga. Anayala ukonde kuti ukole mapazi anga ndipo anandibweza. Anandisiya wopanda chilichonse, wolefuka tsiku lonse.
14 我罪過的軛是他手所綁的, 猶如軛繩縛在我頸項上; 他使我的力量衰敗。 主將我交在我所不能敵擋的人手中。
“Wazindikira machimo anga onse ndipo ndi manja ake anawaluka pamodzi. Machimowa afika pakhosi panga, ndipo Ambuye wandithetsa mphamvu. Iye wandipereka kwa anthu amene sindingalimbane nawo.
15 主輕棄我中間的一切勇士, 招聚多人攻擊我, 要壓碎我的少年人。 主將猶大居民踹下, 像在酒醡中一樣。
“Ambuye wakana anthu anga onse amphamvu omwe ankakhala nane: wasonkhanitsa gulu lankhondo kuti lilimbane nane, kuti litekedze anyamata anga; mʼmalo ofinyira mphesa Ambuye wapondereza anamwali a Yuda.
16 我因這些事哭泣; 我眼淚汪汪; 因為那當安慰我、救我性命的, 離我甚遠。 我的兒女孤苦, 因為仇敵得了勝。
“Chifukwa cha zimenezi ndikulira ndipo maso anga adzaza ndi misozi. Palibe aliyense pafupi woti anditonthoze, palibe aliyense wondilimbitsa mtima. Ana anga ali okhaokha chifukwa mdani watigonjetsa.
17 錫安舉手,無人安慰。 耶和華論雅各已經出令, 使四圍的人作他仇敵; 耶路撒冷在他們中間像不潔之物。
“Ziyoni wakweza manja ake, koma palibe aliyense womutonthoza. Yehova walamula kuti abale ake a Yakobo akhale adani ake; Yerusalemu wasanduka chinthu chodetsedwa pakati pawo.
18 耶和華是公義的! 他這樣待我,是因我違背他的命令。 眾民哪,請聽我的話, 看我的痛苦; 我的處女和少年人都被擄去。
“Yehova ndi wolungama, koma ndine ndinawukira malamulo ake. Imvani inu anthu a mitundu yonse; onani masautso anga. Anyamata ndi anamwali anga agwidwa ukapolo.
19 我招呼我所親愛的, 他們卻愚弄我。 我的祭司和長老正尋求食物、救性命的時候, 就在城中絕氣。
“Ndinayitana abwenzi anga koma anandinyenga. Ansembe ndi akuluakulu anga anafa mu mzinda pamene ankafunafuna chakudya kuti akhale ndi moyo.
20 耶和華啊,求你觀看, 因為我在急難中。 我心腸擾亂; 我心在我裏面翻轉, 因我大大悖逆。 在外,刀劍使人喪子; 在家,猶如死亡。
“Inu Yehova, onani mmene ine ndavutikira! Ndikuzunzika mʼkati mwanga, ndipo mu mtima mwanga ndasautsidwa chifukwa ndakhala osamvera. Mʼmisewu anthu akuphedwa, ndipo ku mudzi kuli imfa yokhayokha.
21 聽見我歎息的有人; 安慰我的卻無人! 我的仇敵都聽見我所遭的患難; 因你做這事,他們都喜樂。 你必使你報告的日子來到, 他們就像我一樣。
“Anthu amva kubuwula kwanga, koma palibe wonditonthoza. Adani anga onse amva masautso anga; iwo akusangalala pa zimene Inu mwachita. Lifikitseni tsiku limene munalonjeza lija kuti iwonso adzakhale ngati ine.
22 願他們的惡行都呈在你面前; 你怎樣因我的一切罪過待我, 求你照樣待他們; 因我歎息甚多,心中發昏。
“Lolani kuti ntchito zawo zoyipa zifike pamaso panu; muwalange ngati mmene mwandilangira ine chifukwa cha machimo anga onse. Ndikubuwula kwambiri ndipo mtima wanga walefuka.”