< 士師記 19 >
1 當以色列中沒有王的時候,有住以法蓮山地那邊的一個利未人,娶了一個猶大伯利恆的女子為妾。
Pa nthawi imeneyo ku Israeli kunalibe mfumu. Mlevi wina ankakhala kutali ku dziko lamapiri la Efereimu. Iyeyu anatenga mzikazi wa ku Betelehemu, mʼdziko la Yuda.
2 妾行淫離開丈夫,回猶大的伯利恆,到了父家,在那裏住了四個月。
Tsiku lina mzikazi uja anakwiyira mwamuna wake ndipo anamuchokera kupita kwa abambo ake ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Anakakhala kumeneko miyezi inayi.
3 她丈夫起來,帶着一個僕人、兩匹驢去見她,用好話勸她回來。女子就引丈夫進入父家。她父見了那人,便歡歡喜喜地迎接。
Mwamuna wake anamulondola kuti akayankhule naye mofatsa kumupempha kuti abwerere. Iye anali ndi antchito ake ndi abulu ake awiri. Anafika ku nyumba kwa mkazi uja ndipo iye anamulowetsa mʼnyumba ya abambo ake. Abambo aja atamuona mnyamata uja anamulandira mwachimwemwe.
4 那人的岳父,就是女子的父親,將那人留下住了三天。於是二人一同吃喝、住宿。
Mpongozi wake, yemwe anali abambo a mtsikanayo, anamupempha kuti aswere. Choncho anakhalako masiku atatu. Ankadya, kumwa ndi kugona komweko.
5 到第四天,利未人清早起來要走,女子的父親對女婿說:「請你吃點飯,加添心力,然後可以行路。」
Tsiku lachinayi anadzuka mʼmamawa kukonzekera kuti azipita kwawo, koma abambo ake a mtsikanayo anawuza mkamwini wawo uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, ndipo kenaka mutha kupita.”
6 於是二人坐下一同吃喝。女子的父親對那人說:「請你再住一夜,暢快你的心。」
Choncho onse awiri anakhala pansi ndi kudya ndi kumwa pamodzi. Atadya, abambo a mtsikanayo anati, “Chonde mugonenso konkuno musangalale.”
Ndipo pamene mwamunayo anakonzeka kuti azipita, apongozi ake anamuwumirizanso kuti asapite. Choncho anagona komweko usiku umenewo.
8 到第五天,他清早起來要走,女子的父親說:「請你吃點飯,加添心力,等到日頭偏西再走。」於是二人一同吃飯。
Mmawa wa tsiku lachisanu, atadzuka kuti azipita abambo ake a mtsikanayo anamuwuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mutandale mpaka madzulo.” Choncho awiriwo anadya pamodzi.
9 那人同他的妾和僕人起來要走,他岳父,就是女子的父親,對他說:「看哪,日頭偏西了,請你再住一夜;天快晚了,可以在這裏住宿,暢快你的心。明天早早起行回家去。」
Pambuyo pake munthu uja pamodzi ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki anakonzeka kuti azipita. Koma abambo a mtsikana uja anatinso kwa iye, “Onani tsopano kukuda. Gonani konkuno pakuti tsiku latha kale. Gonani ndipo musangalale. Mawa mudzuka mʼmamawa ndi kumapita kwanu.”
10 那人不願再住一夜,就備上那兩匹驢,帶着妾起身走了,來到耶布斯的對面(耶布斯就是耶路撒冷。)
Koma munthuyo sanafune kugonanso tsiku limenelo. Choncho ananyamuka kumapita, ndipo anakafika ku malo oyangʼanana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu ake awiri okhala ndi zokhalira zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi.
11 臨近耶布斯的時候,日頭快要落了,僕人對主人說:「我們不如進這耶布斯人的城裏住宿。」
Akuyandikira ku Yebusi nʼkuti kutada ndithu. Tsono mtumiki uja anawuza mbuye wake kuti, “Tiyeni, tipatukire ku mzinda wa Ayebusiwa ndipo tigone.”
12 主人回答說:「我們不可進不是以色列人住的外邦城,不如過到基比亞去」;
Mbuye wake anamuyankha kuti, “Ayi, tisapatukire ku mzinda wa alendo, anthu amene sali Aisraeli. Koma tipitirire mpaka ku Gibeya.”
13 又對僕人說:「我們可以到一個地方,或住在基比亞,或住在拉瑪。」
Tsono anamuwuza mtumiki wake uja kuti, “Tiye tipite ku amodzi a malo awa, ku Gibeya kapena ku Rama ndipo tikagone kumeneko.”
14 他們就往前走。將到便雅憫的基比亞,日頭已經落了;
Choncho nayenda ulendo wawo, ndipo dzuwa linawalowera akuyandikira ku Gibeya mʼdziko la Benjamini.
15 他們進入基比亞要在那裏住宿,就坐在城裏的街上,因為無人接他們進家住宿。
Ndipo anapatukira kumeneko kuti alowe mu mzinda wa Gibeya kukagona usiku umenewo. Anakalowa mu mzindamo ndi kukakhala pabwalo popeza panalibe munthu amene anawalandira ku nyumba kwake kuti akagone.
16 晚上,有一個老年人從田間做工回來。他原是以法蓮山地的人,住在基比亞;那地方的人卻是便雅憫人。
Pambuyo pake anangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito ya ku munda kwake madzulo. Iyeyu anali wa ku dziko la mapiri ku Efereimu, koma ankakhala ku Gibeya. Koma anthu a kumeneko anali a fuko la Benjamini.
17 老年人舉目看見客人坐在城裏的街上,就問他說:「你從哪裏來?要往哪裏去?」
Munthu wokalamba uja anakweza maso ndipo anaona munthu wa paulendo uja atakhala pabwalo la mzindawo, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?”
18 他回答說:「我們從猶大的伯利恆來,要往以法蓮山地那邊去。我原是那裏的人,到過猶大的伯利恆,現在我往耶和華的殿去,在這裏無人接我進他的家。
Iye anayankha kuti, “Tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda ndipo tikupita kutali ku dziko lamapiri la Efereimu kumene ndimakhala. Ndinapita ku Betelehemu mʼdziko la Yuda ndipo tsopano ndikubwerera kwathu. Koma palibe aliyense amene wanditengera ku nyumba yake.
19 其實我有糧草可以餵驢,我與我的妾,並我的僕人,有餅有酒,並不缺少甚麼。」
Tili ndi udzu ndi chakudya cha abulu athu. Tilinso ndi buledi ndi vinyo wokwanira ifeyo: ine, mdzakazi wanuyu, ndi mtumiki amene ali nafeyu. Palibe chimene tikusowa.”
20 老年人說:「願你平安!你所需用的我都給你,只是不可在街上過夜。」
Munthu wokalambayo anati, “Mtendere ukhale nanu. Ine ndikuthandizani pa zosowa zanu zonse, koma musagone pabwalo usiku uno.”
Choncho anapita nawo ku nyumba yake, ndipo anawapatsa abulu ake chakudya. Alendo aja anasamba mapazi awo, nalandira chakudya ndi chakumwa.
22 他們心裏正歡暢的時候,城中的匪徒圍住房子,連連叩門,對房主老人說:「你把那進你家的人帶出來,我們要與他交合。」
Pamene ankadya mosangalala, anangoona anthu ena achabechabe a mu mzindawo azungulira nyumba ija nʼkumamenya chitseko. Tsono anawuza mwini nyumbayo, munthu wokalamba uja kuti, “Mutulutse munthu amene wabwera mʼnyumba yakoyu kuti tigone naye.”
23 那房主出來對他們說:「弟兄們哪,不要這樣作惡;這人既然進了我的家,你們就不要行這醜事。
Koma mwini nyumba uja anatuluka ku bwalo nawawuza kuti, “Ayi, abale anga musachite zoyipa zotere. Popeza munthu uyu walowa mʼnyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere.
24 我有個女兒,還是處女,並有這人的妾,我將她們領出來任憑你們玷辱她們,只是向這人不可行這樣的醜事。」
Onani, pano pali mwana wanga wamkazi wosadziwa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsirani amenewa tsopano ndipo atengeni ndi kuchita nawo chomwe chikukomerani. Koma musachite chinthu chonyansa ndi munthuyu.”
25 那些人卻不聽從他的話。那人就把他的妾拉出去交給他們,他們便與她交合,終夜凌辱她,直到天色快亮才放她去。
Koma anthuwo sanafune kumumvera. Choncho mlendo uja anagwira mzikazi wake namutulutsa kuja kumene kunali iwo. Tsono iwowo anagona naye ndi kuchita naye zonyansa usiku wonse mpaka mmawa. Mʼbandakucha anamulola kuti apite.
26 天快亮的時候,婦人回到她主人住宿的房門前,就仆倒在地,直到天亮。
Ndipo mmawa kukucha mzikazi uja anabwerera nakagwa pansi pa khomo pa nyumba imene mwamuna wake anali, ndipo anakhala pomwepo mpaka kunayera.
27 早晨,她的主人起來開了房門,出去要行路,不料那婦人仆倒在房門前,兩手搭在門檻上;
Mwamuna wake anadzuka mʼmamawa, natsekula chitseko cha nyumba kuti atuluke ndi kumapita. Koma anangoona mzikazi wake uja ali thapsa pa khomo la nyumbayo, manja ake ali pa khonde.
28 就對婦人說:「起來,我們走吧!」婦人卻不回答。那人便將她馱在驢上,起身回本處去了。
Iye anati kwa mkaziyo, “Dzuka tizipita.” Koma sanayankhe kanthu. Kenaka anamukweza pa bulu wake ndipo ananyamuka kumapita kwawo.
29 到了家裏,用刀將妾的屍身切成十二塊,使人拿着傳送以色列的四境。
Atafika ku nyumba yake, anatenga mpeni, nagwira mzikazi wake uja ndi kuduladula thupi lake nthuli khumi ndi ziwiri. Kenaka anazitumiza ku zigawo zonse za Israeli.
30 凡看見的人都說:「從以色列人出埃及地,直到今日,這樣的事沒有行過,也沒有見過。現在應當思想,大家商議當怎樣辦理。」
Aliyense amene anaona zimenezi ankanena kuti, “Zoterezi sizinaonekepo kuyambira pamene Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ganizirani bwino chinthu chimenechi ndipo tiwuzeni zoyenera kuchita!”